Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Nkhondo

Nkhondo

Kale Yehova ankalola kuti Aisiraeli azimenya nkhondo. Koma kodi zimenezi zikusonyeza kuti Mulungu amalola kuti anthu azimenyanso nkhondo masiku ano?

N’chifukwa chiyani Aisiraeli ankapita kunkhondo?

ZIMENE ANTHU ENA AMANENA

 

Aisiraeli ankalambira “mulungu wokonda nkhondo” amene ankakonda kukhetsa magazi.

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

 

Mitundu imene Aisiraeli anaigonjetsa inkachita makhalidwe oipa kwambiri monga kugonana ndi nyama, kugonana pachibale komanso kupereka ana nsembe. Mulungu anachenjeza mitunduyo kwa zaka zambiri kuti isinthe, ndipo kenako anati: “Mitundu imene ndikuichotsa pamaso panu yadzidetsa ndi zonse zimenezi.”​—Levitiko 18:21-25; Yeremiya 7:31.

“Yehova Mulungu wanu akukankhira mitundu iyi kutali ndi inu, kwenikweni chifukwa cha kuipa kwawo.”​—Deuteronomo 9:5.

Kodi masiku ano Mulungu amathandiza gulu linalake pa nkhondo?

MWINA MUMAONA KUTI

 

Pa mikangano yambiri imene imachitika, atsogoleri achipembedzo amanena kuti Mulungu ali kumbali ya gulu lawo. Buku lina linanena kuti: “Zipembedzo zakhala zikutengapo mbali pa nkhondo zonse zimene zakhala zikuchitika m’mbuyomo.”​—The Causes of War.

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

 

Mulungu salola kuti Akhristu azimenyana ndi adani awo. Mtumwi Paulo analembera Akhristu anzake kuti: “Ngati ndi kotheka, khalani mwamtendere ndi anthu onse, monga mmene mungathere. Musabwezere choipa.”​—Aroma 12:18, 19.

Yesu sanatumize otsatira ake kunkhondo, m’malomwake anawauza kuti: “Pitirizani kukonda adani anu ndi kupempherera amene akukuzunzani, kuti musonyeze kuti ndinudi ana a Atate wanu wakumwamba.” (Mateyu 5:44, 45) Ngakhale anthu amtundu wawo atakhala kuti amamenya nkhondo, Akhristu sayenera kumenya nawo nkhondoyo chifukwa sali “mbali ya dzikoli.” (Yohane 15:19) Popeza kuti Mulungu amafuna kuti anthu a mitundu yonse azikonda adani awo komanso asamakhale kumbali ya dziko, ndiye kuti sangathandize gulu linalake kuti lipambane pa nkhondo.

“Ufumu wanga suli mbali ya dziko lino. Ufumu wanga ukanakhala mbali ya dziko lino, atumiki anga akanamenya nkhondo kuti ndisaperekedwe kwa Ayuda. Koma ufumu wanga si wochokera pansi pano ayi.”​—Yohane 18:36.

 Kodi nkhondo idzatha?

ZIMENE ANTHU ENA AMANENA

 

Nkhondo sitingaipewe. Buku lina linanena kuti: “Nkhondo idzakhalapo mpaka kalekale ndipo n’zokayikitsa kwambiri ngati mtsogolomu anthu angadzakhale pamtendere.”​—War and Power in the 21st Century.

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

 

Mtsogolomu nkhondo idzatha chifukwa palibe azidzalakalaka kumenyana ndi mnzake. Ufumu wa Mulungu, womwe ndi boma limene likulamulira kumwamba, udzawononga zida zonse zankhondo ndipo udzathandiza anthu kuti azichita zinthu mwamtendere. Baibulo limatitsimikizira kuti Mulungu “adzakonza zinthu zokhudza anthu ochokera m’mitundu yamphamvu yakutali. Iwo adzasula malupanga awo kuti akhale makasu a pulawo, ndi mikondo yawo kuti ikhale zida zosadzira mitengo. Mtundu wa anthu sudzanyamula lupanga kuti umenyane ndi mtundu unzake, ndipo anthuwo sadzaphunziranso nkhondo.”​—Mika 4:3.

Baibulo limaphunzitsa kuti Ufumu wa Mulungu ukadzayamba kulamulira, sikudzakhalanso maboma ongochita zofuna zawo zokha, okhazikitsa mfundo zopanda chilungamo komanso olimbikitsa kuti anthu azisankhana mitundu. Zimenezi zidzachititsa kuti padzikoli pasakhalenso nkhondo. Mulungu akulonjeza kuti: “Sizidzavulazana kapena kuwonongana . . . chifukwa dziko lapansi lidzadzaza ndi anthu odziwa Yehova ngati mmene madzi amadzazira nyanja.”​—Yesaya 11:9.

“Akuletsa nkhondo mpaka kumalekezero a dziko lapansi. Wathyola uta ndi kuduladula mkondo. Ndipo watentha magaleta pamoto.”​—Salimo 46:9.