Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Akhristu Ayenera Kumapemphera mu Akachisi?

Kodi Akhristu Ayenera Kumapemphera mu Akachisi?

CHAKA chilichonse anthu oposa 6 miliyoni amapita kunkhalango ina yomwe ili pachilumba cha Shima m’dziko la Japan. Kwa zaka pafupifupi 2,000, anthu achipembedzo cha Chishinto akhala akupita kunkhalangoyi kukalambira mulungu wa dzuwa, m’kachisi wamkulu wa Ise. Mulunguyu ndi wamkazi ndipo dzina lake ndi Amaterasu Omikami. Anthuwa asanalowe m’kachisiyu amadziyeretsa posamba m’manja ndi kutsuka mkamwa. Akatero, amaima atayang’ana kachisiyu n’kuwerama, kuomba m’manja kenako amapemphera kwa mulungu wamkaziyu. * Chipembedzo cha Chishinto chimalola kuti anthu am’chipembedzochi azitsatiranso zikhulupiriro za zipembedzo zina. Ndipo anthu enanso a Chibuda, Chikhristu ndi zipembedzo zina amaona kuti palibe vuto lina lililonse kukachita nawo miyambo yomwe imachitika kukachisiyu.

Zipembedzo zikuluzikulu zambiri padzikoli zili ndi akachisi * amene anthu ambiri amapitako. Ndipo m’mayiko amene anthu ambiri ndi Akhristu mulinso akachisi ndi matchalitchi ambiri amene anthu amalambiriramo Yesu, Mariya komanso anthu ena oyera mtima. Akachisi ena amamangidwa m’malo amene zinthu zina zotchulidwa m’Baibulo zinachitikira ndipo ena amamangidwa m’malo amene anthu amaganiza kuti munachitika zozizwitsa m’nthawi yathu ino. Anthu enanso amamanga akachisi awo m’malo amene anasungirako zinthu zakale zokhudza chipembedzo chawo. Anthu ambiri amakonda kupita ku akachisi chifukwa amakhulupirira kuti Mulungu amamva mapemphero awo akamapemphera ali kumalo enaake apadera. Pamene anthu ena amaona kuti kupita ku akachisi ndi chizindikiro chakuti munthu ndi wodzipereka kwambiri pa nkhani za kulambira.

Alendo ali pakachisi wamkulu wa Ise ku Japan, komanso phanga la Massabielle ku Lourdes, m’dziko la France

Koma kodi n’zoona kuti Mulungu amamva ndi kuyankha mapemphero a anthu okhawo amene amakapempherera ku akachisi? Kodi Mulungu amasangalala ndi anthu amene amayenda maulendo aatali opita ku akachisi posonyeza kuti amamulambira modzipereka? Nanga kodi kulambira Mulungu ku akachisi n’koyenera? Mayankho a mafunso amenewa atithandiza kudziwa ngati n’koyenera kulambira mu akachisi. Atithandizanso kudziwa kulambira kumene Mulungu amavomereza.

TIZILAMBIRA MULUNGU “MOTSOGOLEREDWA NDI MZIMU NDI CHOONADI”

Kodi Yesu ankatanthauza chiyani pamene ananena kuti tiyenera kulambira Mulungu motsogoleredwa “ndi mzimu ndi choonadi”?

Zimene Yesu anakambirana ndi mayi wina wachisamariya zimasonyeza mmene Mulungu amaonera nkhani ya kulambira ‘pamalo opatulika’ kapena akachisi. Tsiku lina Yesu akudutsa ku Samariya anaima kuti apume pachitsime china chomwe chinali pafupi ndi mzinda wa Sukari. Kenako mayi wina wachisamariya anafika pachitsimepo kudzatunga madzi. Mayiyo atafika, Yesu anayamba kukambirana naye. Akukambirana, mayiyo ananena mfundo yosonyeza kuti Ayuda ndi Asamariya ndi anthu osiyana zikhulupiriro. Iye anati: “Makolo athu anali kulambira m’phiri ili, koma anthu inu mumanena kuti Yerusalemu ndiwo malo kumene anthu ayenera kulambirirako.”—Yohane 4:5-9, 20.

 Mayiyu ankanena za phiri la Gerizimu lomwe lili pamtunda wa makilomita pafupifupi 50, kumpoto kwa mzinda wa Yerusalemu. M’phiri limeneli Asamariya anali ndi kachisi yemwe ankachitirako zikondwerero monga Pasika. M’malo motaya nthawi n’kumafotokoza za kusiyana zikhulupiriro komwe kunalipo pakati pa Ayuda ndi Asamariya, Yesu ananena kuti: “Mayi, ndithu nthawi idzafika pamene anthu inu simudzalambira Atate m’phiri ili kapena ku Yerusalemu.” (Yohane 4:21) N’zochititsa chidwi kumva kuti Yesu ananena kuti anthu sadzalambiranso ku Yerusalemu, pomwe iyeyo anali Myuda. Koma kodi n’chifukwa chiyani anthu anafunika kusiya kulambira Mulungu ku Yerusalemu?

Yesu ananenanso kuti: “Nthawi idzafika, ndipo ndi yomwe ino, pamene olambira oona adzalambira Atate motsogoleredwa ndi mzimu ndi choonadi, pakuti Atate amafuna oterowo azimulambira.” (Yohane 4:23) Kwa zaka zambiri Ayuda ankaona kuti kachisi wa ku Yerusalemu yemwe anali wokongola kwambiri anali likulu la kulambira kwawo. Iwo ankapita kukachisiyu katatu pachaka kukapereka nsembe kwa Mulungu wawo Yehova. (Ekisodo 23:14-17) Koma Yesu ananena kuti zinthu zidzasintha ndipo “olambira oona” azidzalambira motsogoleredwa ndi “mzimu ndi choonadi.”

Kachisi yemwe Ayuda ankalambirirako anali nyumba yeniyeni komanso anali kudera linalake lodziwika bwino. Koma mzimu ndi choonadi ndi zinthu zosaoneka. Choncho mfundo ya Yesu inali yakuti kulambira Mulungu m’njira yovomerezeka sikudalira kuti anthu azipita kumalo apadera olambirirako monga kachisi wa ku Yerusalemu, phiri la Gerizimu kapenanso malo ena opatulika.

Pokambirana ndi mayi wachisamariya uja, Yesu ananenanso kuti “nthawi idzafika” pamene anthu azidzalambira Mulungu motsogoleredwa ndi mzimu ndi choonadi. Kodi nthawiyi inafika liti? Inafika pamene Yesu anapereka moyo wake monga nsembe. Chifukwa cha nsembe imeneyi, Yesu anathetsa dongosolo lomwe Ayuda ankalambirira Mulungu motsatira Chilamulo cha Mose. (Aroma 10:4) Komabe Yesu ananenanso kuti: “Nthawi . . . ndi yomwe ino.” N’chifukwa chiyani ananena zimenezi? Chinali chifukwa chakuti monga Mesiya, iye anali atayamba kale kusonkhanitsa ophunzira amene akanamvera lamulo linanso lomwe ananena lakuti: “Mulungu ndiye Mzimu, ndipo onse omulambira ayenera kumulambira motsogoleredwa ndi mzimu ndi choonadi.” (Yohane 4:24) Ndiyeno kodi kulambira Mulungu motsogoleredwa ndi mzimu ndi choonadi kumatanthauza chiyani?

Pamene Yesu ankanena za kulambira motsogoleredwa ndi mzimu, ankanena za mzimu woyera wa Mulungu womwe umatithandiza kumvetsa bwino Malemba. (1 Akorinto 2:9-12) Ndipo choonadi chimene Yesu ankanena chimatanthauza kudziwa molondola zimene Baibulo limaphunzitsa. Zimenezi zikutanthauza  kuti Mulungu angavomereze kulambira kwathu ngati kulambirako kukugwirizana ndi zimene Baibulo limaphunzitsa. Ndipo angavomerezenso kulambira kwathu ngati timatsogoleredwa ndi mzimu woyera, osati chabe chifukwa chakuti timamulambirira pamalo enaake apadera.

KODI AKHRISTU AYENERA KUPEMBEDZA MULUNGU MU AKACHISI?

Kodi Akhristu ayenera kupita ku akachisi kapena malo enaake apadera kukalambira Mulungu? Tikaganizira zimene Yesu ananenazi, n’zoonekeratu kuti kulambirira mu akachisi kapena pamalo enaake apadera kulibe phindu lililonse. Ndipotu Baibulo limatiuzanso mmene Mulungu amaonera kulambira mafano. Limati: “Thawani kupembedza mafano.” Limanenanso kuti: “Pewani mafano.” (1 Akorinto 10:14; 1 Yohane 5:21) Choncho Mkhristu woona sangalambire Mulungu pamalo omwe anthu amawaona kuti ndi opatulika kapenanso omwe amalimbikitsa kupembedza mafano. Akhristu oona salambira Mulungu mu akachisi chifukwa cha zimene zimachitika ku akachisiwa.

Komatu Mawu a Mulungu saletsa munthu kusankha malo enaake kuti akapemphere, kuphunzira kapenanso kuganizira zomwe waphunzira. Ndipotu anthufe timafunika kukhala ndi malo adongosolo komanso olemekezeka kuti tiphunzire komanso kukambirana bwino Mawu a Mulungu. Komanso sikulakwa kukumbukira munthu amene anamwalira mwina pomuwakira manda ake. Kuchita zimenezi kumangosonyeza kuti munthuyo tinkamukonda. Komabe kuona malo oterewa kuti ndi opatulika kapena kulambira zithunzi kapena zinthu zina zoikidwa pamalowa n’kosemphana kwambiri ndi zimene Yesu ananena.

Mfundo zomwe taona m’nkhaniyi zikusonyeza kuti sitiyenera kupita ku akachisi kapena malo enaake apadera kuti Mulungu amve mapemphero athu. Komanso sikuti Mulungu angatidalitse mwanjira inayake chifukwa choti tayenda ulendo wopita kumalo enaake opatulika kukamulambira. Baibulo limanena kuti Yehova Mulungu, yemwe ndi “Ambuye wakumwamba ndi dziko lapansi sakhala mu akachisi opangidwa ndi manja.” Koma zimenezi sizikutanthauza kuti sangamve mapemphero athu. Tikhoza kupemphera kwa Mulungu ndipo akhoza kutimva tili kulikonse chifukwa “iye sali kutali ndi aliyense wa ife.”—Machitidwe 17:24-27.

^ ndime 2 Miyambo imene imachitika mu akachisi osiyanasiyana a Chishinto imakhalanso yosiyana.

^ ndime 3 Onani bokosi lakuti, “ Kodi Kachisi N’chiyani?