Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Satana

Satana

Kodi Satana ndi uchimo umene umakhala mumtima mwa munthu?

“Njoka yakale ija, iye wotchedwa Mdyerekezi ndi Satana, . . . akusocheretsa dziko lonse lapansi kumene kuli anthu.”—Chivumbulutso 12:9.

ZIMENE ANTHU AMANENA

Ena amati Satana ndi uchimo umene umakhala mumtima mwa munthu.

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Satana sakhala mumtima mwa munthu. Poyamba iye anali mngelo wabwino koma anasiya kumvera Mulungu. Baibulo limati Satana ndi “wolamulira wa dzikoli.” (Yohane 12:31) Iye amagwiritsa ntchito “zizindikiro zabodza” komanso “chinyengo” pofuna kukwaniritsa zofuna zake.—2 Atesalonika 2:9, 10.

Baibulo limanena kuti nthawi ina Mulungu ndi Satana ankalankhulana. Ngati Satana ndi uchimo umene umakhala mumtima mwa munthu, ndiye zikanatheka bwanji kuti Mulungu, yemwe alibe uchimo, alankhule ndi uchimo womwe unali mumtima mwake? (Deuteronomo 32:4; Yobu 2:1-6) Apatu zikuonekeratu kuti Satana si uchimo umene umakhala mumtima mwa munthu.

N’CHIFUKWA CHIYANI TIYENERA KUDZIWA ZOONA ZA NKHANIYI?

Satana safuna kuti anthu azikhulupirira kuti iye alipo. Ndipo zimene amachitazi n’zofanana ndi zimene chigawenga chimachita. Chigawenga chimabisa khalidwe lake n’cholinga choti chipitirizebe kuchita zoipa mobisa. Kuti muthe kudziteteza kwa Satana, choyamba muyenera kuvomereza kuti iye alipo.

 Kodi Satana Amakhala Kuti?

“Tsoka dziko lapansi . . . chifukwa Mdyerekezi watsikira kwa inu.”—Chivumbulutso 12:12.

ZIMENE ANTHU AMANENA

Anthu ambiri amakhulupirira kuti Satana amakhala pansi pa dziko lapansi pomwe ndi potentha ngati ng’anjo ya moto. Ena amati amakhala m’mitima ya anthu oipa.

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Satana saoneka chifukwa ndi mzimu. Nthawi ina Mulungu ankalola Satana kuti aziyendayenda n’kumafika kumene Mulungu ndi angelo abwino amakhala. (Yobu 1:6) Koma pano, iye limodzi ndi angelo oipa anathamangitsidwa kumwamba ndipo ali padziko lapansi pompano.—Chivumbulutso 12:12.

Koma kodi zimenezi zikutanthauza kuti Satana ali ndi malo enieni amene amakhala? Mwachitsanzo, mwina munawerengapo m’Baibulo kuti mzinda wakale wa Pegamo anali malo ‘amene Satana ankakhala.’ (Chivumbulutso 2:13) Mawu amenewa amangotanthauza kuti anthu ambiri mumzindawu ankalambira Satana. Choncho, Satana alibe malo enieni padziko lapansi amene amakhala. M’malomwake Baibulo limati: “Maufumu onse a padziko lapansi” ali m’manja mwake.—Luka 4:5, 6.

Kodi Satana amazunza kapena kulamulira anthu?

“Dziko lonse lili m’manja mwa woipayo.”—1 Yohane 5:19.

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Anthu ambiri m’dzikoli amachita zofuna za Satana ndipo zimenezi zapangitsa kuti iye aziwalamulira. (2 Akorinto 11:14) N’chifukwa chake anthu alephera kuthetsa mavuto padzikoli.

Baibulo limanenanso kuti nthawi ina Satana ndi ziwanda zake anazunza komanso kulamulira anthu.—Mateyu 12:22; 17:15-18; Maliko 5:2-5.

ZIMENE MUNGACHITE

Simuyenera kuopa Satana. Kuti Satana asamakulamulireni muyenera kudziwa zimene iye amachita pofuna kusocheretsa anthu. Zimenezi zingakuthandizeni kuti ‘mudziwe bwino ziwembu zake.’ (2 Akorinto 2:11) Kuwerenga Baibulo kungakuthandizeni kudziwa njira zimene Satana amagwiritsa ntchito pofuna kusocheretsa anthu, zomwe zingakuthandizeni kupewa misampha yake.

Muzipewa zinthu zilizonse zogwirizana ndi mizimu. (Machitidwe 19:19) Zina mwa zinthu zimenezi ndi zithumwa, mabuku, mafilimu, nyimbo kapena masewera a pakompyuta omwe amalimbikitsa zamizimu kapena zamatsenga.

Baibulo limati: “Tsutsani Mdyerekezi ndipo adzakuthawani.” (Yakobo 4:7) Kumvera malangizo a m’Baibulo kudzakutetezani kuti Satana asakusocheretseni.—Aefeso 6:11-18.