Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 KODI ZINANGOCHITIKA ZOKHA?

Kuwala kwa Ziphaniphani za Mtundu Winawake

Kuwala kwa Ziphaniphani za Mtundu Winawake

PALI ziphaniphani za mtundu wina zimene mbali yake imene imawala imakutidwa ndi tizinthu tooneka ngati mamba a nsomba. Zinthu zimenezi zimapangitsa kuti ziphaniphanizi ziziwala kwambiri. *

Zinthu zooneka ngati mamba a nsomba

Taganizirani izi: Akatswiri ofufuza zinthu apeza kuti tizinthu tooneka ngati mambati n’tosanjikizana ndipo timakhala totukuka pang’ono mbali imodzi. Zimenezi zimachititsa kuti ziphaniphanizi ziziwala kwambiri kuposa mmene zikanamawalira zikanakhala kuti tinthuti sitotukuka mbali imodzi.

Kodi kudziwa zimenezi kungathandize akatswiri kupanga zipangizo, monga ma TV ndi makompyuta owala bwino? Kuti adziwe ngati zingathandizedi, akatswiri anatenga tizinthu tofanana ndi timene timakuta mbali yowala ya ziphaniphani, n’kukuta mbali imene imapangitsa kuti zipangizozi ziziwala. Zotsatira zake zinali zoti zipangizozi zinkatulutsa kuwala kooneka bwino kwambiri kuposa poyamba. Katswiri wina wa sayansi ya kapangidwe ka zinthu, dzina lake Annick Bay, anati: “Chinthu chofunika kwambiri chimene tazindikira pa kafukufukuyu n’choti, tikhoza kuphunzira zambiri poona zimene zimachitika m’chilengedwe.”

Kodi inuyo mukuganiza bwanji? Kodi zinangochitika zokha kuti ziphaniphanizi ziziwala motere, kapena pali winawake amene anazilenga m’njira yoti ziziwala chonchi?

^ ndime 3 Akatswiri a sayansi sanatulukire mitundu yonse ya ziphaniphani za m’gulu limeneli.