Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Tingapirire Mayesero Alionse

Tingapirire Mayesero Alionse

 Tingapirire Mayesero Alionse

KODI mukukumana ndi mayesero pamoyo wanu panopo? Kodi mukuona kuti simungathenso kuwapirira? Kodi nthawi zina mumafika pochita mantha kuti ndinu nokha muli ndi vutolo ndipo palibe njira yolithetsera? Ngati zili choncho, musataye mtima! Baibulo likutitsimikizira kuti mayesero alionse amene tingakumane nawo, Mulungu angathe kutithandiza kuwapirira.

Baibulo limavomereza kuti atumiki a Mulungu ‘adzagwa m’mayesero a mitundu mitundu.’ (Yakobo 1:2) Taonani mawuwo “mitundu mitundu” (Chigiriki poi·kiʹlos). Malinga ndi mmene mawu achigiriki amenewa ankawagwiritsira ntchito kale, amatanthauza “zambiri ndiponso zosiyanasiyana,” kapena “zokhala ndi mitundu yambiri.” Mawuwa akusonyeza kwambiri “kusiyanasiyana kwa mayesero.” Chotero, “mayesero a mitundu mitundu” ndiwo mayesero amene amabwera m’mitundu yambiri, tingatero kunena kwake. Komabe, Yehova amatichirikiza kuti tithe kupirira mayesero onsewo. N’chifukwa chiyani tingakhale otsimikiza za zimenezi?

“Chisomo cha Mitundu Mitundu cha Mulungu”

Mtumwi Petro ananena kuti Akristu amakhala ‘achisoni ndi mayesero a mitundu mitundu.’ (1 Petro 1:6) Panthawi ina m’kalata yake youziridwa ananena kuti, ‘chisomo cha Mulungu’ chili ‘m’mitundu mitundu.’ (1 Petro 4:10) Mawu akuti ‘m’mitundu mitundu’ ali ndi tanthauzo lofanana ndi mawu achigiriki oyambirira aja. Pochitira ndemanga pa mawu amenewa, katswiri wina wa maphunziro a Baibulo anati: “Tanthauzo limeneli ndi lakuya kwambiri. . . . Kunena kuti kukoma mtima [kapena, chisomo] cha Mulungu ndicho poikilos zikutanthauza kuti, pa mikhalidwe ya mitundu mitundu yomwe munthu angakumane nayo palibe umene ungapose chisomo cha Mulungu.” Iye anapitiriza kunena kuti: “Palibe mikhalidwe, kapena mavuto amwadzidzidzi amene chisomo cha Mulungu chingalephere kuthetsa pamoyo. Mawu omveketsa bwino amenewa akuti poikilos akutikumbutsa kwambiri za chisomo cha Mulungu chokhala ndi mitundu yambiri chimene chingatithandize kupirira zinthu zonse.”

Chisomo cha Mulungu Chimatithandiza Kupirira

Malinga n’kunena kwa Petro, njira imodzi imene Mulungu amasonyezera chisomo chake ndi kudzera mwa anthu osiyanasiyana amene ali mu mpingo wachikristu. (1 Petro 4:11) Mtumiki wa Mulungu aliyense ali ndi mphatso zauzimu, kapena kuti maluso, omwe angalimbikitse amene akukumana ndi mayesero. (Aroma 12:6-8) Mwachitsanzo, anthu ena m’mpingo amaphunzitsa bwino kwambiri Baibulo. Mawu awo anzeru amalimbikitsa ndi kuthandiza ena kupirira. (Nehemiya 8:1-4, 8, 12) Ena nthawi zonse amapanga maulendo aubusa ku nyumba za amene akufunika thandizo. Maulendo amenewa amakhala nthawi yolimbikitsa ndiponso yotonthoza mitima.’ (Akolose 2:2) Pamene oyang’anira apanga maulendo olimbitsa chikhulupiriro otero, amagawira ena mphatso yauzimu. (Yohane 21:16) Palinso ena  m’mpingo amene amadziwika chifukwa cha kusonyeza chikondi ndi chifundo kwa okhulupirira anzawo omwe amakhala achisoni chifukwa cha mayesero. (Machitidwe 4:36; Aroma 12:10; Akolose 3:10) Chifundo ndiponso thandizo zimene abale ndi alongo achikondi amenewa amasonyeza ndi njira yapadera, kapena “mtundu” wa chisomo cha Mulungu.​—Miyambo 12:25; 17:17.

“Mulungu wa Chitonthozo Chonse”

Koposa zonse, Yehova amapereka chitonthozo. Iye ndi “Mulungu wa chitonthozo chonse, wotitonthoza ife m’nsautso yathu yonse.” (2 Akorinto 1:3, 4) Nzeru zopezeka m’Mawu a Mulungu ouziridwa ndiponso mphamvu zoperekedwa ndi mzimu wake woyera ndizo njira zazikulu zimene Yehova amayankhira mapemphero athu tikamapempha thandizo. (Yesaya 30:18, 21; Luka 11:13; Yohane 14:16) Tingalimbikitsidwe ndi lonjezo louziridwa la mtumwi Paulo. Iye anati: “Mulungu ali wokhulupirika, amene sadzalola inu kuyesedwa koposa kumene mukhoza; koma pamodzi ndi chiyeso adzaikanso populumukirapo, kuti mudzakhoze kupirirako.”​—1 Akorinto 10:13.

Ndithudi, kaya mayesero athu akhale ‘amtundu’ wotani, kapena abwere bwanji, nthawi zonse padzakhala njira kapena “mtundu” wa chisomo cha Mulungu umene udzatithandiza kupirira. Thandizo la panthawi yake ndiponso loyenera la Yehova kwa atumiki ake ndi umboni umodzi wa “nzeru ya mitundu mitundu ya Mulungu,” ngakhale ziyeso kapena mavuto atakhala osiyanasiyana chotani. (Aefeso 3:10) Kodi simukuvomereza zimenezi?

[Zithunzi patsamba 31]

Yehova amatithandiza kupirira mayesero athu