Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 KODI ZINANGOCHITIKA ZOKHA?

Zipsepse za Nangumi

Zipsepse za Nangumi

PALI nyama ina ya m’madzi yaikulu kwambiri yotchedwa nangumi. Nangumi wamkulu amakhala wamtali komanso wolemera kwambiri kuposa basi yaikulu. Koma chodabwitsa kwambiri n’chakuti nangumi savutika kusambira komanso kutembenuka. N’chifukwa chiyani savutika? Chinsinsi chake chagona pa mmene zipsepse zake zinapangidwira.

Taganizirani izi: Nyama zambiri za m’madzi zimakhala ndi zipsepse zosalala m’mbali. Koma zipsepse za nangumi n’zamabampumabampu. Ndiye zimene zimachitika n’zakuti nangumi akamasambira, madzi amazungulira m’mabampu a zipsepse zake. Zimenezi zikamachitika madziwo amakankhira nangumiyo m’mwamba zimene zimamuthandiza kuti azisambira mosavuta komanso kuti asaime pamalo amodzi. Zipsepsezo zimakhala zazitali pafupifupi hafu ya kutalika kwa thupi lonse la nangumiyo. Kutali kwa Zipsepsezo kumathandizanso kuti madzi asamangomukankhira kulikonse.

Potengera mmene zipsepse za nangumi zimagwirira ntchito, akatswiri akupanga chiwongolero cha bwato chosavuta kugwiritsa ntchito, makina oyendera madzi, makina oyendera mphepo komanso zopukusa ndege ya helekopita.

Kodi inuyo mukuganiza bwanji? Kodi zinangochitika zokha kuti zipsepse za nangumi zizigwira ntchito chonchi kapena pali winawake amene anachita kukonza kuti zizitero?