Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

GALAMUKANI! Na. 5 2017 | Zimene Tingachite Kuti Tipulumuke Pakachitika Ngozi Zadzidzidzi

N’chifukwa chiyani tiyenera kukonzekera ngozi zadzidzidzi?

Baibulo limati: “Wochenjera amene waona tsoka amabisala. Koma anthu osadziwa zinthu amene amangopitabe amalangidwa.”—Miyambo 27:12.

Magaziniyi ikufotokoza zomwe tingachite ngozi yadzidzidzi isanachitike, ikamachitika komanso pambuyo poti yachitika.

 

NKHANI YAPACHIKUTO

Zimene Tingachite Kuti Tipulumuke Pakachitika Ngozi Zadzidzidzi

Kutsatira mfundozi kungapulumutse inuyo ndi anthu ena.

Zimene Muyenera Kudziwa Zokhudza Magetsi ndi Mafuta

Ganizirani njira zitatu zimene zingatithandize kugwiritsa ntchito bwino magetsi ndi mafuta tikakhala kunyumba kwathu, pa nkhani ya mayendedwe komanso pa zochita za tsiku ndi tsiku.

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Nkhondo

Kale Yehova ankalola kuti Aisiraeli azimenya nkhondo. Koma kodi zimenezi zikusonyeza kuti Mulungu amalola kuti anthu azimenyanso nkhondo masiku ano?

MFUNDO ZOTHANDIZA MABANJA

Kodi Mumakonda Masewera Oika Moyo Pangozi?

Achinyamata ambiri amafuna kudziwa ngati angakwanitse kuchita masewera enaake ngakhale kuti nthawi zina zingaike moyo wawo pangozi. Kodi nanunso zimenezi zimakuchitikirani?

ANTHU NDI MAYIKO

Dziko la Kazakhstan

Kale, anthu a ku Kazakhstan ankakonda kusamukasamuka komanso kukhala m’nyumba zotha kuyenda nazo. Kodi zimene anthuwa amachita masiku ano zikusonyeza bwanji kuti amakondabe chikhalidwe cha makolo awo?

KODI ZINANGOCHITIKA ZOKHA?

Zigoba za Nkhono Zam’madzi

Zigobazi zimakhala zolimba kwambiri moti zimatha kuteteza nkhono zomwe zili mkati mwake.

Zina zimene zili pawebusaiti

N’chifukwa Chiyani a Mboni za Yehova Sapita Kunkhondo?

A Mboni za Yehova ndi odziwika bwino padziko lonse kuti amakana kupita kunkhondo. Werengani nkhaniyi kuti mudziwe chifukwa chake sitipita kunkhondo.

Pa Nthawi ya Tsoka, Timathandizana Chifukwa cha Chikondi

M’mayiko ambirimbiri, a Mboni za Yehova amathandiza anthu amene ali m’mavuto.