GALAMUKANI! June 2013 | Kodi N’kulakwa Kugula Katundu Wambirimbiri?

Mu nkhani zimenezi tidziwa kuipa kogula zinthu zambirimbiri komanso tidziwa zimene tingachite kuti tisamangogula zinthu mwachisawawa.

Zochitika Padzikoli

Nkhani zake ndi monga: kuipa kwa utsi wa dizilo, mankhwala a malungo achinyengo akupezeka ku Africa ndi ku Asia.

MFUNDO ZOTHANDIZA MABANJA

Zimene Mwamuna ndi Mkazi Angachite Kuti Asamasiye Kulankhulana Akasemphana Maganizo

Kodi chimachititsa n’chiyani kuti mwamuna ndi mkazi wake asiye kulankhulana, nanga n’chiyani chingathandize kuti athetse kusamvana?

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Satana

Kodi Satana ndi uchimo umene umakhala mumtima mwa munthu?

NKHANI YAPACHIKUTO

N’chifukwa Chiyani Anthu Amakonda Kugula Katundu Wambirimbiri?

N’chifukwa chiyani anthu ambiri amakonda kugula zinthu ngakhale zimene sakufunikira? Kodi mungatani kuti otsatsa malonda asakukopeni?

NKHANI YAPACHIKUTO

Kodi Mungatani Kuti Musamangogula Zinthu Mwachisawawa?

Werengani mfundo 6 zokuthandizani kuti musamangogula zinthu mwachisawawa.

ANTHU NDI MAYIKO

Panama

Ku Panama n’kotchuka kwambiri chifukwa cha ngalande zake. Werengani kuti mumve zambiri za anthu amene amkhala m’dziko limeneli.

TIONE ZAKALE

Kupha Anthu M’dzina la Mulungu

Chikalata chinalola kuti asilikari a ku Spain aphe anthu mwankhanza kwambiri. Kodi Mulungu ndi amene anachititsa zimenezi?

KODI ZINANGOCHITIKA ZOKHA?

Zipsepse za Nangumi

Werengani kuti mudziwe mmene anthufe timapindulira chifukwa cha kapangidwe ka chipsepse cha nangumi.

Zina zimene zili pawebusaiti

Kodi Ndimangokhalira Kuganizira za Maonekedwe Anga?

Kodi mungatani kuti muzisangalala ndi mmene mumaonekera?

Mkazi wa Loti Anasanduka Chipilala Chamchere

Werengani nkhani ya m’Baibulo kenako lumikizani madontho. Kodi mukuphunzira chiyani kwa mkazi wa Loti?