Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 Nkhani Ya Pachikuto

Chenjerani ndi Mbava Komanso Anthu Ogwiririra

Chenjerani ndi Mbava Komanso Anthu Ogwiririra

“Nthawi zambiri ndikapita kukacheza anzanga ankakonda kundiperekeza kunyumba kunja kukada. Koma tsiku lina ndinatopa kwambiri moti ndinangoganiza zochita hayala taxi.

“Koma dalaivalayo anakhotetsera galimotoyo kutchire kuti akandigwiririre. Kenako anayamba kundigwiragwira ndipo ndinakuwa kwambiri moti anandisiya. Ataona kuti ndasiya kukuwa, anayambiranso kundigwiragwira ndipo ndinakuwanso n’kuthawa.

“Poyamba ndinkaona ngati kukuwa sikungathandize munthu akafuna kukugwiririra. Koma ndi zimene zinandichitikirazi ndinaona kuti kukuwa n’kothandiza kwambiri.”—Anatero KARIN. *

M’MAYIKO ambiri muli vuto la umbava komanso anthu ogwiririra. Woweruza milandu wina ananena kuti: “Mfundo yosatsutsika ndi yakuti aliyense akhoza kukumana ndi mbava kapena anthu ogwiririra.” N’zoona kuti m’madera ena vuto limeneli ndi locheperako. Komabe si nzeru kumachita zinthu motayirira chifukwa nthawi zambiri anthu amene amachita zinthu motayirira ndi amene amaberedwa komanso kugwiriridwa.

Kodi mungatani kuti mudziteteze komanso muteteze banja lanu ngakhale kuti mwina mukukhala m’dera limene zimenezi sizimachitika kawirikawiri? Chimene chingakuthandizeni kwambiri ndi kutsatira mfundo ya m’Baibulo iyi: “Wochenjera ndi amene amati akaona tsoka amabisala, koma anthu osadziwa zinthu amangopitabe ndipo amalangidwa.” (Miyambo 22:3) N’chifukwa chakenso apolisi amalimbikitsa anthu kuti azipewa zinthu zimene zingachititse kuti aberedwe kapena kugwiriridwa.

Anthu amene aberedwa kapena kugwiriridwa amavulala, kulandidwa katundu komanso kuvutika maganizo kwa nthawi yaitali. N’chifukwa chake tiyenera kuyesetsa kuchita zinthu zimene zingatiteteze. Tiyeni tikambirane zimene tingachite.

 KUBA MOOPSEZA

Kodi zimachitika bwanji? Munthu wokuba moopseza amagwiritsa ntchito chida kapena kungoopseza ndi mawu pofuna kuti mumpatse zimene akufuna.

Mmene zimakhudzira anthu: Ku Britain, akuba ataba malo osiyanasiyana motsatizana, wapolisi wina anafotokoza kuti anthu oberedwawo sanavulazidwe koma ankavutika maganizo kwambiri. Iye ananena kuti: “Ambiri mwa anthuwa anali ndi nkhawa komanso ankasowa tulo ndipo pafupifupi onse ananena kuti zimene zinachitikazo zinasokoneza kwambiri moyo wawo.”

Zimene mungachite.

 • Mbava zimakonda kupezerera anthu amene sachita zinthu mochenjera, choncho muzikhala tcheru kuti muziona anthu okayikitsa

  Muzichita zinthu mochenjera. Mbava zimakonda kubera anthu amene sachita zinthu mochenjera. Choncho muzikhala tcheru kuti muziona anthu okayikitsa ndipo muzipewa kuledzera kapena kumwa mankhwala osokoneza bongo chifukwa zimenezi zimachititsa kuti munthu asamaganize mochangamuka. Buku lina la za umoyo linanena kuti: “Munthu akaledzera kapena akamwa mankhwala osokoneza bongo amalephera kuganiza bwino moti sangathe kuzindikira anthu okayikitsa.”

 • Muziteteza zinthu zanu. Muzitseka mawindo ndi kukhoma zitseko za nyumba komanso galimoto yanu. Musamangotenga anthu osawadziwa m’galimoto yanu kapena kulowetsa anthu osawadziwa m’nyumba mwanu. Lemba la Miyambo 11:2 limati: “Nzeru zimakhala ndi anthu odzichepetsa.” Akuba komanso ana opemphapempha amakonda kubera anthu amene amaika zinthu ngati mafoni poonekera.

 • Muzimvera malangizo. Baibulo limati: “Njira ya munthu wopusa imakhala yolondola m’maso mwake, koma womvera malangizo ndi wanzeru.” (Miyambo 12:15) Ngati mwapita kudera linalake lomwe simukulidziwa bwinobwino, funsani anthu okhawo omwe ndi osakayikitsa kapena apolisi. Akhoza kukuuzani malo oopsa amene mufunika kupewa komanso angakuuzeni zimene mungachite kuti akuba asakubereni.

NKHANZA ZOKHUDZA KUGONANA

Kodi zimachitika bwanji? Si kuti nkhanza zokhudza kugonana ndi kugwiriridwa kokha. Ngati munthu akukakamiza kapena kuopseza munthu wina kuti agone naye kapena kuti achite naye zinthu zina zokhudza kugonana, ndiye kuti akumuchitira nkhanza zokhudza kugonana.

Mmene zimakhudzira anthu: Mtsikana wina yemwe anagwiriridwapo ananena kuti: “Munthu ukagwiriridwa sikuti umangovutika nthawi yokhayo. Umavutikabe maganizo kwa nthawi yaitali komanso chilichonse pa moyo wako chimasintha ndipo zimakhudza kwambiri achibale ako.” Komanso dziwani kuti, munthu akagwiriridwa safunika kudziimba mlandu chifukwa wolakwa amakhala wogwirirayo.

Zimene mungachite.

 • Ngati pali munthu wokaikitsa muzichokapo. Dipatimenti ya apolisi ya ku North Carolina, ku America, inanena kuti: “Ngati muli pamalo okayikitsa kapena pamalopo pali munthu wokayikitsa ndi bwino kuchokapo. Musalole munthu kukuletsani kuchoka ngati inuyo mukuona kuti mukufunika kuchokapo.”

 • Muzichita zinthu molimba mtima ndipo muzikhala tcheru. Anthu ogwiririra amakonda kupezerera anthu amene akuoneka amantha komanso osachita zinthu mochenjera. Choncho mukamayenda muzionetsetsa kuti mukuchita zinthu mochangamuka komanso muzikhala tcheru.

 • Muzichita zinthu zodziteteza mwansanga. Munthu akafuna kukugwiririrani muzikuwa. (Deuteronomo 22:25-27) Muziyesetsa kuthawa kapena kumumenya paliponse. Ndipo ngati n’zotheka, thawirani kumene kuli anthu n’kuimbira apolisi. *

 UCHIGAWENGA WA PA INTANETI

Kodi zimachitika bwanji? Zigawenga za pa Intaneti zimabera anthu ndalama m’njira zosiyanasiyana kuphatikizapo kuwanamiza kuti awagulitsa katundu wotchipa kapena kuti awalemba ntchito. Pochita zonsezi, akuba amauza anthuwo kuti alipire ndalama ndipo akatero amaba ndalamazo.

Mmene zimakhudzira anthu: Uchigawenga wa pa Intaneti umachititsa kuti anthu oberedwawo komanso dziko liwononge mabiliyoni ambiri. Taganizirani zimene zinachitikira Sandra. Iye analandira imelo yomwe inkaoneka ngati yachokera ku banki yake. Mu imeloyo anamuuza kuti atumize ku bankiyo manambala ndi zinthu zina zachinsinsi zokhudza akaunti yake. Patangopita mphindi zochepa atatumiza zinthuzo, anazindikira kuti ku akaunti yake kwachoka ndalama zokwana madola 4,000. Pamenepa iye anadziwa kuti anthu ena amuyenda pansi.

Zimene mungachite.

 • Muzisamala. Musamangokopeka ndi ma webusaiti omwe akuoneka ngati ndi odalirika. Dziwani kuti makampani odalirika sangapemphe munthu kutumiza zinthu zake zachinsinsi pa Intaneti. Mukafuna kugula kapena kugulitsa zinthu pa Intaneti muzifufuza kaye za kampani imene mukufuna kuchita nayo malondayo. Lemba la Miyambo 14:15 limati: “Munthu amene sadziwa zinthu amakhulupirira mawu alionse, koma wochenjera amaganizira za mmene akuyendera.” Komanso muzichita zinthu mosamala mukafuna kugula zinthu ku kampani yam’dziko lina chifukwa ngati patakhala vuto linalake, zikhoza kukhala zovuta kuti mulithetse.

 • Muzifufuza zambiri za kampaniyo. Dzifunseni kuti: “Kodi ndikudziwa kumene kuli kampaniyi? Kodi nambala ya foni ya kampaniyi ndi yolondola? Kodi katunduyu adzafunika kulipira ndalama zina zowonjezera? Kodi ndidzalandira liti katundu amene ndikugulayu? Kodi kampaniyi imalola kukubwezera ndalama kapena kubweza katundu?”

 • Muzisamala ndi makampani amene amalonjeza zinthu zabwino kwambiri. Nthawi zambiri anthu oba pa Intaneti amapezerera anthu adyera komanso amene amakonda kupeza zinthu mwaulere. Akubawo amanyengerera anthu powauza kuti awapatsa ndalama zambiri akagwira kantchito kochepa, awapatsa ngongole ngakhale atakhala kuti sangakwanitse kuibweza kapena amawauza kuti akagulitsa zinthu motchipa apeza ndalama zambiri. Bungwe lina la ku America linanena kuti: “Muzifufuza mokwanira mukafuna kugulitsa zinthu pa Intaneti. Ngati akukulonjezani kuti mupeza ndalama zambiri, dziwani kuti amenewo ndi akuba. Musalole kuti anthu ena akunyengerereni kuti mupange malonda ndi anthu kapena kampani imene mukuikayikira.”

KUGWIRITSA NTCHITO MWAKUBA ZINTHU ZACHINSINSI ZA ANTHU ENA

Kodi zimachitika bwanji? Anthu amaba zinthu zachinsinsi za munthu wina n’kuzigwiritsa ntchito m’dzina la mwini wakeyo n’cholinga choti abe kapena kuti achite zinthu zina zachinyengo.

Mmene zimakhudzira anthu: Akuba amatha kugwiritsa ntchito zinthu zanu zachinsinsi monga dzina lanu, nambala ya akaunti yanu yakubanki kutengera ngongole kapena kutsegula akaunti yakubanki. Zimenezi zingachititse kuti ngongole zonse zimene angatenge zikhale m’dzina lanu. Ngakhale bankiyo itadziwa kuti siinu amene munatenga ngongoleyo, n’kukuuzani kuti musalipire, zimakhala zovuta kuti azikukhulupirirani pankhani ya ndalama. Munthu wina amene zimenezi zinamuchitikirapo ananena kuti: “Zinthu ngati zimenezi zikakuchitikira chilichonse chimasokonekera. Ndipo n’zopweteka kwambiri kuposa kukubera ndalama.”

Zimene mungachite.

 • Muzisunga mosamala zinthu zanu zachinsinsi. Ngati mumagula zinthu, kutumiza kapena kulandira ndalama pogwiritsa ntchito Intaneti, muzisinthasintha nambala yanu yachinsinsi yolowera pa kompyuta. Muzichita zimenezi makamaka ngati kompyutayo imagwiritsidwa  ntchito ndi anthu ambiri. Komanso muzisamala ndi ma imelo amene amakuuzani kuti mutumize zinthu zanu zachinsinsi pa Intaneti.

  Zigawenga zobera anthu pa Intaneti sizimagwiritsa ntchito makompyuta okha zikafuna kuba. Zimabanso makalata ena ofunika ngati makalata a kubanki, mabuku a cheke komanso manambala achinsinsi a anthu. Choncho muzisunga pabwino zinthu ngati zimenezi ndipo ngati mukufuna kutaya mapepala amene angakhale ndi zinthu zanu zachinsinsi, muziwang’amba kapena kuwawotcha. Ngati mwazindikira kuti mapepala ena ofunika kwambiri abedwa kapena asowa mungachite bwino kukanena kupolisi kapena kubanki mwansanga.

 • Muziona mmene ndalama zanu zikuyendera. Bungwe lina la ku America linanena kuti: “Chinthu chimodzi chomwe mungachite kuti anthu asabe n’kugwiritsa ntchito zinthu zanu zachinsinsi ndi kudziwa bwino mmene ndalama zanu zikuyendera. Mukaona mwansanga kuti penapake ndalama zanu sizinayende bwino zimakhala zosavuta kuti mukonze zinthu.” Choncho muzidziwa kuti ndalama zanu zikuyenda bwanji ndipo muzionetsetsa ngati penapake sizinayende bwino. Ngati n’zotheka, muzitenga sitetimenti yanu kuti muone ndalama zimene mwakhala mukutenga komanso zimene zili ku akaunti yanu.

N’zoona kuti masiku ano simungadzitetezeretu kwa anthu akuba chifukwa ngakhale anthu osamala kwambiri aberedwapo kapena kugwiriridwa. Komabe kugwiritsa ntchito nzeru zopezeka m’Baibulo kumatithandiza chifukwa limati: “Nzeruzo usazisiye ndipo zidzakusunga. Uzikonde ndipo zidzakuteteza.” (Miyambo 4:6) Ndipo n’zosangalatsa kuti Baibulo limalonjeza kuti umbava komanso kugwirirana zidzatha.

Umbava Komanso Kugwiririra Zitha Posachedwapa

Kodi n’chiyani chingatithandize kukhulupirira kuti Mulungu adzathetsa umbava komanso kugwiririra? Taonani malemba otsatirawa:

 • Mulungu amafunitsitsa kuthetsa umbava komanso kugwiririra. “Ine Yehova ndimakonda chilungamo. Ndimadana ndi zauchifwamba ndi kupanda chilungamo.”—Yesaya 61:8.

 • Mulungu ali ndi mphamvu zothetsera umbava komanso kugwiririra. “Iye ali ndi mphamvu zambiri, ndipo sadzanyoza chilungamo ndi kulungama kochuluka.”—Yobu 37:23.

 • Mulungu walonjeza kuti adzawononga anthu onse oipa n’kusiya anthu abwino. “Pakuti ochita zoipa adzaphedwa.” “Olungama adzalandira dziko lapansi, Ndipo adzakhala mmenemo kwamuyaya.”—Salimo 37:9, 29.

 • Mulungu walonjeza kuti anthu okhulupirika adzakhala padziko latsopano. “Koma anthu ofatsa adzalandira dziko lapansi, ndipo adzasangalala ndi mtendere wochuluka.”—Salimo 37:11.

Zimenezitu ndi zolimbikitsa kwambiri. Mungachite bwino kupatula nthawi yoti muziphunzira Baibulo kuti mudziwe zimene Mulungu akufuna kuchitira anthu. Baibulo ndi buku lokhalo limene lili ndi malangizo othandiza komanso limatitsimikizira kuti umbava ndi kugwiririra zitha posachedwapa. *

Mulungu walonjeza kuti anthu okhulupirika adzakhala m’dziko latsopano mmene simudzakhala mbava komanso anthu ogwiririra

^ ndime 5 Mayina asinthidwa.

^ ndime 22 Anthu ambiri amagwiriridwa ndi achibale kapena anthu ena owadziwa. Kuti mudziwe zambiri, onani mutu wakuti, “How Can I Protect Myself From Sexual Predators?” m’buku lachingerezi lakuti Questions Young People Ask—Answers That Work, Volume 1, patsamba 228. Bukuli mukhoza kulipezanso pa Webusaiti yathu www.jw.org.

^ ndime 44 Mukhoza kudziwa zimene Baibulo limanena pa nkhani zosiyanasiyana m’buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? Bukuli mukhoza kulipeza mwaulere kwa a Mboni za Yehova kapena mukhoza kuliwerenga pa Webusaiti ya www.jw.org.