Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Zimene Muyenera Kudziwa Zokhudza Magetsi ndi Mafuta

Zimene Muyenera Kudziwa Zokhudza Magetsi ndi Mafuta

TIMADALIRA mphamvu za magetsi komanso mafuta kuti tichite zinthu zambiri zatsiku ndi tsiku. Mwachitsanzo, magetsi amathandiza kutenthetsa kapena kuziziritsa m’nyumba ndipo magalimoto amafunika mafuta kuti ayende. Komatu padziko lonse anthu akukumana ndi mavuto pankhani ya magetsi ndi mafuta.

A Gary a ku South Africa anati: “Kukwera mtengo kwa mafuta ndi nkhani yaikulu.” A Jennifer a ku Philippines ananena kuti amada nkhawa kwambiri chifukwa cha kusadalirika kwa ‘magetsi omwe amangozima nthawi ndi nthawi.’ Nawonso a Fernando, a ku El Salvador anati: “Ndimakhudzidwa kwambiri chifukwa chakuti zachilengedwe zikuwonongeka.” Padziko lonse, makampani ndi mafakitale amene amapanga mphamvu za magetsi ndi mafuta amawononga kwambiri zachilengedwe.

Mwina mungafunse kuti, ‘Kodi ineyo ndingatani kuti ndilimbane ndi mavuto amenewa?’

Tonsefe tingathe kugwiritsa ntchito magetsi ndi mafuta mwanzeru. Kugwiritsa ntchito zinthuzi mosamala kumathandiza kuti tisamawononge ndalama zambiri. Tikamachita zimenezi timathandizanso kuti chilengedwe chisamawonongeke komanso timachepetsa mavuto a magetsi ndi mafuta.

Tiyeni tione njira zitatu zimene zingatithandize kugwiritsa ntchito bwino magetsi ndi mafuta tikakhala kunyumba kwathu, pa nkhani ya mayendedwe komanso pa zochita za tsiku ndi tsiku.

KUNYUMBA

Muzigwiritsira ntchito mosamala zipangizo zotenthetsera komanso zoziziritsira m’nyumba. Kafukufuku amene anachitika m’dziko lina la ku Europe anasonyeza kuti kutsitsa pang’ono chipangizo chotenthetsera m’nyumba kungathandize kuti mphamvu zambiri zamagetsi zisamawonongeke pachaka. A Derek amene amakhala ku Canada anati: “Kuvala majuzi nthawi yozizira m’malo moyatsa chipangizo chotenthetsera m’nyumba kumathandizanso kuti banja lathu lisamawononge magetsi.”

N’chimodzimodzinso ndi nthawi yotentha. A Rodolfo, a ku Philippines amatsitsa mphamvu ya chipangizo choziziritsira m’nyumba mwawo. Iwo ananena kuti: “Tikamachita zimenezi sitiwononga magetsi komanso ndalama zambiri.”

Muzitseka mawindo ndi zitseko mukamagwiritsa ntchito zipangizo zotenthetsera kapena kuziziritsira m’nyumba. * Ngati tatseka mawindo ndi zitseko potenthetsa kapena kuziziritsa m’nyumba, tingachepetse mphamvu zamagetsi zimene tingawononge. Mwachitsanzo, tikasiya zitseko zosatseka nthawi yozizira ndiye kuti pangafunike mphamvu zambiri zamagetsi kuti titenthetse m’nyumbamo.

Kuwonjezera pa kutseka mawindo ndi zitseko, anthu ena anaika mawindo omwe amathandiza kuti mpweya wotentha usatuluke komanso wozizira usalowe m’nyumba mwawo. Zimenezi zimathandiza kuti azigwiritsa ntchito mphamvu zamagetsi zochepa.

Muzigwiritsa ntchito mababu osafuna mphamvu zambiri zamagetsi. A Jennifer, omwe tawatchula poyamba aja anati: “Panopa timagwiritsa ntchito mababu osafuna mphamvu zambiri zamagetsi.” Ngakhale kuti mababu amenewa amakhala odula, amafuna mphamvu zamagetsi zochepa ndiponso amakhala nthawi yaitali. Zimenezi zimathandiza kuti musamawononge ndalama zambiri polipira magetsi.

MAYENDEDWE

Ngati n’zotheka muzikwera basi. A Andrew, a ku Britain anati: “Ndikamapita kuntchito ndimangokwera njinga kapena sitima.” Buku lina linati: “Ngati aliyense amene wakwera basi atasankha kuyenda pa galimoto yake, pangawonongeke mafuta ochuluka kuwirikiza katatu mafuta amene basi ingagwiritse ntchito.”​—Energy: What Everyone Needs to Know.

Muzikonzeratu maulendo amene mukufuna kuyenda. Ngati mwakonzeratu kuti muyende maulendo ofunika okha, mungachepetse mafuta omwe mungagwiritse ntchito. Izi zingathandize kuti musawononge nthawi komanso ndalama.

A Jethro, a ku Philippines, mwezi uliwonse amaikiratu pambali ndalama zogulira mafuta a galimoto yawo. Iwo anati: “Zimenezi zimathandiza kuti ndiziyenda maulendo ofunika okha.”

ZOCHITA ZA TSIKU NDI TSIKU

Muziyesetsa kuti musamagwiritse ntchito madzi ambiri otentha. Kafukufuku wina anasonyeza kuti, “m’mizinda ya ku Australia, 27 peresenti ya magetsi amene amagwiritsa ntchito pakhomo lililonse imakhala yotenthetsera madzi.”

Popeza kuti madzi otentha amafuna mphamvu zambiri zamagetsi, ndi bwino kugwiritsa ntchito madzi otentha ochepa kuti tisamawononge magetsi ambiri. A Victor, a ku South Africa anati: “Tikamasamba, timayesetsa kugwiritsa ntchito madzi otentha ochepa.” Wasayansi wina, dzina lake Steven Kenway anati: “Kugwiritsa ntchito madzi otentha ochepa n’kothandiza kwambiri chifukwa umagwiritsa ntchito mphamvu zamagetsi zochepa ndipo suwononga ndalama zambiri polipira magetsi ndi madzi.”

Muzizimitsa zipangizo zamagetsi. Zipangizozi ndi monga ma TV, makompyuta ndi zipangizo zina za m’nyumba kuphatikizapo mababu. Zambiri mwa zipangizozi zimatengabe mphamvu ya magetsi ngakhale zitazimitsidwa. Akatswiri ena amati ndi bwino kuzula mawaya ku magetsi n’cholinga choti zipangizozi zizimiretu. A Fernando omwe tawatchula poyamba aja amachita zimenezi. Iwo anati: “Ndimazimitsa mababu komanso kuzula mawaya a zipangizo zomwe sindikugwiritsa ntchito.”

Ngakhale kuti zimene ifeyo patokha tingachite sizingathetseretu mavuto a magetsi ndi mafuta kapena kuwonongeka kwa chilengedwe, n’zotheka kugwiritsa ntchito zinthuzi mwanzeru. Ndipotu zimenezi ndi zomwe anthu padziko lonse akuchita. N’zoona kuti pamafunika zambiri kuti tithe kusamala magetsi ndi mafuta koma tikayesetsa kutero, pamakhala phindu lalikulu. A Valeria, a ku Mexico anati: “Sindiwononga ndalama zambiri ndipo ndimateteza nawo zinthu zachilengedwe.”

^ ndime 10 Muzitsatira mosamala malangizo a chipangizo chanu chotenthetsera kapena kuziziritsira m’nyumba. Mwachitsanzo, zipangizo zina zimafuna kuti muzizigwiritsa ntchito mutatsegula zitseko komanso mawindo.