Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mzinda wa Astana

 ANTHU NDI MAYIKO

Dziko la Kazakhstan

Dziko la Kazakhstan

KALE, anthu a ku Kazakhstan ankakonda kukhala moyo wosamukasamuka. Mpaka pano ambiri mwa anthuwa makamaka amene ali ndi ziweto, amasamukasamukabe. M’nthawi yotentha amakakhala kumapiri komwe amakadyetsa ziweto zawo. Ndiyeno kukayamba kuzizira, amasamukira kuzigwa komwe kumakhala kotentherako.

Masiku ano anthu ambiri a ku Kazakhstan amakhala m’mizinda yotukuka. Komabe amatsatira kwambiri zimene makolo awo akale ankachita pa nkhani ya miyambo, zakudya komanso zinthu zosiyanasiyana zopanga pamanja. Anthuwa amakondanso ndakatulo ndi nyimbo zimene amaimba pogwiritsa ntchito zida zoimbira zakale.

Anthu amene amakonda kusamukasamuka, amapanga nyumba zoyenda nazo ndipo ambiri amaona kuti nyumbazi ndi chizindikiro choti anthu a ku Kazakhstan sawononga  zinthu zachilengedwe. Abusa amakondabe kukhala m’nyumba zimenezi ndipo nthawi zambiri anthu enanso omwe amakhala m’matawuni, amazigwiritsabe ntchito pa zochitika zapadera. Alendo okaona malo amathanso kukagona m’nyumba zimenezi. Mkati mwake mumaoneka mokongola kwambiri chifukwa cha luso limene azimayi a ku Kazakhstan ali nalo lopeta nsalu, kuluka komanso kukonza makapeti.

Mkati mwa kanyumba koyenda nako

Mabanja a ku Kazakhstan amene amakhala m’madera a kumidzi amakonda kwambiri mahatchi. Anthuwa ali ndi mayina pafupifupi 21 otchulira hatchi ndipo dzina lililonse lili ndi tanthauzo lake. Ndipo pali mawu oposa 30 ofotokozera mitundu yosiyanasiyana ya ubweya wa mahatchiwa. Iwo amaona kuti akapatsidwa hatchi ndiye kuti apatsidwa mphatso yamtengo wapatali kwambiri. Komanso anyamata amayamba ali aang’ono kuphunzira kukwera mahatchi.

Pa chakudya chimene anthu a ku Kazakhstan amadya sipalephera nyama. Nthawi zambiri nyamayi imakhala yopanda zonunkhiritsa kapena zokometsera. Amakonda chakumwa chotchedwa koumiss, chopangidwa kuchokera ku mkaka wa hatchi ndipo amati chakumwachi n’chopatsa thanzi. Amakondanso shubat, chakumwa chowawasirapo chopangidwa kuchokera ku mkaka wa ngamila.

Ofesi ya Mboni za Yehova yomwe ili ku Almaty imalandira alendo amene apita kukaona malo pa ofesiyo.

Kambuku wa kumalo ozizira kwambiri, m’nthawi yotentha amakhala m’mapiri a ku Kazakhstan