Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Ntchito ndi Dalitso Kapena Temberero?

Kodi Ntchito ndi Dalitso Kapena Temberero?

 Kodi Ntchito ndi Dalitso Kapena Temberero?

‘Kodi si chabwino kuti munthu . . . aonetse moyo wake zabwino m’ntchito yake?’​—Mlaliki 2:24.

“POWERUKA ndimakhala nditatheratu n’kutopa.” Izi n’zimene munthu mmodzi mwa anthu atatu alionse ogwira ntchito ananena m’kafukufuku amene anachitika posachedwa, pofotokoza mmene amamvera nthawi zambiri. Zimenezitu n’zosadabwitsa chifukwa anthu akukhala mopanikizika maganizo kwambiri. Amagwira ntchito maola ambiri, mpaka ntchito zina amazitengera kunyumba. Kuwonjezera pa zimenezo, alinso ndi mabwana amene nthawi zambiri sawayamikira.

Kubwera kwa makampani akuluakulu opanga zinthu kwapangitsa apantchito ambiri kudziona kukhala ngati osanunkha kanthu pa kampani yaikulu imene sadziwika n’komwe kwa mabwana. Kawirikawiri, kulimbikira kwa munthu ndiponso maganizo othandiza amene angapereke zimangoponderezedwa. Mwachibadwa, zimenezi zimapangitsa anthu kuona ngati ntchito ndi yoipa.  Chidwi chonse chakuti munthu alimbikire ntchito chimatha. Munthu sakhalanso ndi chikhumbo choti apititse patsogolo luso lake. Zinthu ngati zimenezi zingapangitse munthu kusaikonda ntchito yake.

Kudzifufuza Mmene Timaionera Ntchito

Kunena zoona, si nthawi zonse pamene tingathe kusintha ntchito. Komabe, kodi simukuvomereza kuti maganizo athu a mmene timaionera ntchito tikhoza kuwasintha? Ngati mupeza kuti inunso pang’onopang’ono mwayamba kutengera maganizo osakonda ntchito, ndi bwino kuganizira za mmene Mulungu amaonera nkhaniyi. Muyenera kuganiziranso mfundo za m’Malemba zokhudza nkhani imeneyi. (Mlaliki 5:18) Anthu ambiri aona kuti kulingalira zimenezi kwawathandizako kukhala osangalala ndi okhutira ndi ntchito yawo.

Mulungu ndi Wogwira Ntchito Woposa. Mulungu amagwira ntchito. Mwina simunayambe mwam’ganizirapo mwa njira imeneyi, koma n’zimene mwiniwakeyo akuyamba nazo potidziwitsa za iye m’Baibulo. Buku la Genesis limayamba ndi kufotokoza mmene Yehova analengera kumwamba ndi dziko lapansi. (Genesis 1:1) Taganizani ntchito zosiyanasiyana zimene Mulungu anachita pamene anayamba kulenga. Iye anali, wokonza mapulani, mmisiri wopanga zinthu, waluso lokongoletsa zinthu, katswiri wosankha zipangizo, katswiri wa mankhwala opangira zinthu, katswiri wa mmene thupi limagwirira ntchito, katswiri wa zinyama, katswiri wa zinenero, kungotchulapo zochepa chabe.​—Miyambo 8:12, 22-31.

Kodi ntchito ya Mulungu itatha inali yotani? Baibulo limanena kuti zimene anapangazo zinali ‘zabwino,’ “zabwino ndithu.” (Genesis 1:4, 31) Ndithudi, zolengedwa “zimalalikira ulemerero wa Mulungu,” ifenso tiyenera kumutamanda!​—Salmo 19:1; 148:1.

Komabe, ntchito ya Mulungu siinalekezere pa kulenga zinthu zakumwamba zooneka, kenako dziko lapansi ndi anthu awiri oyamba aja, ayi. Mwana wa Yehova, Yesu Kristu, anati: “Atate wanga amagwira ntchito kufikira tsopano.” (Yohane 5:17) Inde, Yehova akugwirabe ntchito mwa kusamalira zolengedwa zake, kuchirikiza chilengedwe chonse, ndiponso mwa kupulumutsa om’pembedza okhulupirika. (Nehemiya 9:6; Salmo 36:6; 145:15, 16) Iye amatha kugwiritsa ntchito ngakhale anthu, “antchito anzake a Mulungu,” kuti athandize kuchita ntchito zina.​—1 Akorinto 3:9.

Ntchito imatha kukhala dalitso. Kodi Baibulo silisonyeza kuti ntchito ndi temberero? Lemba la Genesis 3:17-19 lingaoneke ngati likusonyeza kuti, pamene Mulungu anauza Adamu ndi Hava kuti adzafunikira kugwira ntchito molimbika, anali kuwapatsa chilango chifukwa cha kupanduka kwawo. Poweruza anthu oyambirirawo, Mulungu anati kwa Adamu: “M’thukuta la nkhope yako udzadya chakudya, kufikira kuti udzabwerera kunthaka.” Kodi mawu amenewa akusonyeza kuti ntchito inakhala temberero?

Ayi. Koma anatanthauza kuti, chifukwa cha kusakhulupirika kwa Adamu ndi Hava, ntchito yofutukula Paradaiso wa Edene siikanathekanso panthawiyo. Nthaka inali itatembereredwa ndi Mulungu. Kuti munthu akhalebe ndi moyo anafunikira kugwira ntchito mokhetsa thukuta kuti apeze chakudya m’nthaka.​—Aroma 8:20, 21.

M’malo mosonyeza ngati kuti ntchito ndi temberero, Baibulo limasonyeza kuti ndi dalitso loyenera kuliyamikira. Monga taonera kale, Mulungu mwiniyo ndi wolimbika pantchito. Yehova atalenga anthu m’chifanizo chake, anawapatsa mphamvu ndi ulamuliro wakuti asamalire chilengedwe chake cha pansi pano. (Genesis 1:26, 28; 2:15) Udindo umenewo Mulungu anawapatsa asanapereke chiweruzo cholembedwa pa Genesis 3:19. Ntchito ikanakhala temberero komanso chinthu choipa, Yehova sakanalimbikitsa konse anthu kugwira ntchito. Nowa ndi banja lake anali ndi ntchito yambiri yoti aigwire pambuyo pa Chigumula. M’nthawinso za Chikristu, ophunzira a Yesu analimbikitsidwa kugwira ntchito.​—1 Atesalonika 4:11.

Komabe, tonse timadziwa kuti masiku ano ntchito imatha kukhala chinthu chopweteka kwambiri. Ina ya “minga ndi mitula” ya ntchito masiku ano ndiyo nkhawa, ngozi za pantchito, kusungulumwa, zokhumudwitsa, mpikisano, zachinyengo, ndi kupanda chilungamo. Komatu sikuti ntchito yeniyeniyo ndi temberero ayi. Pa Mlaliki 3:13, Baibulo limasonyeza kuti ntchito limodzi ndi mapindu ake ndi mphatso yochokera kwa Mulungu.​—Onani kabokosi kakuti “Kupirira Nkhawa Zobwera Chifukwa cha Ntchito.”

 Mukhoza kulemekeza Mulungu ndi ntchito yanu. Nthawi zonse ngati ntchito yagwirika bwino imakhala yotamandika. Kugwira bwino ntchito n’chimodzi mwa zinthu zimene Baibulo limanena kuti n’zofunika pa ntchito. Mulungu mwiniyo amagwira ntchito bwino koposa. Iye watipatsa nzeru ndi luso, ndipo amafuna kuti tizigwiritse ntchito pa ntchito zabwino. Mwachitsanzo, pantchito yomanga chihema mu Israyeli wakale, Yehova anapatsa anthu ngati Bezaleli ndi Oholiba nzeru zowirikiza, kumvetsa zinthu, ndi kuzindikira, zimene zinawathandiza kugwira bwino ntchito zawo za luso la manja. (Eksodo 31:1-11) Zimenezi zimasonyeza kuti Mulungu anafunitsitsa kuti umisiri, mapulani, ndi mbali zina zonse zokhudza ntchitoyo zichitike bwino.

Zimenezi ziyenera kukhudza kwambiri mmene timaonera maluso athu ndi zizolowezi zathu pantchito. Zimatithandiza kuona mbali zimenezi monga mphatso yochokera kwa Mulungu, imene sitiyenera  kuitenga mopepuka. Choncho, tikulimbikitsa Akristu kuti pogwira ntchito zawo, azigwira ngati kuti Mulungu akuyang’anira mmene akuigwirira. Paja lemba la Akolose 3:23 limati: “Chilichonse mukachichita, gwirani ntchito mochokera mumtima, monga kwa Ambuye, osati kwa anthu ayi.” Atumiki a Mulungu akulamulidwa kugwira ntchito mwakhama, kuti uthenga wachikristu ukhale wokopa kwa apantchito anzawo ndi anthu ena.​—Onani kabokosi kakuti “Kutsatira Mfundo za M’Baibulo ku Ntchito.”

Pachifukwa chimenechi, tingachite bwino kudzifunsa mmene timagwirira ntchito ndiponso khama limene timachita. Kodi Mulungu angakondwere ndi mmene timagwirira ntchito yathu? Kodi timakhutiradi ndi mmene timagwirira ntchito zimene tapatsidwa? Ngati sitikhutira kwenikweni, mpata ulipo wakuti tiwongolere.​—Miyambo 10:4; 22:29.

Ikani ntchito ndi zinthu zauzimu pa malo ake. Ngakhale kuti kugwira ntchito molimbika ndi chinthu chotamandika, palinso chinsinsi china chomwe chingatithandize kukhutira ndi ntchito komanso ndi moyo wathu. Ndicho zinthu zauzimu. Mfumu Solomo, amene anali kugwira ntchito molimbika ndi kusangalala ndi chuma ndi zabwino zonse zimene munthu angakhale nazo pamoyo, ananena kuti: ‘Opa Mulungu, nusunge malamulo ake; pakuti choyenera anthu onse ndi ichi.’​—Mlaliki 12:13.

Mwachionekere, tiyenera kuganizira zimene Mulungu amafuna pa chilichonse chimene tiyenera  kuchita. Kodi timachita zinthu mogwirizana ndi zimene iye amafuna, kapena timachita zosemphana ndi chifuniro chake? Kodi timayesetsa kum’kondweretsa Mulungu, kapena kwenikweni cholinga chathu ndi kuchita zotisangalatsa? Ngati sitichita zimene Mulungu amafuna, potsirizira pake tidzakhala okhumudwa, osungulumwa, ndipo tiziona kuti ndife osanunkha kanthu.

Steven Berglas anati mabwana otopa ndi ntchito modetsa nkhawa ‘amakhala ndi cholinga chimene amavutikira, ndipo chimakhala mbali ya moyo wawo.’ Koma palibe cholinga chingakhale chaphindu kuposa kutumikira Uyo amene anatipatsa nzeru ndi luso lochitira ntchito zatanthauzo. Sitingakhale anthu osakhutira ngati tigwira ntchito imene imakondweretsa Mlengi wathu. Yesu anaona ntchito imene Yehova anam’patsa ngati chakudya. Inali yom’patsa thanzi, yokhutiritsa, ndi yotsitsimutsa. (Yohane 4:34; 5:36) Ndipo kumbukirani kuti Mulungu, amene ndi Wantchito Wopambana, akutipempha kukhala “antchito anzake.”​—1 Akorinto 3:9.

Kupembedza Mulungu ndi kukula mwauzimu kumatikonzekeretsa ntchito ndi udindo wopindulitsa. Popeza kuntchito nthawi zambiri kumakhala zochitika zotipatsa nkhawa, mikangano, ndi zopanikiza zina, chikhulupiriro chathu chozama komanso zinthu zauzimu, zingatithandize kwambiri pamene tikuyesetsa kukhala ogwira ntchito odalirika kapena mabwana abwino. Komanso, zimene zimachitika pamoyo m’dziko losaopa Mulunguli, zingatithandize kuzindikira mbali zimene tingafunikire kukulitsa chikhulupiriro chathu.​—1 Akorinto 16:13, 14.

Pamene Ntchito Idzakhaladi Dalitso Lenileni

Amene akuchita zonse zotheka kuti atumikire Mulungu angakhale ndi chiyembekezo chodzakhalapo pamene Mulungu adzabwezeretsa Paradaiso, ndipo dziko lonse lapansi lidzakhala ndi ntchito zopindulitsa zokhazokha. Polosera za moyo wa panthawi imeneyo, Yesaya, mneneri wa Yehova anati: “Iwo adzamanga nyumba ndi kukhalamo; ndipo iwo adzawoka minda yamphesa, ndi kudya zipatso zake. Iwo sadzamanga, ndi wina kukhalamo; iwo sadzawoka, ndi wina kudya; . . . Osankhidwa anga adzasangalala nthawi zambiri ndi ntchito za manja awo.”​—Yesaya 65:21-23.

Ha! mmene ntchito idzakhalire yopindulitsa panthawiyo. Mukadziwa zimene Mulungu amafuna kuti akuchitireni, komanso mukakhala ndi moyo wochita zimene Mulungu amafuna, mudzakhala mmodzi wa odalitsika a Yehova, ndipo ‘mudzaona zabwino m’ntchito zanu zonse.’​—Mlaliki 3:13.

[Mawu Otsindika patsamba 8]

Mulungu ndi Wantchito Wopambana: Genesis 1:1, 4, 31; Yohane 5:17

[Mawu Otsindika patsamba 8]

Ntchito ikhoza kukhala dalitso: Genesis 1:28; 2:15; 1 Atesalonika 4:11

[Mawu Otsindika patsamba 8]

Mukhoza kulemekeza Mulungu ndi ntchito yanu: Eksodo 31:1-11; Akolose 3:23

[Mawu Otsindika patsamba 8]

Kuika ntchito ndi zinthu zauzimu pa malo ake: Mlaliki 12:13; 1 Akorinto 3:9

[Bokosi/​Chithunzi patsamba 6]

KUPIRIRA NKHAWA ZOBWERA CHIFUKWA CHA NTCHITO

Akatswiri a zamatenda aika nkhawa zobwera chifukwa cha ntchito m’gulu la ngozi za pantchito. Nkhawazo zimatha kuyambitsa zilonda za m’mimba ndi kudwala maganizo, ngakhale kupangitsa munthu kudzipha kumene. Ajapani ali ndi mawu otchulira nkhawa zimenezi zodza ndi ntchito. Amati karoshi, kutanthauza “kufa ndi ntchito.”

Pali zinthu zambiri zokhudzana ndi ntchito zimene zingayambitse nkhawa zimenezi. Zina mwa izo ndi kusintha nthawi yogwirira ntchito kapena magwiridwe antchito, kusiyana maganizo ndi mabwana, kusinthidwa maudindo kapena mtundu wa ntchito, kupumitsidwa pantchito, ndiponso kuchotsedwa ntchito. Pokhumudwa ndi zimenezi, ena amayesa kupezako mtendere wa maganizo mwa kusintha ntchito kapena malo. Ena amayesa kubisa nkhawa zimenezi, koma zimakatulukirabe m’mbali zina za moyo, nthawi zambiri zimakatulukira m’banja. Anthu ena amafika mpaka podwala ndi maganizo ndiponso kutaya mtima.

Akristu ali ndi zida zonse zowathandiza kupirira nkhawa zobwera chifukwa cha ntchito. Baibulo limapereka mfundo zambiri zofunikira zomwe zingatipatse nyonga yauzimu ndi kutilimbikitsa maganizo panthawi zovuta. Mwachitsanzo, Yesu anati: “Musadere nkhawa za mawa; pakuti mawa adzadzidera nkhawa iwo okha. Zikwanire tsiku zovuta zake.” Mfundo pano ndi yotilimbikitsa kuika maganizo athu pa mavuto a lero, osati a mawa. Tikatero, tidzapewa kukokomeza mavuto athu, zomwe zingangotikulitsira nkhawa.​—Mateyu 6:25-34.

Ndi chinthu chofunika kwambiri kuti Akristu azidalira mphamvu ya Mulungu, osati yawo ayi. Zikafika poti sitingathenso kupirira, Mulungu amatha kutipatsa mtendere ndi chisangalalo mu mtima. Amatipatsanso nzeru zotithandiza kuthana ndi vuto lililonse. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Chotsalira, tadzilimbikani mwa Ambuye, ndi m’kulimba kwa mphamvu yake.”​—Aefeso 6:10; Afilipi 4:7.

Mfundo yomalizira n’jakuti, zochitika zodetsa nkhawa nazonso zingathe kukhala ndi zotsatirapo zabwino. Mayesero angatichititse kutembenukira kwa Yehova, kupempha thandizo lake, ndi kum’dalira. Mayesero angatithandizenso kupitiriza kukulitsa umunthu wachikristu ndi kutipatsa mphamvu kuti tithe kupirira nkhawa. Paulo akutilangiza kuti: “Tikondwera m’zisautso; podziwa ife kuti chisautso chichita chipiriro; ndi chipiriro chichita chizolowezi; ndi chizolowezi chichita chiyembekezo.”​—Aroma 5:3, 4.

Choncho, nkhawanso zingathe kuthandiza munthu kukula mwauzimu, m’malo mwakuti ataye mtima ndi kukhala wachisoni.

[Bokosi/​Chithunzi patsamba 7]

KUTSATIRA MFUNDO ZA M’BAIBULO KU NTCHITO

Khalidwe la Mkristu ku ntchito lingapangitse uthenga wa m’Baibulo kukhala wokopa kwa apantchito anzake ndi anthu ena. M’kalata imene mtumwi Paulo analembera Tito, analangiza awo amene ali pamalo ofanana ndi a wantchito kuti “amvere ambuye awo [mabwana] a iwo okha, nawakondweretse m’zonse; osakana mawu awo; osatapa pa zawo, komatu aonetsere chikhulupiriko chonse chabwino; kuti akakometsere chiphunzitso cha Mpulumutsi wathu Mulungu m’zinthu zonse.”​—Tito 2:9, 10.

Mwachitsanzo, tamverani zimene mwamuna wina wabizinesi analembera ku likuli la padziko lonse la Mboni za Yehova. Iye anati: “Ndikupempha chilolezo chanu kuti ndilembe ganyu a Mboni za Yehova. Ndikufuna iwo chifukwa ndikudziwa kuti ndi anthu oona mtima, okhulupirika, ndiponso odalirika, komanso sangandichite zachinyengo. Anthu okhawo omwe ndimawakhulupirira ndi a Mboni za Yehova. Thandizeni chonde.”

Kyle ndi mzimayi wachikristu yemwe amagwira ntchito pamalo olandirira alendo pasukulu imene si yaboma. Atasiyana maganizo ndi mzimayi mnzake amene amagwira naye ntchito, mnzakeyo anamutukwana pamaso pa ana asukulu. Kyle akukumbukira kuti: “Ndinayesetsa kusamala kwambiri kuti ndisanyozetse dzina la Yehova.” Kwa masiku asanu otsatira, Kyle anasinkhasinkha mmene akanagwiritsira ntchito mfundo za makhalidwe abwino za m’Baibulo. Imodzi ya mfundozo imapezeka pa lemba la Aroma 12:18. Mfundoyo imati: “Ngati n’kutheka, monga momwe mukhoza, khalani ndi mtendere ndi anthu onse.” Iye anatumizira mnzakeyo uthenga wa pakompyuta ndipo anam’pepesa chifukwa cha kusemphana maganizo kwawo. Mu uthengawo, Kyle anapempha mnzakeyo kuti atsalire akaweruka kuti akambirane ndi kubwezeretsa mtendere pakati pawo. Zimenezo zitachitika, mnzake wa Kyle anabweza mtima nayamikira njira yanzeru imene Kyle anaigwiritsa ntchito. Iye anauza Kyle kuti, “Ndikhulupirira watha kuchita zimenezi chifukwa cha chipembedzo chako,” ndipo anam’kumbatira mwachikondi natsazikana. Kodi Kyle anati chiyani ataona zimenezi? Anati: “Ukatsatira mfundo za m’Baibulo sunong’oneza bondo.”

[Chithunzi pamasamba 4, 5]

Apantchito ochuluka amadziona ngati osanunkha kanthu pa kampani yaikulu imene amakhala osadziwika kwa mabwana

[Mawu a Chithunzi]

Japan Information Center, Consulate General of Japan in NY

[Mawu a Chithunzi patsamba 8]

Globe: NASA photo