GALAMUKANI! February 2014 | Kodi Mungatani Kuti Muzigwiritsa Ntchito Bwino Nthawi?

Nthawi ikangodutsa sibwereranso. Werengani nkhaniyi kuti mudziwe njira 4, zimene zathandiza anthu ena kugwiritsa ntchito bwino nthawi yawo pa zinthu zofunika.

Zochitika Padzikoli

Nkhani zake: kuzembetsa minyanga ya njovu ku Malaysia, anthu sakukhulupiriranso tchalitchi ku Italy, matenda ku Africa ndi ana otchova juga ku Australia.

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Kukhulupirira Mizimu

Anthu ambiri amaganiza kuti n’zotheka kulankhula ndi akufa, kodi Baibulo limati chiyani pa nkhaniyi?

NKHANI YAPACHIKUTO

Kodi Mungatani Kuti Muzigwiritsa Ntchito Bwino Nthawi?

Njira imodzi imene ingakuthandizeni kuti muzigwiritsa ntchito bwino nthawi yanu ndi kuonanso bwinobwino zinthu zimene mumachita pa moyo wanu. Kodi zinthu zimenezi ndi ziti?

KUCHEZA NDI ANTHU

Wasayansi Akufotokoza za Chikhulupiriro Chake

Zimene Dr. Hans Kristian Kotlar anaphunzira zokhudza chitetezo cha m’thupi, zinapangitsa kuti ayambe kufufuza zokhudza mmene moyo unayambira. Kodi zimene anaphunzira m’Baibulo zinayankha bwanji mafunso ake?

TIONE ZAKALE

Constantine

Werengani kuti mudziwe mmene zimene Constantine anachita pa nkhani ya chipembedzo ndi ndale, zinakhudzira zomwe zipembedzo zambiri zimakhulupirira masiku ano.

MFUNDO ZOTHANDIZA MABANJA

Ngati Mwana Wanu Wamkazi Akuvutika Maganizo

Atsikana ambiri amavutika ndi zimene zimachitika akamakula. Kodi makolo angawathandize bwanji akamavutika maganizo chifukwa cha zimenezi?

KODI ZINANGOCHITIKA ZOKHA?

Kuwala kwa Ziphaniphani za Mtundu Winawake

Kodi tizilombo timeneti tathandiza bwanji asayansi kuganiza zopanga zipangizo zowala bwino?

Zina zimene zili pawebusaiti

Kodi Ndimangokhalira Kuganizira za Maonekedwe Anga?

Kodi mungatani kuti muzisangalala ndi mmene mumaonekera?

Kodi Mnzako Weniweni Ungamudziwe Bwanji?

N’zosavuta kupeza anzanu amene sangakuthandizeni, koma kodi mungapeze bwanji mnzanu weniweni?

Kodi Ndiyenera Kudziwa Zotani pa Nkhani Yotumizirana Mameseji ndi Zinthu Zina Zolaula?

Kodi munthu wina amakukakamizani kuti mumutumizire zolaula? Kodi kutumizirana zolaula kuli ndi mavuto otani? Kodi ndi kukopana basi?

Mose Anakulira ku Iguputo

N’chifukwa chiyani amayi a Mose anabisa mwana wawoyu m’mbali mwa mtsinje wa Nailo? Werengani nkhaniyi kuti mudziwe zambiri zokhudza Mose, makolo ndi achibale ake, komanso mwana wamkazi wa Farao.