Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 KODI ZINANGOCHITIKA ZOKHA?

Khutu Lamphamvu la Bwamnoni

Khutu Lamphamvu la Bwamnoni

KU SOUTH AMERICA kuli mtundu winawake wa bwamnoni ndipo ali ndi kakhutu kakang’ono kwambiri koma kamagwira ntchito ngati khutu la munthu. Bwamnoniyu amatha kusiyanitsa phokoso la zinthu zosiyanasiyana ngakhale zili kutali. Mwachitsanzo, amatha kusiyanitsa kulira kwa bwamnoni wina ndi kwa mleme umene ukusaka, zomwe nthawi zambiri zimamveka mofanana.

KHUTU LA BWAMNONI

Taganizirani izi: Makutu a bwamnoniyu ali pa miyendo yake iwiri yakutsogolo. Mofanana ndi mmene khutu la munthu limagwirira ntchito, khutu la bwamnoniyu likamva phokoso, limatumiza uthenga ku ubongo zomwe zimathandiza bwamnoniyu kudziwa kuti phokosolo ndi la chiyani. Koma chaposachedwapa, asayansi atulukira kuti mkati mwa khutu la bwamnoniyu muli kanthu kenakake kokhala ngati kabaluni ndipo mkati mwake muli timadzi. Kabalunika ndi kamene kamathandiza kuti bwamnoniyu azimva kwambiri.

Pulofesa wina wa pa yunivesite ya Bristol’s School of Biological Sciences ku United Kingdom, dzina lake Daniel Robert, ananena kuti potengera khutu la bwamnoniyu, asayansi akhoza “kupanga tizipangizo tothandiza anthu ovutika kumva tating’ono koma tamphamvu kwambiri kuposa timene akupanga masiku ano.” Asayansi akuona kuti zikhoza kuthandizanso makampani opanga makina a kuchipatala, otha kumva komanso kujambula mkati mwa thupi la munthu, amphamvu kwambiri kuposa omwe akupanga masiku ano.

Kodi inuyo mukuganiza bwanji? Kodi zinangochitika zokha kuti bwamnoniyu akhale ndi khutu lomva kwambiri chonchi?