Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Zochitika Padzikoli

Zochitika Padzikoli

Padziko Lonse

Bungwe Loona za Umoyo pa Dziko Lonse lanena kuti kupuma mpweya wochokera m’mainjini omwe amagwiritsa ntchito dizilo “kukuyambitsa matenda a khansa ya m’mapapo” komanso kukhoza kuyambitsa khansa ya m’chikhodzodzo.

Antarctica

Akatswiri ofukula zinthu zakale apeza tinjere ting’onoting’ono ta mtengo wa mgwalangwa tomwe tinakwiririka pansi pa nyanja. Iwo akukhulupirira kuti umenewu ndi umboni wakuti m’mbuyomu, ku Antarctic kunkapezeka mitengo ya mgwalangwa komanso mitengo ina yomwe imamera m’madera otentha. Ambiri akukhulupirira kuti zaka mamiliyoni ambiri m’mbuyomu, ku Antarctic sikunkazizira ngati mmene kumazizira masiku ano m’nyengo yozizira komanso madzi sankaundana. Akuganizanso kuti nyengo ya ku Antarctic ndi ku Arctic siinali yosiyana kwambiri ndi nyengo ya m’madera ena padzikoli.

Ireland

Bungwe lina la Ansembe a Katolika la ku Ireland linachita kafukufuku m’chaka cha 2012 kwa akatolika a ku Ireland. Kafukufukuyu anasonyeza kuti anthu 87 pa 100 alionse amaona kuti ansembe ayenera kukwatira ndipo anthu 77 pa 100 alionse amaona kuti akazi ayenera kuloledwa kukhala ansembe.

Sahara ndi Asia

Kafukufuku amene anachitika pofuna kuona mmene mankhwala a malungo amagwirira ntchito anasonyeza kuti m’madera ena, mankhwala a malungo anali opanda mphamvu kapena osagwira ntchito, zomwe zimachititsa kuti munthu akamwa mankhwalawa asachire. Mwachitsanzo, kum’mwera chakumadzulo kwa Asia, 36 peresenti ya mankhwala amene anayesedwa anapezeka kuti ndi opanda mphamvu ndipo kum’mwera kwa Sahara, ku Africa, anapeza kuti 20 peresenti ya mankhwala a malungo analinso opanda mphamvu.

El Salvador

Akuluakulu a boma la El Salvador analengeza kuti tsiku lina cha mkatikati mwa April 2012, panalibe munthu amene anaphedwa m’dzikolo. Aka n’koyamba kukhala tsiku lonse munthu osaphedwa m’zaka pafupifupi zitatu. M’chaka cha 2011, anthu 69 pa 100,000, alionse anaphedwa pa ziwawa zimene zinayamba chifukwa cha anthu amene anagwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo. Chiwerengero chimenechi n’chokwera kwambiri poyerekeza ndi mayiko ena.