Kodi Zamoyo Zinachita Kulengedwa?

Zimene mumakhulupirira pa nkhani ya mmene moyo unayambira zimakhudza moyo wanu.

Mawu Oyamba

Kodi dzikoli linapangidwa kuti muzikhala zamoyo? Kodi zimene anthu amaphunzitsa zoti zamoyo zinachita kusintha kuchokera ku zinthu zina zili ndi umboni wake?

Kodi Inuyo Mumakhulupirira Zotani?

N’kutheka kuti mumakhulupirira kuti kuli Mulungu komanso mumalemekeza Baibulo. Koma mwinanso mumalemekeza zimene asayansi amanena zoti zamoyo sizinachite kulengedwa.

Pulaneti Lokhala ndi Zamoyo

Padzikoli sipakanakhala zamoyo zina zilizonse pakanapanda zinthu zosiyanasiyana zodabwitsa zimene zilipo. Kodi zinthuzi zinangokhalapo pa zokha kapena pali winawake amene anazikonza?

Kodi Ndi Ndani Anayamba Kuzipanga?

Anthu amatsanzira zinthu za m’chilengedwe popanga zinthu zovuta. Ngati kutsanzira chinthu china kumafuna nzeru za munthu, kuli bwanji kupanga chinthu choyambiriracho?

Kodi Zamoyo Zinasinthadi Kuchokera ku Zinthu Zina?​—Zimene Anthu Amanena Komanso Zoona Zake

Asayansi ena amakhulupirira kuti kusintha kwa maselo kumachititsa kuti zamoyo zisinthiretu n’kukhala za mtundu watsopano. Kodi pali umboni uliwonse wa zimenezi?

Kodi Nkhani ya M’buku la Genesis Ikugwirizana ndi Sayansi?

Kodi sayansi imatsutsa zimene Baibulo limanena pa nkhani yolenga zinthu?

Kodi Zimene Mumakhulupirira pa Nkhaniyi Zimakhudza Moyo Wanu?

Kodi zimene mumakhulupirira pa nkhani yoti zamoyo zinangokhalapo zokha zimakhudza moyo wanu?

Mndandanda wa Mabuku

Onani mabuku amene anagwiritsidwa ntchito polemba kabukuka.