Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Phunzitsani Ana Anu Kukonda Mtendere

Phunzitsani Ana Anu Kukonda Mtendere

 Phunzitsani Ana Anu Kukonda Mtendere

Posangalala kuti banja lawo lonse lipita kukaona malo enaake akutali, Nicole, yemwe anali ndi zaka 8, ankakonda kuuza mnzake Gabrielle, nkhani zokhudza ulendowo. Koma tsiku lina Gabrielle anauza Nicole kuti watopa nazo nkhani za ulendo wakewo. Nicole atakhumudwa kwambiri anauza mayi ake kuti: “Amene uja sindikufuna kudzamuonanso!”

NTHAWI zambiri ana akayambana ngati mmene anachitira Nicole ndi Grabrielle, pamafunika kuti makolo alowererepo n’kukhazikitsa mtendere komanso kuwaphunzitsa anawo njira yoyendetsera bwino nkhani zotere. Mwana ndi mwana basi, ndipo kawirikawiri sazindikira kuti mawu ndiponso zochita zake zingathe kukhumudwitsa ena. (1 Akorinto 13:11) Choncho, ana amafunika kuwaphunzitsa makhalidwe amene angachititse kuti azikhala mwamtendere ndi anzawo komanso abale awo.

Makolo achikhristu ndi ofunitsitsa kuphunzitsa ana awo “kupeza mtendere ndi kuusunga.” (1 Petulo 3:11) Kukhala munthu wamtendere kumabweretsa chimwemwe chosaneneka moti m’pake kuchita khama mmene mungathere kuti muphunzitse ana anu kuthetsa maganizo okayikira ena ndiponso, okonda kukwiya. Choncho, mungawaphunzitse bwanji kukhala amtendere?

Aphunzitseni Mtima Wofuna Kusangalatsa “Mulungu wa Mtendere”

Yehova amatchedwa “Mulungu wa mtendere” ndipo Baibulo limatinso iyeyu ndiye “amapatsa mtendere.” (Afilipi 4:9; Aroma 15:33) Motero, makolo anzeru amagwiritsa ntchito mwaluso Baibulo lomwe ndi Mawu a Mulungu, kulimbikitsa ana awo kukhala ndi mtima wofuna kusangalatsa Mulungu ndi kutsanzira makhalidwe ake. Mwachitsanzo, thandizani ana anu kupanga chithunzithunzi m’maganizo mwawo cha zimene mtumwi Yohane anaona m’masomphenya. Iye anaona utawaleza wooneka ngati mwala wa emarodi utazungulira mpando wachifumu wa Yehova. * (Chivumbulutso 4:​2, 3) Afotokozereni kuti utawaleza umenewu umatanthauza mtendere ndi bata zimene  zili ku mpando wa Yehova ndipo muwafotokozerenso kuti anthu onse amene amamvera Yehova adzakhala mwamtendere ndi bata.

Yehova amatitsogoleranso kudzera mwa Mwana wake Yesu, yemwe amatchedwa “Kalonga wa mtendere.” (Yesaya 9:​6, 7) Motero, ana anuwo muwawerengere ndi kukambirana nawo nkhani za m’Baibulo zimene Yesu anaphunzitsamo anthu mfundo zothandiza mmene angapewere mikangano ndi ndewu. (Mateyo 26:​51-56; Maliko 9:​33-35) Afotokozereni chifukwa chimene Paulo, yemwe poyamba anali munthu “wachipongwe,” anasinthira n’kufika polemba kuti “kapolo wa Ambuye sayenera kukangana ndi anthu, koma ayenera kukhala wodekha kwa onse, . . . wougwira mtima pokumana ndi zoipa.” (1 Timoteyo 1:13; 2 Timoteyo 2:24) Mungadabwe kwambiri kuona mmene ana anu angasinthire.

Evan amakumbukira kuti ali ndi zaka 7, panali mnyamata wina amene ankakonda kumuvutitsa akakwera basi yopita kusukulu kwawo. Iye anati: “Zinkandiwawa kwambiri moti ndinkafuna kubwezera. Koma kenaka ndinakumbukira zimene ndinaphunzira kunyumba zokhudza anthu amene amakonda zandewu. Ndinadziwa kuti Yehova amafuna kuti ‘ndisabwezere choipa pa choipa’ ndiponso kuti ‘ndizikhala mwamtendere ndi anthu onse.’” (Aroma 12:​17, 18) Zimenezi zinam’thandiza Evan kuti alimbe mtima n’kuthetsa nkhaniyi poyankha modekha. Iye ankafuna kusangalatsa Mulungu wamtendere.

Makolonu Muzikhala Amtendere

Kodi pakhomo panu pali mtendere? Ngati ndi choncho, ana anu angaphunzire zambiri pankhani ya mtendere ngakhale popanda kuwauza mawu aliwonse. Sizingavute kuphunzitsa ana anu kukhala amtendere ngati mumatsanzira kwambiri njira zamtendere za Mulungu ndi Khristu.​—Aroma 2:21.

Russ ndi Cindy amayesetsa kuphunzitsa ana awo awiri aamuna, ndipo amawalimbikitsa kuti azingosonyeza chikondi kwa anthu omwe awaputa. Cindy anati: “Khalidwe limene ineyo ndi Russ timaonetsa ana athu komanso anthu ena pakabuka mavuto, lathandiza kwambiri kuti ana athu aphunzire kuthetsa mavuto otere m’njira yoyenerera.”

Palibe makolo amene salakwitsa, choncho ngakhale mutachita zinazake zolakwika, mungathebe kugwiritsira ntchito mwayi umenewu kuphunzitsa ana anu zinthu zinazake zofunika. Stephen anavomereza kuti: “Nthawi zina, ineyo ndi mkazi wanga Terry tinkalanga ana athu atatu tisanamvetse bwinobwino nkhani yonse. Tikachita zimenezi, tinkawapepesa.” Nayenso Terry anati: “Timadziwitsa ana athuwo kuti nafenso ndife opanda ungwiro ndipo timalakwitsa. Taona kuti zimenezi zachititsa kuti banja lathu likhale lamtendere komanso zathandiza ana athu kuphunzira kukhazikitsa mtendere.”

Kodi ana anu akuphunzira kukhala anthu okonda mtendere poona mmene mumachitira nawo zinthu? Yesu analimbikitsa anthu kuti: “Zinthu zonse zimene mukufuna kuti anthu akuchitireni, inunso muwachitire zimenezo.” (Mateyo 7:12) Ngakhale kuti mungamalakwitse mwina ndi mwina, dziwani kuti chikondi chimene mumasonyeza ana anu chidzabala zipatso zabwino. Ngati mumalangiza ana anu mwachikondi, zidzakhala zosavuta kuti iwo atsatire malangizo anuwo.

 Osafulumira Kukwiya

Lemba la Miyambo 19:11 limati: “Kulingalira kwa munthu kuchedwetsa mkwiyo.” Kodi mungathandize bwanji ana anu kuti azichita zimenezi? David anafotokoza njira imene iyeyo ndi mkazi wake Mariann amagwiritsa ntchito pothandiza mwana wawo wamwamuna ndi wamkazi. Iye anati: “Iwowa akapsa mtima ndi winawake amene wanena kapena kuchita zinazake zopweteketsa mtima, timawathandiza kuti aganizirenso mbali ya munthuyo. Timawafunsa mafunso monga akuti: ‘Kodi n’kutheka kuti munthuyo anali wotopa kwambiri? Kapena mwina akuchita nanu nsanje? Kodi n’kutheka kuti wakhumudwitsana ndi winawake?’” Mariann anatinso: “Mafunso ngati amenewa amathandiza ana athuwo kukhazika mtima pansi, m’malo mokhalabe okwiya kapena kumangolimbikira zoti wolakwa si iwowo pankhaniyo.”

Kuphunzitsa ana zimenezi kungabweretse madalitso osaneneka. Taonani mmene Nicole, amene tam’tchula kumayambiriro kwa nkhani ino anathandizidwira ndi mayi ake, dzina lawo a Michelle. Iwowa anam’thandiza kwambiri, osati kungomugwirizanitsa ndi Gabrielle. Mayiwa akuti: “Tinawerengera limodzi mutu 14 wa m’buku la Phunzirani kwa Mphunzitsi wa Luso. * Kenaka ndinam’fotokozera tanthauzo la zimene Yesu ananena zakuti tizikhululukira anzathu “nthawi 77.” Kenaka anayamba kundiuza mmene iyeyo akumvera ndipo ndinamvetsera mosamala. Ndiyeno ndinamuthandiza kumva mmene Gabrielle anali kumvera podziwa kuti mnzake wapamtima achokapo n’kupita kutali.”​—Mateyo 18:​21, 22.

Nicole atazindikira kuti mwina Gabrielle anakalipa chifukwa cha chisoni, anamumvera chifundo mnzakeyo ndipo anamuimbira telefoni n’kumupepesa. Michelle anati: “Kuyambira nthawi imeneyo mwana wangayu amasangalala kwambiri kuchita zinthu moganizira ena ndi kuwachitira zinthu zabwino kuti azisangalala.”​—Afilipi 2:​3, 4.

Thandizani ana anu kupewa kukhumudwa kwambiri ndi zolakwa za ena kapena kusemphana nawo maganizo. Mukatero mungathe kusangalala kuona ana anu akusonyeza ena chikondi chenicheni n’kumawafuniradi zabwino mochoka pansi pamtima.​—Aroma 12:10; 1 Akorinto 12:25.

Alimbikitseni Kufuna Ulemerero wa Kukhululukira

Lemba la Miyambo 19:11 limanena kuti kukhululukira cholakwa ndi ulemerero. Yesu anatsanzira Atate wake posonyeza mtima wokhululukira panthawi imene anali kumva ululu wosaneneka. (Luka 23:34) Ana anu angathenso kuphunzira ulemerero wa kukhululukira akaona mmene mtima wawo umakhalira pansi inuyo mukawakhululukira.

Mwachitsanzo, mwana wina wazaka zisanu, dzina lake Willy, amakonda masewera opaka utoto pa zithunzi zojambula. Iyeyu amachita zimenezi ndi agogo ake aakazi. Panthawi ina agogo akewo anangosiya masewerawo mwadzidzidzi, n’kumukalipira Willy, basi n’kuchokapo. Willy anakhumudwa nazo kwambiri. Bambo ake, dzina lawo a Sam, anafotokoza kuti: “Agogo a Willy amadwala matenda enaake osokoneza ubongo. Motero, tinam’fotokozera Willy momveka bwino za vuto limeneli.” Sam anadabwa kwambiri ndi zimene Willy anachita atamuuza kuti angowakhululukira agogo akewo chifukwa nayenso wakhululukidwapo nthawi zambiri. Bambo akewo anati: “Tangoganizirani mmene ineyo ndi mkazi wanga tinamvera kuona mwana wathuyu akupita kwa agogo akewo, omwe anali ndi zaka 80, n’kuyamba kuwapepesa, kenaka n’kuwagwira padzanja n’kubwerera nawo patebulo imene amajambulira ija.”

Umakhaladi ulemerero weniweni kuona ana  ataphunzira ‘kulolera’ zofooka ndiponso zolakwa za ena n’kumawakhulukira. (Akolose 3:13) Atsimikizireni ana anuwo kuti ngakhale pamene anthu akuchitira dala zinthu zowapsetsa mtima, kuchita zinthu mwamtendere ndiyo njira yothandiza kwambiri, chifukwa “njira za munthu zikakonda Yehova, ayanjanitsana naye ngakhale adani ake.”​—Miyambo 16:7.

Pitirizani Kuthandiza Ana Anu Kukonda Mtendere

Makolo akamagwiritsira ntchito Mawu a Mulungu kuphunzitsa ana awo “mu mtendere” ndipo ngati “amafesa mu mtendere,” ana awo amadalitsidwa kwambiri. (Yakobe 3:18) Makolo otere amakhala akuphunzitsa ana awo kudziwa njira yabwino yothetsera kusamvana ndiponso kukhala anthu okonda mtendere. Zimenezi zimawathandiza kwambiri anawo kukhala osangalala pamoyo wawo wonse.

Dan ndi Kathy ali ndi ana atatu omwe sanakwanitse zaka 20, ndipo onse akuchita bwino mwauzimu. Dan anati: “Ngakhale kuti zinali zovuta kuwaphunzitsa bwinobwino anawa adakali aang’ono, koma panopo ndife osangalala kwambiri kuti ana akuchita bwino mwauzimu. Panopo amagwirizana ndi anzawo, ndipo akayambana nawo sachedwa kuwakhululukira.” Kathy anati: “Zimenezi zimatilimbikitsa kwambiri, chifukwa choti mtendere ndi mbali ya chipatso cha mzimu wa Mulungu.”​—Agalatiya 5:​22, 23.

Motero, pa zifukwa zabwino, makolo achikhristu ‘saleka’ kapena “kutopa” ndi kuphunzitsa ana awo kukhala anthu amtendere, ngakhale zitamaoneka kuti anawo akuchedwa kuphunzira khalidwe limeneli. Mukamatero, dziwani kuti “Mulungu wachikondi ndi wamtendere adzakhala nanu.”​—Agalatiya 6:9; 2 Akorinto 13:11.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 6 Onani chithunzi cha zimenezi patsamba 75 la buku lakuti Revelation​—Its Grand Climax At Hand! lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

^ ndime 16 Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Bokosi/​Chithunzi patsamba 20]

KODI AMAPHUNZITSA MTENDERE?

Bungwe lina loona zofalitsa nkhani (Media Awareness Network) linati: “Mafilimu ambiri, kapena zinthu zina zotere zimalimbikitsa mfundo yakuti njira yabwino yothetsera mkangano ndiyo kuchita zachiwawa. Anthu otchuka a m’filimu kawirikawiri amathetsa nkhani zawo mwachiwawa.” Bungweli linaunika bwinobwino mapulogalamu a pa TV ndiponso mafilimu osiyanasiyana. Pamapulogalamu ndi mafilimu 100 aliwonse amene linaunika, akuti ndi 10 okha amene ankaonetsa kuopsa kochita zinthu zachiwawa. Bungweli linanenanso kuti ena onsewo “ankaonetsa kuti chiwawa ndi njira yomveka, yachibadwa, komanso yosapeweka yothetsera mavuto.”

Kodi pamenepa mukuona kuti ndi bwino kuti pakhomo panu musinthe zinthu zina ndi zina pankhani ya kuonera TV? Musamalole kuti zinthu monga mafilimu zikubwezereni m’mbuyo pantchito yanu yophunzitsa ana kukhala amtendere.

[Chithunzi patsamba 17]

Thandizani ana anu kukhala ndi mtima wofuna kusangalatsa “Mulungu wa mtendere”

[Chithunzi patsamba 18]

Yesetsani kuthandiza ana anu kuti asamalankhule kapena kuchita zinthu zokwiyitsa ena

[Chithunzi patsamba 19]

Ana anu ayenera kuphunzira kupepesa ndi kukhululuka