Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 KODI ZINANGOCHITIKA ZOKHA?

Chigoba Chomwenso Chimaona

Chigoba Chomwenso Chimaona

PALI kachilombo kena ka m’madzi komwe kamaoneka ngati nyenyezi. Kachilomboka kali ndi chigoba pakati chodabwitsa kwambiri. Pamwamba pa chigobacho pali tizinthu tooneka tonyezimira tomwe timachititsa kuti chigobacho chizigwiranso ntchito ngati diso la kachilomboka.

Tinthu tokhala ngati tiziphuphu tapamwamba pa chigoba, timagwira ntchito ngati diso la kachilomboka

Taganizirani izi: Magazini ina yotchedwa Natural History, inanena kuti asayansi ataunika chigoba cha kachilomboka anaona kuti “pamwamba pa chigobapo pali tinthu tooneka ngati tiziphuphu tonyezimira ndiponso kalikonse n’kakang’ono kuposa tsitsi la munthu.” Tiziphuphuto timakhala ndi timagalasi tomwe timatumiza chithunzi ku minyewa ya m’chigobacho. Timagalasito tinapangidwa kuti tizigwira ntchito ngati mmene maso athu amagwirira ntchito.

Katswiri wina wasayansi, dzina lake Joanna Aizenberg, ananena kuti mmene chigoba cha kachilomboka chimagwirira ntchito zimasonyeza kuti “chinthu chimodzi chikhoza kugwira ntchito zosiyanasiyana.”

Potengera mmene chigoba cha kachilomboka chimagwirira ntchito, asayansi atulukira njira yosavuta komanso yotchipa yopangira timagalasi. Timagalasiti timagwira ntchito zosiyanasiyana kuphatikizapo kutumiza mauthenga. Timagalasito timatumiza uthenga pogwiritsa ntchito kuwala.

Kodi inuyo mukuganiza bwanji? Kodi zinangochitika zokha kuti chigoba cha kachilomboka chizithanso kugwira ntchito ngati diso, kapena pali winawake amene anakonza kuti chizigwira ntchito choncho?