Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 NKHANI YA PACHIKUTO | N’CHIFUKWA CHIYANI YESU ANAVUTIKA MPAKA KUFA?

Kodi Zinachitikadi?

Kodi Zinachitikadi?

Kumayambiriro kwa chaka cha 33 C.E., Yesu wa ku Nazareti anaimbidwa mlandu wabodza woukira boma. Anamenyedwa kwambiri ndipo kenako anakhomereredwa pamtengo. Yesu anafa mozunzika kwambiri. Komabe Mulungu anamuukitsa ndipo patatha masiku 40 anabwerera kumwamba.

Nkhani imeneyi imapezeka m’mabuku 4 a Uthenga Wabwino m’Malemba Achigiriki Achikhristu, omwe anthu ambiri amawatchula kuti Chipangano Chatsopano. Koma kodi nkhaniyi inachitikadi? Funso limeneli ndi lofunika kwambiri chifukwa ngati zili zabodza, ndiye kuti zimene Akhristu amakhulupirira ndi zopanda phindu, komanso zimene amayembekezera zoti dzikoli lidzakhala Paradaiso ndi maloto chabe. (1 Akorinto 15:14) Koma ngati zinachitikadi, ndiye kuti akuyembekezera zinthu zabwino kwambiri mtsogolo ndipo inunso mukhoza kudzasangalala ndi zinthu zimenezi. Ndiye funso ndi lakuti, Kodi nkhani zimene zili m’Mabuku a Uthenga Wabwino ndi zoonadi?

UMBONI WOTSIMIKIZIRA KUTI ZINACHITIKADI

Mosiyana ndi nkhani zongopeka zomwe anthu amakhulupirira, nkhani zomwe zili m’Mauthenga Abwino ndi zolondola chifukwa zinafufuzidwa mosamala kwambiri. Mwachitsanzo, nkhanizi zimatchula mayina  enieni a malo ndipo ambiri mwa malowa ndi oti anthu amapitako. Zimatchulanso mayina enieni a anthu ndipo olemba mbiri ena amatsimikizira kuti anthuwo anakhalakodi.—Luka 3:1, 2, 23.

Olemba mbiri ena omwe analipo pa nthawiyo analembanso nkhani zina zokhudza Yesu. * Nkhani za m’mabuku a Uthenga Wabwino zokhudza mmene Yesu anafera, zimagwirizana ndi zimene Aroma ankachita akafuna kunyonga munthu. Komanso zinthu zimene zinachitika zinalembedwa molondola ndipo olembawo sanabise china chilichonse moti analembanso zimene otsatira a Yesu analakwitsa. (Mateyu 26:56; Luka 22:24-26; Yohane 18:10, 11) Mfundo zonsezi zikusonyezeratu kuti amene analemba mabuku a Uthenga Wabwino analemba zinthu zolondola zokhudza Yesu.

KODI YESU ANAUKITSIDWADI?

Anthu ambiri amavomereza kuti Yesu anakhalako padziko lapansili ndipo kenako anamwalira. Koma pali anthu ena amene amatsutsa zoti anaukitsidwa. Zimenezi n’zimenenso atumwi ake anachita chifukwa sanakhulupirire atangomva kuti Yesu waukitsidwa. (Luka 24:11) Koma Yesu ataonekera kwa atumwiwo ndiponso kwa ophunzira ake ena, m’pamene anakhulupirira kuti waukitsidwadi. Ndipo nthawi ina Yesu anaonekeranso kwa anthu opitirira 500.—1 Akorinto 15:6.

Atumwiwo anayamba kulengeza molimba mtima kuti Yesu waukitsidwa ngakhale kuti ankadziwa kuti akhoza kumangidwa kapenanso kuphedwa chifukwa chochita zimenezi. Iwo ankalengeza uthenga umenewu ngakhale kwa anthu omwe anapha Yesu. (Machitidwe 4:1-3, 10, 19, 20; 5:27-32) Ophunzira a Yesu sakanalimba mtima kumalengeza kuti waukitsidwa pamene sanaukitsidwe. Ndipotu anthu ambiri pa nthawiyo anakhala Akhristu chifukwa cha kuukitsidwa kwa Yesu ndipo ndi mmenenso zikuchitikira masiku ano.

Zimene mabuku a Uthenga Wabwino amanena zokhudza imfa ya Yesu komanso kuukitsidwa kwake ndi zenizeni. Mukamaphunzira nkhanizi mwakhama mudzazindikira kuti zinachitikadi. Kenako mudzayamba kumvetsa chifukwa chake zinthu zimenezi zinachitika. Ndipo nkhani yotsatira ifotokoza chifukwacho.

^ ndime 7 Mwachitsanzo, katswiri wina wolemba mbiri yakale, dzina lake Tacitus, yemwe anabadwa cha m’ma 55 C.E., analemba kuti: “Khristu, [dzina limene Akhristu anatengerako dzina lawo] anazunzidwa kwambiri ndi bwanamkubwa wathu Pontiyo Pilato, pa nthawi ya ulamuliro wa Mfumu Tiberiyo.” Palinso olemba mbiri ena a m’zaka 100 zoyambirira amene anachitira umboni za Yesu monga Seutonius ndi Josephus, wolemba mbiri wachiyuda. Zitatha zaka 100 zoyambirira, Pliny Wamng’ono yemwe anali bwanamkubwa wa mzinda wa Bituniya, nayenso analemba zokhudza Yesu.