GALAMUKANI! October 2013 | Zinthu Zitatu Zimene Sitingagule ndi Ndalama

Kukhala ndi chuma kungatilepheretse kuganizira zinthu zofunika kwambiri pa moyo wathu, zomwe sitingagule ndi ndalama. Tiyeni tione zitsanzo zitatu.

Zochitika Padzikoli

Nkhani zake ndi monga: Kuchuluka kwa magalimoto m’misewu ya ku China, kuphwanya ufulu wa chipembedzo ku Armenia, kuopsa kogwiritsa ntchito malo ochezera a pa Intaneti ku Japan ndi zina.

MFUNDO ZOTHANDIZA MABANJA

Zimene Mungachite Ngati Mumacheza Kwambiri ndi Munthu Amene si Mwamuna Kapena Mkazi Wanu

Mukamacheza kwambiri ndi munthu yemwe si mwamuna kapena mkazi wanu, kodi mumaona kuti palibe vuto lina lililonse? Ngati mumaona choncho, werengani nkhaniyi kuti muone mfundo za m’Baibulo zosonyeza kuti maganizo amenewo ndi oopsa.

KUCHEZA NDI ANTHU

Wasayansi Akufotokoza za Chikhulupiriro Chake

Kodi n’chiyani chinapangitsa katswiri wina kusintha zimene ankakhulupirira pa nkhani ya mmene moyo unayambira komanso n’chiyani chinamutsimikizira kuti Baibulo linalembedwa ndi Mulungu?

NKHANI YAPACHIKUTO

Zinthu Zitatu Zimene Sitingagule ndi Ndalama

Ndalama zimatithandiza kuti tigule zinthu zofunika pa moyo wathu koma zinthu zimene zingatipangitse kukhala ndi moyo wosangalala sizingagulidwe ndi ndalama.

Zimene Muyenera Kudziwa Ponena za Matenda a Khunyu

Anthu ambiri sawamvetsa matenda a khunyu. Werengani nkhaniyi kuti mudziwe zinthu zina zomwe muyenera kudziwa ponena za matendawa

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Kuvutika Maganizo

Werengani nkhaniyi kuti mudziwe chifukwa chake anthu amadwala matenda ovutika maganizo komanso mmene Baibulo lingawathandizire.

KODI ZINANGOCHITIKA ZOKHA?

Khutu Lamphamvu la Bwamnoni

Bwamnoniyu ali ndi kakhutu kakang’ono kwambiri koma kamagwira ntchito ngati khutu la munthu. Kodi zimene akatswiri apeza zokhudza khutu la bwamnoniyu zingathandize bwanji asayansi komanso akatswiri opanga zinthu?

Zina zimene zili pawebusaiti

Kodi Ndingatani Anthu Ena Akamandivutitsa?

Anthu ambiri amene akuvutitsidwa amaona kuti palibe chimene angachite. Nkhaniyi ikufotokoza zimene mungachite kuti anthu asiye kukuvutitsani.

Kodi Ndimangokhalira Kuganizira za Maonekedwe Anga?

Kodi mungatani kuti muzisangalala ndi mmene mumaonekera?

Kodi Ndingatani Ngati Ndikudwala Matenda Aakulu?​—Gawo 1

Achinyamata 4 akufotokoza zimene zikuwathandiza kupirira matenda awo kuti asamangokhalira kudandaula.

Zimene Achinyamata Amanena pa Nkhani ya Maonekedwe

N’chifukwa chiyani achinyamata ambiri zimawavuta kuti azisangalala ndi mmene amaonekera? N’chiyani chingawathandize pa nkhaniyi?

Maloto a Wophika Mkate

Koperani ndi kusindikiza zithunzizi ndiyeno onani zinthu zitatu zimene zikusiyana pa zithunzi ziwirizo.