Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Padziko Lonse Anthu Akugwirizana—Kodi Zikutheka Bwanji?

Padziko Lonse Anthu Akugwirizana—Kodi Zikutheka Bwanji?

Padziko Lonse Anthu Akugwirizana​—Kodi Zikutheka Bwanji?

KODI mawu akuti “kugwirizana” amatanthauza chiyani? Kwa ena mawuwa amangotanthauza kusayambana kapena kusakangana basi. Mwachitsanzo, ngati mayiko awiri kapena angapo asayinirana pangano la mtendere, amati pakati pawo pali mgwirizano. Koma kodi zimenezi n’zoona? Osati kwenikweni.

Taganizirani izi: Kuyambira kalekale, mayiko akhala akuswa mapangano osiyanasiyana a mtendere amene akhala akupanga. N’chifukwa chiyani? Nthawi zambiri n’chifukwa choti atsogoleri a mayiko padziko lonse amaganizira kwambiri za mphamvu zimene ayenera kukhala nazo osati za mtendere kapena kugwirizana. Palinso mayiko ena amene amaopa kwambiri zimene zingachitike ngati atayamba kutsalira pankhani ya zida zankhondo.

Motero sikuti mayiko akakhala kuti sakumenyana ndiye kuti ali pamtendere. Kodi ngati mutaona anthu awiri ataimitsana mwandewu, zikwanje zili m’manja, munganene kuti ali pamtendere chifukwa choti sanayambe kukhapana? Ayi, munthu wanzeru sangaganize choncho. Komatu umu ndi mmene zinthu zilili pakati pa mayiko ambiri masiku ano. Chifukwa chokayikirana kwambiri mayikowa amaopana poganiza kuti tsiku lina adzaukirana. Kodi n’chiyani chimene mayikowa achita pofuna kupewa zoopsa zoterezi?

Kuopa Zida za Nyukiliya Kukulepheretsa Kugwirizana

Anthu ambiri amalimba mtima poganizira za pangano limene mayiko anapanga (lotchedwa Nuclear Non-Proliferation Treaty [NPT]) loletsa mayiko amene alibe zida za nyukiliya kuyamba kupanga zidazi. Mayiko anavomereza panganoli mu 1968 ndipo limaletsanso mayiko amene ali nazo kale kuti asazifalitse. Cholinga cha panganoli, lomwe tsopano lavomerezedwa ndi mayiko oposa 180, n’chakuti m’kupita kwa nthawi mayiko onse adzatule pansi zida zawo za nyukiliya.

Ichi ndi cholinga chabwino ndithu, koma pali anthu ena amene akuona kuti cholinga cha pangano limeneli n’chongofuna kupondereza mayiko enaake kuti asakhale nawo m’gulu la mayiko okhala ndi zida za nyukiliya. Motero akuti n’zotheka kuti mayiko ena amene anasayina nawo panganoli asinthe maganizo m’tsogolo. Ndipotu pali mayiko ena amene amaona kuti sichilungamo kuti iwowo aziletsedwa kupanga zida zimene angathe kudziteteza nazo.

Pavutiranso nkhani m’pakuti palibe dziko limene limaletsedwa kugwiritsira ntchito zinthu zopangira zida za nyukiliyazi kupangira zinthu zina monga magetsi. Moti anthu ena akuda nkhawa kuti n’kutheka kuti mayiko ena akungonama kuti akugwiritsira ntchito zinthuzi popangira magetsi pamene kwenikweni akupangira zida za nyukiliya.

Ngakhale mayiko amene ali nazo kale zida za nyukiliya angathe kuswa pangano limene anapangana lija. Akatswiri ena amanena kuti palibe munthu wozindikira amene angakhulupirire kuti mayiko amene panopo ali ndi zida zambiri angaziphwasule kapena kuzichepetsa kumene. Buku lina linati: “Kuti achite zimenezi . . . mayiko amene ali paudani ayenera kukhala paubale ndi kuyamba kukhulupirirana kwambiri [zomwe n’zovuta kukhulupirira] kuti zingachitike.”

Anthu alephera kubweretsa mgwirizano, ngakhale kuti nthawi zina ayesetsa kuchita zimenezi moona mtima kwambiri. Izitu sizodabwitsa kwa anthu amene amawerenga Baibulo, chifukwa Mawu a Mulungu amati: “Sikuli kwa munthu woyenda kulongosola mapazi ake.” (Yeremiya 10:23) Baibulo limanenanso mosapita m’mbali kuti: “Ilipo njira yooneka kwa mwamuna ngati yowongoka, koma matsiriziro ake ndi njira za imfa.” (Miyambo 16:25) Maboma a anthu sangabweretse mgwirizano weniweni. Komabe tisataye mtima ayi.

Njira Imene Idzabweretse Mgwirizano Weniweni

M’Baibulo muli lonjezo la Mulungu lakuti anthu padziko lonse adzakhala ogwirizana koma osati chifukwa cha nzeru za anthu. Mlengi, yemwe analonjeza kuti anthu adzakhala mumtendere padziko lonse, ndiye adzachite zimene anthu sangathe kuchitazi. Kwa ena zonsezi zingaoneke ngati nkhambakamwa chabe. Komatu pachiyambi pomwe, Mulungu anakonza zoti anthu azikhala mwamtendere ndiponso mogwirizana. * M’Baibulo muli malemba ambiri amene amachitira umboni mfundo yakuti cholinga cha Mulungu choti anthu onse akhale ogwirizana sichinasinthe ayi. Taonani ena mwa malemba amenewa.

• “Idzani, penyani ntchito za Yehova, amene achita zopululutsa pa dziko lapansi. Aletsa nkhondo ku malekezero a dziko lapansi; athyola uta, nadula nthungo; atentha magareta ndi moto.”​—SALMO 46:​8, 9.

• “Sizidzaipitsa, sizidzasakaza m’phiri langa lonse loyera, chifukwa kuti dziko lapansi lidzadzala ndi odziwa Yehova, monga madzi adzaza nyanja.”​—YESAYA 11:9.

• “Iye wameza imfa ku nthawi yonse; ndipo Ambuye Mulungu adzapukuta misozi pa nkhope zonse; ndipo chitonzo cha anthu ake adzachichotsa pa dziko lonse lapansi; chifukwa Yehova wanena.”​—YESAYA 25:8.

• “Pali miyamba yatsopano ndi dziko lapansi latsopano zimene ife tikuyembekeza malinga ndi lonjezo lake, ndipo mmenemo mudzakhala chilungamo.”​—2 PETULO 3:13.

• “[Mulungu] adzapukuta msozi uliwonse m’maso mwawo, ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kapena kubuula, ngakhale kupweteka. Zakalezo zapita.”​—CHIVUMBULUTSO 21:4

Amenewa ndi malonjezo osakayikitsa ngakhale pang’ono. N’chifukwa chiyani? N’chifukwa choti Yehova Mulungu ndi Mlengi, ndipo ali ndi mphamvu zotha kugwirizanitsa anthu onse. (Luka 18:27) Komanso Iye akufunitsitsa kwambiri kuchita zimenezi. Ndipotu Baibulo limanena kuti zimenezi ndi zinthu “zokomera [Mulungu] . . . kusonkhanitsanso zinthu zonse pamodzi mwa Khristu, zinthu za kumwamba ndi zinthu za padziko lapansi.”​—Aefeso 1:​8-10.

Zimene Mulungu walonjeza zobweretsa “dziko lapansi latsopano” limene “mudzakhala chilungamo” si zongolakalaka chabe ayi. (2 Petulo 3:13) Ponena za malonjezo ake, Yehova Mulungu anati: “Sadzabwerera kwa Ine chabe, koma adzachita chimene ndifuna, ndipo adzakula mmene ndinawatumizira.”​—Yesaya 55:11.

Kugwirizana Chifukwa cha Mawu a Mulungu

Monga tanenera m’nkhani yapitayi, zipembedzo zakhala zikugawanitsa anthu m’malo mowagwirizanitsa. Nkhani imeneyi ndi yofunika kuiganizira, chifukwa choti ngati timavomereza zoti kuli Mlengi, tiyenera kudzifunsa kuti, kodi sipomveka kuyembekezera kuti anthu olambira Mlengiyu azikhala mwamtendere ndiponso mogwirizana? Inde m’pomveka.

Khalidwe logawanitsa anthu lopezeka m’zipembedzo silisonyeza maganizo a Yehova Mulungu kapena opezeka m’Mawu ake. M’malomwake limaonetsa poyera chinyengo cha zipembedzo zimene zimalimbikitsa njira za anthu zokhazikitsira mtendere m’malo molimbikitsa cholinga cha Mulungu. Yesu anatcha atsogoleri achipembedzo a m’nthawi yake kuti “onyenga” ndipo anawauza kuti: “Yesaya ananenera moyenera za inu, muja anati, ‘Anthu awa amandilemekeza ndi milomo yokha, koma mtima wawo uli kutali ndi ine. Amandilambira ine pachabe, chifukwa amaphunzitsa malamulo a anthu monga ziphunzitso za Mulungu.’”​—Mateyo 15:​7-9.

Mosiyana ndi zimenezi, chipembedzo choona chimagwirizanitsa anthu. Mneneri Yesaya analosera kuti: “Padzakhala masiku otsiriza, kuti phiri la nyumba ya Yehova lidzakhazikika pa nsonga ya mapiri, ndipo lidzakwezedwa pamwamba pa zitunda; mitundu yonse idzasonkhana kumeneko. Iye adzaweruza pakati pa akunja, adzadzudzula mitundu yambiri ya anthu; ndipo iwo adzasula malupanga awo akhale zolimira, ndi nthungo zawo zikhale anangwape; mtundu sudzanyamula lupanga kumenyana ndi mtundu wina, ndipo sadzaphunziranso nkhondo.”​—Yesaya 2:​2, 4.

Monga ulosiwu unanenera, masiku ano Mboni za Yehova m’mayiko oposa 230 zikutsatira malangizo amene Yehova Mulungu anapereka pankhani ya mgwirizano. Kodi maziko a kugwirizana kwawoku n’chiyani? Mtumwi Paulo analemba kuti: “Valani chikondi, pakuti ndicho chomangira umodzi changwiro.” (Akolose 3:14) Mawu oyambirira amene Paulo anagwiritsa ntchito potanthauza kuti “chomangira” angatanthauze mitsempha imene imagwirizanitsa mafupa pamodzi m’thupi la munthu. Mitsemphayi imakhala yolimba ngati chingwe, ndipo imathandizanso kugwira pamodzi ziwalo za m’thupi.

N’chimodzimodzinso ndi chikondi. Khalidwe limeneli sikuti limangoletsa anthu kuti asamaphane ayi. Chikondi changati cha Khristu chimachititsa kuti anthu osiyana m’njira zambiri azitha kukhala bwinobwino mwamtendere. Mwachitsanzo, chimachititsa kuti anthu azikhala mogwirizana ndi lamulo lotchuka limene Yesu Khristu anapereka pa Mateyo 7:​12, lakuti: “Zinthu zonse zimene mukufuna kuti anthu akuchitireni, inunso muwachitire zimenezo.” Kutsatira mfundo imeneyi kwathandiza anthu ambiri kuthetsa tsankho.

‘Kukondana’

A Mboni za Yehova amayesetsa kwambiri kuchita zinthu mosonyeza kuti ndi ophunzira a Khristu. Iwo amatero potsatira zimene Yesu Khristu ananena zakuti: “Mwa ichi onse adzadziwa kuti ndinu ophunzira anga, ngati mukondana wina ndi mnzake.” (Yohane 13:35) Mboni za Yehova zaonetsa mwapadera chikondi chimenechi m’madera amene pakhala kusamvana chifukwa chosankhana mitundu ndiponso chifukwa cha nkhani za ndale. Mwachitsanzo, mu 1994 pomwe a Hutu ankamenyana ndi a Tutsi ku Rwanda, Mboni za Yehova zinasonyezana chikondi. Mboni zachihutu zinaika miyoyo yawo pachiswe pofuna kuteteza abale awo omwe anali a Tutsi.

Komabe, si zomveka kuganiza kuti mitundu ya padzikoli idzayamba kukondana n’kufika poti dziko lonse lidzakhale logwirizana. Baibulo limati Mulungu ndi amene adzakwanitse kuchita zimenezi panthawi yake. Koma ngakhale panopo, anthu angathe kuyamba kukulitsa chikondi chawo n’kukhala ogwirizana.

Chaka chathachi, Mboni za Yehova zinathera maola oposa 1 biliyoni poyendera anthu ndi kuwauza za Baibulo komanso za kufunika kwake pa moyo masiku ano. Kudziwa Mawu a Mulungu molondola kwagwirizanitsa anthu mamiliyoni ambiri, ndipo ena mwa iwo ankadana kwambiri m’mbuyomo. Ena mwa anthu otere ndi Aluya ndi Ayuda, Alumeniya ndi Ataki, Ajeremani ndi Arasha, ndi enanso otere.

Kodi mungakonde kudziwa zambiri za mmene Mawu a Mulungu, Baibulo, amagwirizanitsira anthu? Ngati mungakonde kutero, pezani Mboni za Yehova kwanuko, kapena lembani kalata ku adiresi yoyenera pa maadiresi amene ali pa tsamba 2.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 12 Kuti mudziwe zambiri zokhudza cholinga cha Mulungu polenga anthu, onani mutu 3 wa buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lofalisidwa ndi Mboni za Yehova.

[Mawu Otsindika patsamba 4]

Mayiko akhala akuswa mapangano osiyanasiyana a mtendere

[Mawu Otsindika patsamba 7]

Kutsatira mfundo za m’Baibulo kwasintha anthu m’njira imene maboma a anthu sangakwanitse.

[Chithunzi patsamba 5]

Mawu a Mulungu amasonyeza njira imene idzabweretse mgwirizano weniweni

[Chithunzi patsamba 7]

Mboni za Yehova za chihutu ndi chitutsi zikumangira limodzi malo olambirira