Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pa Nthawi ya Tsoka, Timathandizana Chifukwa cha Chikondi

Pa Nthawi ya Tsoka, Timathandizana Chifukwa cha Chikondi

Pa nthawi yamavuto, a Mboni za Yehova amathandizana komanso amathandiza anthu ena omwe si a Mboni. Iwo amachita zimenezi chifukwa cha chikondi chomwe ndi chizindikiro cha Akhristu oona.​—⁠Yohane 13:⁠35.

M’munsimu muli nkhani zochepa chabe zosonyeza zimene a Mboni za Yehova achita pa nkhaniyi kwa miyezi yoposa 12, kuyambira mu 2011 mpaka chapakatikati pa chaka cha 2012. M’nkhanizi simunafotokozedwe zimene a Mboni za Yehova anachita pothandiza anthuwo mwauzimu komanso m’njira zina zapadera. Ofesi ya nthambi imasankha makomiti amene amayendetsa ntchito yothandiza anthuyi. Komanso mipingo ya m’dera limene lakhudzidwa ndi tsokalo imathandiza nawo pa ntchitoyo.

Japan

Japan: Pa March 11, 2011, panachitika chivomerezi champhamvu kwambiri komanso tsunami m’dera lakumpoto m’dziko la Japan ndipo anthu masauzande ambirimbiri anakhudzidwa. Anthu a Mboni za Yehova padziko lonse lapansi anapereka mowolowa manja zinthu monga ndalama ndi katundu wawo kuti zikathandizire anthu amene anakhudziwawo. Tangoonerani vidiyo yosonyeza ntchito yothandiza anthu amene anakhudzidwa ndi tsokalo ku Japan.

Brazil: Anthu ambirimbiri anafa chifukwa cha madzi osefukira, kukokoloka kwa nthaka komanso chifukwa cha kuchuluka kwa matope. Pofuna kuthandiza pa ngoziyi, a Mboni za Yehova anatumiza katundu wosiyanasiyana kudera limene linakhudzidwalo. Iwo anatumiza chakudya chosawonongeka msanga cholemera matani 42, mabotolo a madzi akumwa okwana 20,000, matani 10 a zovala, matani 5 a zipangizo zogwiritsira ntchito poyeretsa komanso mankhwala akuchipatala ndi zina zambiri.

Congo (Brazzaville): Bomba linaphulika kumalo ena otayira zida za nkhondo ndipo nyumba 4 za anthu a Mboni za Yehova zinawonongeka moti sizinakakonzedwanso komanso nyumba zina 28 za a Mboni ena zinawonongeka koma moti n’kukonzedwanso. Anthu a Mboni za Yehova anathandiza anthu amene anakhudzidwa ndi ngoziyo powapatsa chakudya ndi zovala. Komanso anthu ena a Mboni a m’deralo anatenga anthu ena amene nyumba zawo zinawonongeka n’kumakhala nawo.

Congo (Kinshasa): Gulu la Mboni za Yehova linapereka mankhwala kwa anthu amene anakhudzidwa ndi mliri wa kolera. Kuwonjezera pamenepa, anthu ena amene anakhudzidwa ndi kusefukira kwa madzi anapatsidwa zovala. Komanso anthu amene anali m’misasa ya anthu othawa kwawo anapatsidwa thandizo la mankhwala a kuchipatala, mbewu zoti adzale ndiponso zovala zolemera matani ambirimbiri.

Venezuela: Mvula yamphamvu inachititsa kuti nthaka ikokoloke komanso madzi asefukire. Izi zitachitika, makomiti othandiza anthu pangozi anathandiza anthu a Mboni 288 amene anakhudzidwa. Makomitiwa anathandizanso pomanga nyumba zatsopano zoposa 50. Komanso makomitiwa anathandiza anthu amene nyumba zawo zinali m’mbali mwa nyanja ya Valencia, omwe akanakhudzidwa ndi kusefukira kwa nyanjayo.

Philippines

Philippines: Mvula yamphamvu inachititsa kuti madzi asefukire m’madera ena a dzikoli. Ofesi ya nthambi inatumiza zakudya ndi zovala kwa anthu amene anakhudzidwa ndi tsokalo, ndipo madzi ataphwera, anthu a Mboni a m’deralo anathandiza pa ntchito yochotsa matope m’nyumba za m’deralo.

Canada: Moto wolusa utabuka m’nkhalango ku Alberta, mpingo wa Mboni za Yehova wa m’tauni ya Slave Lake unalandira zopereka zambiri ndithu kuchokera kumipingo ina ya m’deralo kuti zithandize pa ntchito yokonzanso zinthu zimene zinawonongeka ndi motowo. Zoperekazo zinali zambiri ndithu ndipo mpingowo unagwiritsa ntchito ndalama zosakwana hafu ya ndalama zonse zimene unalandira. Choncho mpingowo unapereka ndalama zotsalazo kuti zithandizire anthu ena amene angakhudzidwe ndi masoka a mwadzidzidzi m’madera ena padziko lapansili.

Côte d’Ivoire: Zinthu monga katundu, malo ogona ndiponso mankhwala a kuchipatala zinkaperekedwa kwa anthu ovutika m’dzikoli. Anthu ankapatsidwa zinthuzi nkhondo isanayambe, itayamba komanso itatha.

Fiji: Mvula yoopsa yomwe inagwa m’dzikoli inachititsa kuti madzi asefukire m’madera ambiri ndipo mabanja 192 a Mboni za Yehova anakhudzidwa. Ambiri mwa mabanja amenewa mbewu zawo zomwe zinali m’minda zinawonongekeratu ndipo anthuwo anasowa mtengo wogwira chifukwa amadalira mbewuzo kuti apeze chakudya komanso ndalama. Anthuwa anathandizidwa popatsidwa zakudya komanso zinthu zina zofunikira.

Ghana: Anthu omwe anakhudzidwa ndi madzi osefukira m’chigawo chakum’mawa cha dzikoli anapatsidwa zakudya, mbewu ndi malo ogona.

United States: Mphepo yamkuntho inawononga nyumba 66 za anthu a Mboni za Yehova m’madera atatu osiyanasiyana. Kuwonjezera pamenepa, mphepoyo inaphwasuliratu nyumba zina 12 za anthu a Mboni. Ngakhale kuti nyumba zambiri zimene zinawonongedwa zinali ndi inshulansi, anthu ena a Mboni anapereka ndalama zothandizira kukonza nyumba za Akhristu anzawo zimene zinawonongekazo.

Argentina: Anthu a mipingo ya Mboni za Yehova anathandiza anthu a m’dera lakum’mwera kwa dzikoli, omwe nyumba zawo zinawonongedwa ndi phulusa limene linatuluka paphiri lina lomwe linaphulika.

Mozambique: Anthu oposa 1,000 omwe ankavutika ndi chilala anagawiridwa chakudya.

Nigeria: Anthu 12 a Mboni za Yehova amene anavulala pa ngozi yoopsa kwambiri ya basi anathandizidwa ndi ndalama. Anthu enanso amene analandira thandizo m’dzikoli ndi amene amakhala m’dera lakumpoto, omwe ankavutika chifukwa cha nkhondo ya pakati pa anthu osiyana mitundu komanso zipembedzo.

Benin: Anthu omwe anakhudzidwa ndi kusefukira kwa madzi anathandizidwa ndi zinthu ngati zovala, maneti odzitetezera ku udzudzu, madzi akumwa ndiponso malo ogona.

Dominican Republic

Dominican Republic: Mvula yamkuntho yotchedwa Hurricane Irene itachitika, anthu a m’mipingo ya m’dzikoli anathandiza pa ntchito yokonzanso nyumba komanso anapereka zinthu zothandizira anthu amene anakhudzidwawo.

Ethiopia: Ndalama zinatumizidwa kuti zikathandizire anthu a m’madera awiri amene anakhudzidwa ndi chilala komanso anthu a m’dera lina amene anakhudzidwa ndi vuto la kusefukira kwa madzi.

Kenya: Ndalama zinatumizidwa kuti zithandize anthu amene anakhudzidwa ndi chilala.

Malawi: Ndalama zinatumizidwa kuti zithandize anthu amene amakhala kumalo a anthu othawa kwawo otchedwa Dzaleka.

Nepal: Matope omwe ankakokoloka anawononga kwambiri nyumba ya mayi wina wa Mboni za Yehova. Munthuyo anathandizidwa pomumangira nyumba ina yongoyembekezera komanso anthu a mumpingo wake anamuthandiza kwambiri ndi zinthu zina zofunikira.

Papua New Guinea: Zigawenga zinatentha nyumba 8 za anthu a Mboni za Yehova. Izi zitachitika, panakonzedwa dongosolo lothandiza anthuwo kumanganso nyumbazo.

Romania: Madzi osefukira anawononga nyuma za anthu ena a Mboni. Anthuwo anathandizidwa kuti nyumbazo zimangidwenso.

Mali: Ndalama zinatumizidwa kuchokera ku Senegal, kuti zithandizire anthu amene amavutika ndi njala imene inabwera chifukwa cha chilala.

Sierra Leone: Madokotala a Mboni za Yehova ochokera ku France anapereka thandizo la mankhwala kwa anthu a Mboni za Yehova amene akukhala m’madera amene munkachitika nkhondo.

Thailand: Madzi osefukira anawononga zinthu kwambiri m’madera ochuluka. Anthu ambiri anadzipereka n’kuthandiza anthu amene anakhudzidwawo moti anakonzanso nyumba 100 komanso Nyumba za Ufumu 6 zimene zinawonongeka.

Czech Republic: Madzi osefukira atawononga nyumba zambiri ku Czech Republic, anthu a Mboni ochokera m’dziko loyandikana nalo la Slovakia anathandiza kwambiri anthu amene anakhudzidwawo.

Sri Lanka: Ntchito yaikulu yothandiza anthu amene anakhudzidwa ndi tsunami yatha tsopano.

Sudan: Anthu a Mboni za Yehova omwe athawa kwawo chifukwa cha nkhondo imene ikuchitika m’dzikoli anatumiziridwa zakudya, zovala, nsapato ndiponso mapepala apulasitiki.

Tanzania: Madzi owopsa atasefukira m’dera lina, katundu wa mabanja 14 anawonongeka. Mipingo ya m’deralo inatumiza zovala ndi ziwiya zina za m’nyumba. Mipingoyo inathandizanso pomanga nyumba ina imodzi.

Zimbabwe: M’dera lina la m’dzikoli munagwa chilala chomwe chinachititsa njala yoopsa. Anthu omwe anakhudzidwa ndi njalayi anatumiziridwa zakudya ndi ndalama.

Burundi: Anthu othawa kwawo akupatsidwa zinthu zowathandiza pamoyo wawo, kuphatikizapo thandizo la mankhwala.