Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mukutsatira Malangizo Achikondi a Yehova?

Kodi Mukutsatira Malangizo Achikondi a Yehova?

Kodi Mukutsatira Malangizo Achikondi a Yehova?

“Ndimadana ndi njira iliyonse yachinyengo.”​—SAL. 119:128.

1, 2. (a) Ngati mukufunsa njira yopita kwinakwake, kodi mungayamikire chenjezo lotani ndipo n’chifukwa chiyani? (b) Kodi Yehova amapereka machenjezo otani kwa atumiki ake ndipo n’chifukwa chiyani?

TIYEREKEZE kuti muli pa ulendo ndipo mukupita kumalo achilendo amene simunapiteko. Ndiyeno mukufunsa mnzanu wina wodalirika yemwe akudziwa bwino njira yake. Pokuuzani mmene mungayendere mnzanuyo akunena kuti, “Koma samalani chifukwa kutsogoloko kuli chikwangwani chimene chimasocheretsa anthu ambiri.” Kodi simungayamikire chenjezo limeneli n’kulitsatira? Yehova ali ngati mnzathu wotereyu. Iye amatipatsa malangizo abwino otithandiza kuti tipeze moyo wosatha komanso amatichenjeza kuti tipewe zinthu zoipa zimene zingatisocheretse.​—Deut. 5:32; Yes. 30:21.

2 M’nkhani ino ndiponso yotsatira tikambirana zinthu zingapo zimene Yehova Mulungu, yemwe ndi Mnzathu, amatichenjeza. Tiyenera kukumbukira kuti Yehova amatichenjeza chifukwa chotidera nkhawa komanso kutikonda. Iye amafuna kuti tipeze moyo wosatha. Zimamupweteka kwambiri akamaona anthu akusochera chifukwa chokopeka ndi zinthu zoipa. (Ezek. 33:11) M’nkhani ino tikambirana zinthu zitatu zimene zingatisocheretse. Chinthu choyamba chimachokera kwa anthu ena, chachiwiri chimachokera kwa ife eni ndipo chachitatu si chinthu chenicheni koma n’choopsa. Tiyenera kuzidziwa bwino zinthu zimenezi ndiponso mmene Atate wathu wakumwamba akutiphunzitsira kuti tizipewe. Wamasalimo wina anauza Yehova kuti: “Ndimadana ndi njira iliyonse yachinyengo.” (Sal. 119:128) Kodi inunso mumadana ndi njira iliyonse yachinyengo? Tiyeni tione zimene tingachite kuti tikhaledi ndi maganizo amenewa komanso kuti tizichita zinthu mogwirizana ndi maganizowo.

‘Musamatsatire Khamu la Anthu’

3. (a) Ngati sitikudziwa njira yoyenera kudutsa, n’chifukwa chiyani zili zoopsa kungotsatira anthu ena? (b) Kodi pa Ekisodo 23:2 pali mfundo yofunika kwambiri iti?

3 Ngati muli pa ulendo wautali ndipo simukudziwa njira yoyenera kudutsa, kodi mungatani? Mwina mungaganize zongolowera njira imene anthu ambiri akudutsa. Komatu izi n’zoopsa kwambiri. Mwina anthuwo akupita kosiyana ndi kumene inu mukupita apo ayi mwina iwonso asochera. Pa nkhani imeneyi, tiyeni tione zimene tikuphunzira pa lamulo limene Aisiraeli akale anapatsidwa. Anthu amene anali oweruza kapena opereka umboni pa milandu anachenjezedwa za kuopsa ‘kotsatira khamu la anthu.’ (Werengani Ekisodo 23:2.) N’zosavuta kwa anthu opanda ungwiro kutengeka ndi zimene anthu ena amafuna kenako n’kuchita zinthu zopanda chilungamo. Koma kodi mfundo yakuti tisamangotsatira khamu la anthu imagwira ntchito pa nkhani za milandu zokha? Ayi.

4, 5. Kodi Yoswa ndi Kalebe anayesedwa bwanji kuti atsatire khamu la anthu, nanga n’chiyani chinawathandiza kuti akane zimenezi?

4 Kunena zoona, nthawi ina iliyonse tikhoza kuyesedwa kuti tichite zinthu ‘mongotsatira khamu la anthu.’ Izi zikhoza kuchitika mwadzidzidzi ndipo zingakhale zovuta kuti tikane. Taganizirani zimene Yoswa ndi Kalebe anakumana nazo. Iwo anali m’gulu la anthu 12 amene anatumidwa kukazonda Dziko Lolonjezedwa. Atabwerera, anthu 10 m’gululi ananena zinthu zoipa ndiponso zokhumudwitsa. Iwo ananena kuti m’dzikoli munali ziphona. Iwo anati ziphonazi zinali mbadwa za Anefili omwe anabadwa pa nthawi imene angelo opanduka anagona ndi akazi padziko lapansi. (Gen. 6:4) Komatu izi sizinali zoona. Anefili onse anaphedwa ndi Chigumula zaka zambirimbiri izi zisanachitike. Koma anthu amene ali ndi chikhulupiriro chochepa amatha kukhulupirira ngakhale mabodza achabechabe. Zinthu zoipa zimene anthu 10 amenewa ananena zinachititsa mantha anthu ambiri moti anasowa nazo mtendere. Pasanapite nthawi yaitali, anthu ambiri anaona kuti si bwino kutsatira malangizo a Yehova akuti akalowe m’dziko limene iye anawalonjeza. Kodi Yoswa ndi Kalebe anatani zinthu zitavuta chonchi?​—Num. 13:25-33.

5 Iwo sanatsatire khamu la anthu. M’malomwake, ananena choonadi ndipo sanasinthe ngakhale kuti anthu ambiri ankadana nazo ndipo ankafuna kuwapha powaponya miyala. Kodi n’chiyani chinawathandiza kukhala olimba mtima? Mosakayikira, chikhulupiriro chawo chinawathandiza. Anthu amene ali ndi chikhulupiriro champhamvu amatha kusiyanitsa pakati pa mabodza a anthu ndi malonjezo amene Yehova Mulungu amapereka. Pa nthawi ina, Yoswa ndi Kalebe ananena mmene ankamvera chifukwa chakuti Yehova sanalepherepo kukwaniritsa malonjezo ake onse. (Werengani Yoswa 14:6, 8; 23:2, 14.) Yoswa ndi Kalebe ankakonda kwambiri Mulungu wawo wokhulupirika. Choncho sanayerekeze n’komwe kuchita zinthu zimene zikanamupweteketsa mtima chifukwa chotsatira khamu la anthu opanda chikhulupiriro. Iwo anali olimba ndipo chimenechi ndi chitsanzo chabwino kwambiri kwa ifeyo masiku ano.​—Num. 14:1-10.

6. Kodi tingayesedwe bwanji kuti titsatire khamu la anthu?

6 Kodi nanunso nthawi zina mumayesedwa kuti mutsatire khamu la anthu? Masiku ano, pali anthu ambirimbiri amene salemekeza Yehova ndipo amanyoza mfundo zake za makhalidwe abwino. Nthawi zambiri, anthu oterewa amalimbikitsa mfundo zawo pa nkhani ya zosangalatsa. Iwo amati palibe vuto lililonse ngati munthu atamasangalala ndi zinthu zachiwerewere, zachiwawa kapena zamizimu zimene zafala kwambiri pa TV, m’mafilimu ndiponso m’masewera a pa kompyuta. (2 Tim. 3:1-5) Kodi mukamasankha zosangalatsa panokha kapena ndi banja lanu mumalola kuti muzitsatira chikumbumtima cha anthu otayirira? Kodi zimenezi sizingatanthauze kuti mwayamba kutsatira khamu la anthu?

7, 8. (a) Kodi tingaphunzitse bwanji ‘mphamvu zathu za kuzindikira’ ndipo n’chifukwa chiyani zimenezi zili zothandiza kwambiri kuposa kungouzidwa zochita nthawi zonse? (b) N’chifukwa chiyani munganene kuti zochita za Akhristu achinyamata ambiri n’zolimbikitsa?

7 Yehova watipatsa ‘mphamvu za kuzindikira’ ndipo mphatso yamtengo wapatali imeneyi ikhoza kutithandiza kuti tizisankha zinthu mwanzeru. Komabe mphamvu zimenezi tiyenera kuziphunzitsa ‘pozigwiritsa ntchito.’ (Aheb. 5:14) Ngati timangotsatira zimene anthu ena akuchita kapena ngati timangouzidwa chochita pa nkhani zimene munthu ayenera kusankha yekha, ndiye kuti sitikuphunzitsa mphamvu zathu za kuzindikira. N’chifukwa chake anthu a Yehova sapatsidwa mndandanda wa mafilimu, mabuku kapena malo a pa Intaneti ofunika kuwapewa. Atati apatsidwe mndandandawu ukhoza kukhala wopanda ntchito chifukwa chakuti dzikoli likusintha nthawi zonse. (1 Akor. 7:31) Komanso vuto lalikulu ndi loti titapatsidwa mndandanda wotere, sitingakhale ndi mwayi wosankha tokha zochita pambuyo poona bwinobwino mfundo za m’Baibulo ndiponso kupemphera.​—Aef. 5:10.

8 N’zoona kuti nthawi zina kutsatira mfundo za m’Baibulo kungapangitse anthu ena kudana nafe. Akhristu achinyamata amene ali pa sukulu angayesedwe kuti azionera kapena kuchita zinthu zimene anzawo onse akuonera kapena kuchita. (1 Pet. 4:4) Zimakhala zosangalatsa kuona Akhristu achinyamata ndi achikulire omwe akutsanzira chikhulupiriro cha Yoswa ndi Kalebe amene anakana kutsatira khamu la anthu.

Musamatsatire “Zilakolako za Mitima Yanu ndi Maso Anu”

9. (a) Ngati tikupita kwinakwake, n’chifukwa chiyani si bwino kungolowera njira iliyonse imene yatisangalatsa? (b) N’chifukwa chiyani lamulo la pa Numeri 15:37-39 linali lofunika kwambiri kwa anthu a Mulungu akale?

9 Chinthu chachiwiri chimene chingatisocheretse chimachokera kwa ife eni. Tayerekezerani kuti mukupita kumalo amene simunapiteko. Kodi mungasiye kutsatira mapu n’kungolowera njira iliyonse imene yakusangalatsani? Ngati mutachita zimenezi, simungafike kumene mukupita. Pa mfundo imeneyi, taganizirani lamulo lina limene Yehova anapatsa Aisiraeli akale. Anthu ambiri masiku ano sangamvetse lamulo lakuti Aisiraeli ankayenera kusokerera mphonje ndiponso chingwe cha buluu pa zovala zawo. (Werengani Numeri 15:37-39.) Koma kodi mukudziwa kufunika kwake? Kutsatira lamulo limeneli kunathandiza kuti anthu a Mulungu akhale osiyana kwambiri ndi mitundu ina yosalambira Mulungu imene inawazungulira. Izi zinali zofunika kwambiri kuti akhalebe pa ubwenzi wabwino ndi Yehova. (Lev. 18:24, 25) Komabe lamulo limeneli likutithandizanso kudziwa chinthu china chochokera kwa ife eni chimene chingatilepheretse kupeza moyo wosatha. Kodi likutithandiza bwanji?

10. Kodi Yehova anasonyeza bwanji kuti amadziwa mmene anthu alili?

10 Pofotokoza chifukwa chimene anaperekera lamuloli, Yehova anati: “Muleke kutsatira zilakolako za mitima yanu ndi maso anu, chifukwa potsatira zilakolako zimenezo, mukuchita chiwerewere.” Mawu akuti mtima amatanthauza munthu wathu wamkati. Yehova amadziwa bwino kwambiri mmene anthu alili. Iye amadziwa kuti mitima yathu sichedwa kutengeka ndi zinthu zimene timaona. N’chifukwa chake Baibulo limatichenjeza kuti: “Mtima ndi wonyenga kwambiri kuposa china chilichonse ndipo ungathe kuchita china chilichonse choipa. Ndani angaudziwe?” (Yer. 17:9) Kodi mwaona tsopano chifukwa chimene Yehova anachenjezera Aisiraeli? Iye ankadziwa kuti iwo akhoza kutengeka ndi zimene anaona kwa anthu osalambira Mulungu amene anawazungulira. Iwo akanafuna kuti azioneka ngati anthu osakhulupirirawo kenako n’kuyamba kuganiza ndiponso kuchita zinthu ngati iwowo.​—Miy. 13:20.

11. Kodi tingakopedwe bwanji ndi zimene maso athu amaona?

11 Masiku ano, n’zosavuta kwambiri kuti mtima wathu wonyenga ukopedwe ndi zimene maso athu amaona. Dziko limene tikukhalali limachititsa kuti tizikopeka mosavuta ndi zinthu zoipa. Ndiyeno kodi tingatsatire bwanji mfundo ya pa Numeri 15:39? Mwachitsanzo, ngati anthu a kusukulu, kuntchito kapena kudera lanu amavala zovala zimene zingachititse ena kukhala ndi maganizo oipa, kodi mungakopeke nazo? Kodi mungayambe “kutsatira zilakolako za mitima yanu ndi maso anu” n’kutengera zimene mumaona? Kodi mungasiye kutsatira mfundo zimene mumayendera n’kuyamba kuvala ngati iwowo?​—Aroma 12:1, 2.

12, 13. (a) Kodi tiyenera kutani ngati timakonda kuona zinthu zosayenera? (b) N’chiyani chingatithandize kuti tisachititse ena kukopeka ndi zoipa?

12 Tiyenera kuyesetsa kwambiri kuti tikhale odziletsa. Ngati timakonda kuona zinthu zosayenera, tiyeni tikumbukire zimene Yobu anachita. Iye anapangana ndi maso ake kuti asayang’ane mkazi wina momusirira. Izi zikutanthauza kuti anatsimikiza mumtima mwake kuti asasirire akazi ena. (Yobu 31:1) Nayenso Mfumu Davide anatsimikiza mumtima mwake kuti: “Sindidzaika maso anga pa chinthu chilichonse chopanda pake.” (Sal. 101:3) Chinthu chilichonse chimene chingawononge chikumbumtima chathu choyera kapena ubwenzi wathu ndi Yehova ndi “chopanda pake.” Izi zikuphatikizapo chilichonse chimene chingachititse maso ndi mtima wathu kukopeka kuti tichite zinthu zoipa.

13 Komanso sitiyenera kuchititsa anthu ena kuti ayambe kukopeka ndi zinthu zoipa chifukwa tikatero ifeyo tingakhale ngati ‘chinthu chopanda pake.’ Choncho timatsatira malangizo ouziridwa a m’Baibulo akuti tizivala zovala zoyenera ndiponso zaulemu. (1 Tim. 2:9) Kuvala mwaulemu sikutanthauza kungovala zimene ifeyo tikuona kuti ndi zaulemu. Tiyenera kuganizira chikumbumtima cha anthu amene tingakumane nawo n’kumapewa kuvala zinthu zimene zingawakhumudwitse. (Aroma 15:1, 2) Mu mpingo wachikhristu muli achinyamata ambirimbiri amene amapereka chitsanzo chabwino pa nkhani ya kavalidwe. Timawanyadira kwambiri chifukwa chakuti amakana ‘kutsatira zilakolako za mitima yawo ndi maso awo’ ndipo amasangalatsa Yehova ngakhale pa nkhani ya kavalidwe.

Musamatsatire Zopanda Pake

14. Kodi Samueli anapereka chenjezo lotani pa nkhani ya kutsatira zinthu zopanda pake kapena kuti zimene si zenizeni?

14 Tayerekezani kuti ulendo umene mukuyenda uja ndi wodutsa m’chipululu chachikulu komanso chotentha kwambiri. N’chiyani chingachitike ngati mutasiya msewu kuti mutsatire chizimezime poganiza kuti ndi madzi? Zimenezi zikhoza kuika moyo wanu pa ngozi. Yehova amadziwa kuopsa kokhulupirira zinthu zoti si zenizeni. Taganizirani chitsanzo ichi. Aisiraeli anafuna kukhala ngati mitundu yowazungulira imene inkalamuliridwa ndi anthu. Kufuna kuti munthu awalamulire kunali tchimo lalikulu chifukwa kunali ngati kukana kulamuliridwa ndi Yehova. Ngakhale kuti Yehova anawalola kukhala ndi mfumu, iye anauza Samueli kuti awachenjeze mosapita m’mbali kuopsa kotsatira “milungu yopanda pake,” kapena kuti zinthu zimene si zenizeni.​—Werengani 1 Samueli 12:21.

15. Kodi Aisiraeli anatsatira bwanji zinthu zopanda pake?

15 Kodi Aisiraeli ankaganiza kuti munthu akhoza kukhala mfumu yeniyeni ndiponso yodalirika kuposa Yehova? Ngati ndi choncho, ndiye kuti anali kutsatira zinthu zopanda pake. Iwo anali pa ngozi yotsatira zinthu zinanso zopanda pake zochokera kwa Satana. Zikanakhala zosavuta kuti mafumu otere awachititse kulambira mafano. Anthu olambira mafano amaganiza kuti milungu yopangidwa kuchokera ku mitengo kapena miyala imakhala yeniyeni ndiponso yodalirika kuposa Yehova Mulungu wosaoneka amene analenga zinthu zonse. Koma malinga ndi zimene mtumwi Paulo ananena, mafano ndi ‘opanda pake.’ (1 Akor. 8:4) Sangaone, kumva, kulankhula kapena kuchita chilichonse. N’zotheka kuti muone ndiponso kukhudza mafanowo koma mukawalambira ndiye kuti mukutsatira chinthu chopanda pake, kapena kuti chinthu chimene si chenicheni, chomwe chingakuchititseni kukumana ndi zoopsa zokhazokha.​—Sal. 115:4-8.

16. (a) Kodi Satana amakopa bwanji anthu ambiri masiku ano kuti atsatire zinthu zopanda pake? (b) N’chifukwa chiyani tinganene kuti zinthu zakuthupi ndi zopanda pake tikaziyerekeza ndi Yehova Mulungu?

16 Masiku anonso Satana ali ndi luso lokopa anthu kuti atsatire zinthu zopanda pake. Mwachitsanzo, iye wakopa anthu ambiri kuti azifunafuna chuma poganiza kuti chiwathandiza kukhala ndi moyo wabwino. Ndalama, katundu ndiponso ntchito zapamwamba zingaoneke zothandiza. Koma kodi zinthu zimenezi zingathandizedi pamene munthu wadwala, pamene chuma cha dziko chasokonekera kwambiri kapena pamene tsoka lachilengedwe lachitika? Kodi zinthu zimenezi zingathandize munthu kukhala ndi cholinga chenicheni pa moyo ndiponso kupeza mayankho a mafunso amene amamuvutitsa? Nanga zingateteze munthu kuti asamwalire? Tikamaganiza kuti zinthu zakuthupi zitithandiza pa zosowa zathu zauzimu tidzagwiritsidwa mwala. Zinthu zakuthupi sizithandiza kwenikweni chifukwa ndi zopanda pake. Sizingatiteteze ngakhale mwakuthupi chifukwa sizingatalikitse kwenikweni moyo wathu kapena kuthetsa matenda ndi imfa. (Miy. 23:4, 5) Yehova Mulungu yekha ndi amene ali weniweni. Kukhala pa ubwenzi wolimba ndi iye n’kumene kungatithandize kukhala ndi moyo wabwino kwambiri. Uwutu ndi mwayi wamtengo wapatali kwambiri. Tiyeni tisayerekeze n’komwe kusiya Yehova n’kutsatira zinthu zopanda pake.

17. Popeza kuti takambirana zinthu zitatu zimene zingatisocheretse, kodi inu mwatsimikiza kuchita chiyani?

17 Tili ndi mwayi waukulu kwambiri chifukwa chakuti Yehova ndi Mnzathu ndipo akutitsogolera pa moyo. Tikamamvera chenjezo lake pa nkhani yopewa kutsatira khamu la anthu, kutsatira mitima yathu ndiponso zinthu zopanda pake, tikhoza kudzalandira moyo wosatha. M’nkhani yotsatira tidzakambirana machenjezo enanso atatu amene Yehova wapereka n’cholinga chotithandiza kupewa ndiponso kudana ndi njira zachinyengo zimene zikusocheretsa anthu ambiri.​—Sal. 119:128.

Kodi Mukuganiza Bwanji?

Kodi mungagwiritse ntchito bwanji mfundo zimene mwaphunzira m’malemba amene ali m’munsiwa?

Ekisodo 23:2

Numeri 15:37-39

1 Samueli 12:21

Salimo 119:128

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 11]

Kodi nthawi zina mumayesedwa kuti mutsatire khamu la anthu?

[Chithunzi patsamba 13]

N’chifukwa chiyani kungotsatira mtima wanu n’koopsa?

[Chithunzi patsamba 14]

Kodi mukutsatira zinthu zopanda pake?