Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

 ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Kukhulupirira Mizimu

Kukhulupirira Mizimu

Kodi n’kulakwa kuyesa kulankhulana ndi anthu amene anamwalira?

“Musatembenukire kwa olankhula ndi mizimu . . . ndi kudetsedwa nawo.”—Levitiko 19:31.

ZIMENE ANTHU AMANENA

Anthu amafuna kutsimikizira kuti omwe anamwalira sakuvutika. Ndiye amaona kuti palibe cholakwika kulankhula nawo kudzera mwa asing’anga kapena olankhula ndi mizimu. Iwo amaganiza kuti kuchita zimenezi kungachititse kuti asamade nkhawa podziwa kuti munthuyo sakuvutika.

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Kukhulupirira mizimu kunayamba kalekale, koma Baibulo limanena momveka bwino kuti kuchita zimenezi n’kolakwika. Mwachitsanzo, Yehova Mulungu anapereka lamulo loletsa Aisiraeli kuchita zimenezi. Iye anati: “Pasapezeke munthu . . . aliyense wofunsira kwa wolankhula ndi mizimu . . . kapena aliyense wofunsira kwa akufa. Pakuti aliyense wochita zimenezi ndi wonyansa kwa Yehova.” (Deuteronomo 18:10-12) Baibulo limanenanso kuti amene amachita zilizonse zokhudzana ndi kukhulupirira mizimu, “sadzalowa mu ufumu wa Mulungu.”—Agalatiya 5:19-21.

 Kodi akufa angatichitire chilichonse, chabwino kapena choipa?

“Amoyo amadziwa kuti adzafa, koma akufa sadziwa chilichonse.”Mlaliki 9:5.

ZIMENE ANTHU AMANENA

Ambiri amakhulupirira kuti munthu akafa mzimu wake umapitirizabe kukhala ndi moyo kwinakwake. Choncho amaganiza kuti angathe kulankhula ndi munthuyo kuti adziwe zinazake kapena pofuna kumusangalatsa kuti asawachitire zoipa.

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

“Amoyo amadziwa kuti adzafa, koma akufa sadziwa chilichonse . . . Chikondi chawo, chidani chawo ndiponso nsanje yawo [zimene ankachita ali moyo] zatha kale.” (Mlaliki 9:5, 6) Choncho Baibulo limaphunzitsa kuti munthu akafa, ndiye kuti wafa basi ndipo sangalambire Mulungu kapena kuchita chilichonse. Lemba la Salimo 115:17 limati: “Akufa satamanda [Mulungu], ngakhalenso aliyense wotsikira kuli chete.”

Kodi si zoona kuti anthu olankhula ndi mizimu amanena zoona nthawi zina?

“Kodi tizifunsira kwa anthu akufa kuti athandize anthu amoyo?”Yesaya 8:19.

ZIMENE ANTHU AMANENA

Ena amanena kuti anthu olankhula ndi mizimu amatha kunena zinthu zomwe angadziwe ndi munthu womwalirayo, anthu a m’banja lake kapena anzake okha basi.

ZIMENE BAIBULO LIMENENA

Lemba la 1 Samueli chaputala 28 limanena za mfumu Sauli amene anaphwanya lamulo la Mulungu pofunsira kwa mayi wolankhula ndi mizimu. Iye anauza mayiyo kuti akufuna kulankhula ndi Samueli yemwe anali atamwalira. Koma kodi analankhuladi ndi Samueli? Ayi. Mayiyu ankalankhula ndi chiwanda chimene chinkayerekezera kuti ndi Samueli.

Chiwanda chimenechi chinkatumikira Satana yemwe ndi “tate wake wa bodza.” (Yohane 8:44) Koma kodi n’chifukwa chiyani mizimu yoipa kapena kuti ziwanda, zimachita zinthu zomwe zimapangitsa anthu kuganiza kuti akufa amapitirizabe kukhala ndi moyo? Cholinga chawo ndi kuipitsa mbiri ya Mulungu komanso kuti anthu asamakhulupirire Baibulo.—2 Timoteyo 3:16.

Kodi zimene takambirana m’nkhaniyi zikusonyeza kuti palibe chiyembekezo chilichonse kwa anthu amene anamwalira? Ayi, chifukwa Baibulo limalonjeza kuti anthu amene ‘akugona’ m’manda, kapena kuti omwe anamwalira, adzaukitsidwa. * (Yohane 11:11-13; Machitidwe 24:15) Panopa, Baibulo limatitsimikizira kuti anthu amene anamwalira sakuvutika mwanjira iliyonse.

^ ndime 16 Kuti mudziwe zambiri, werengani mutu 7, wakuti “Chiyembekezo Chotsimikizika Chokhudza Okondedwa Anu Amene Anamwalira” m’buku lakuti, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?