Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mungatani Kuti Musamangogula Zinthu Mwachisawawa?

Kodi Mungatani Kuti Musamangogula Zinthu Mwachisawawa?

N’zoona kuti nthawi zina timagula zinthu chifukwa chokopedwa ndi otsatsa malonda. Koma kawirikawiri anthufe timagula zinthu chifukwa chotsanzira mtima basi. Tiyeni tikambirane mfundo 6 zimene zingathandize kuti tisamangogula zinthu mwachisawawa.

  1. Musamangogula chifukwa chakuti mwaziona. Kodi mumakonda kugula zinthu makamaka zimene azitsitsa mtengo? Ngati ndi choncho ndiye kuti mwina nthawi zina mumagula zinthu musanaganizire bwino. Kuti mupewe zimenezi, muziganizira kaye mavuto amene angabwere chifukwa chogula zinthuzo. Muziganiziranso mavuto amene nthawi ina munakumana nawo mutagula chinthu mopupuluma. Choncho mukaona chinthu chinachake muzikhala kaye phee, kuganizira ngati mukufunikiradi kuchigula.

  2. Musamagule zinthu kungoti musangalale. Anthu ena amati akakhumudwa, amangopita kukagula zinthu n’cholinga choti asangalaleko ndipo amasangalaladi. Koma amangosangalala kwa nthawi yochepa chifukwa akakhumudwanso amafuna kuti akagule katundu winanso wambiri. Choncho mukakhumudwa muzipeza anzanu amene mungawauze nkhawa zanu kapena muzichita zinthu zina zolimbitsa thupi monga kupita kokayenda.

  3.   Musamangogula zinthu chifukwa chakuti mukusowa chochita. Anthu ena amapita kumalo komwe amagulitsa zinthu zapamwamba n’cholinga choti akangoona zinthu basi. Koma dziwani kuti zimene mungakaonezo zingakupangitseni kuti mufune kugula katunduyo. Choncho muzipita kushopu kapena kumsika pokhapokha ngati mukufunadi kugula chinthu chinachake ndipo muzionetsetsa kuti mwangogula chimene mwapitiracho.

  4. Muzisankha mwanzeru anthu ocheza nawo. Zimene anzanu amakonda kuchita komanso kulankhula zimakhudza kwambiri zimene inuyo mumachita. Ngati mumagula katundu wambiri n’cholinga choti mufanane ndi anzanu, mungachite bwino kusiya kucheza nawo n’kupeza anzanu amene sakonda kugula zinthu zambiri.

  5. Musamakonde kugula zinthu pangongole. Munthu akazolowera kugula zinthu pangongole amakhoza kugula zinthu zambirimbiri osaganizira za mtengo wa zinthuzo. Ngati mwatenga zinthu pangongole muziyesetsa kubweza ngongole yonse pakutha pa mwezi. Mukafuna kugula zinthu zofuna ndalama zambiri muziyesetsa kusunga ndalama, n’kudzapereka kamodzi m’malo mogula pangongole.

  6. Muzidziwa mmene ndalama zanu zikuyendera. Ngati simukudziwa mmene ndalama zanu zikuyendera mukhoza kumangogula zinthu zambirimbiri. Choncho muzidziwa kuti mukugwiritsa ntchito ndalama zochuluka bwanji komanso mukutsala ndi zochuluka bwanji. Mungachite bwino kulemba bajeti. Pakutha pa mwezi muziona kuti mwawononga ndalama zingati ndipo muziyerekezera ndi bajeti imene munalemba. Ngati pali zinthu zina zomwe simuzimvetsa bwino, zokhudza kagwiritsidwe ntchito ka ndalama, funsani mnzanu amene mumamudalira kuti akuthandize.