Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Ndikaulule Tchimo la Mnzanga?

Kodi Ndikaulule Tchimo la Mnzanga?

Zimene Achinyamata Amadzifunsa

Kodi Ndikaulule Tchimo la Mnzanga?

“Chifukwa chakuti anali mnzanga kwambiri, zinandivuta zedi kukamunenera.”—James. *

“Zinthu sizinali bwino. Anayamba kunditenga ngati kuti sanandionepo chifukwa chakuti ndinaulula zimene anachita.”—Ann.

BAIBULO limati: ‘Lilipo bwenzi lipambana mbale kuumirira.’ (Miyambo 18:24) Kodi muli ndi mnzanu ngati ameneyu? Ngati muli naye, ndiye kuti muli ndi chinthu chamtengo wapatali.

Koma bwanji ngati mnzanu amene amati ndi Mkhristu wachita tchimo? Mwachitsanzo, bwanji ngati wachita chiwerewere, wasuta fodya, wamwa mowa asanafike pamsinkhu wovomerezeka ndi boma, wagwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo kapena wachita tchimo linalake lalikulu? (1 Akorinto 6:9, 10; 1 Timoteyo 1:9, 10) Kodi muyenera kuchita chiyani? Kodi muyenera kumuuza kuti mwadziwa zimene wachita? Kodi muyenera kuuza makolo anu kapena ake? Kapena kodi muyenera kuuza mkulu wina mumpingo? * Kodi mukakamunenera, sizisokoneza ubwenzi wanu? Kapena zingakhale bwino kungosiya osaulula?

Kodi Ndiulule Kapena Ndisaulule?

Munthu aliyense amalakwa. Ndipotu Baibulo limati: “Onse ndi ochimwa ndipo ndi operewera pa ulemerero wa Mulungu.” (Aroma 3:23) Komabe, ena amachita machimo aakulu. Anthu ena ‘amapatuka panjira’ moti ngati atapanda kusintha angagwere m’mavuto aakulu. (Agalatiya 6:1) Taonani chitsanzo ichi chimene chinachitikadi.

Mkhristu wina wachinyamata dzina lake Susan anapeza kuti mnzake wina, amenenso ndi Mkhristu, anali kuonera pa Intaneti zinthu zolaula ndi kumvera nyimbo zotukwana.

Taganizirani Izi: Kodi mukanatani mukanakhala Susan? Kodi mukanamunenera mnzanuyo? Kapena mukanangoti n’zake zimenezo, sizikundikhudza? Nanga bwanji ngati Susan akanakupemphani malangizo, kodi mukanamuuza chiyani?

․․․․․

Zimene Susan Anachita: Susan ataiganizira nkhaniyi, anaona kuti ndi bwino kukalankhula ndi makolo a mnzakeyo. Iye anati: “Ndinkachita mantha kuwauza chifukwa makolowo analinso anzanga. Zinali zondivuta zedi kuti ndiwauze nkhaniyi moti ndinangoyamba kulira.”

Kodi mukuganiza bwanji? Kodi Susan anachita bwino? Kapena zikanakhala bwino akanangokhala osanena chilichonse?

Kuti tikuthandizeni kuganizira bwino nkhaniyi, onani mfundo zina zofunika kuzilingalira.

Kodi bwenzi lenileni lingachite chiyani? Lemba la Miyambo 17:17 limati: “Bwenzi limakonda nthawi zonse; ndipo mbale anabadwira kuti akuthandize pooneka tsoka.” Munthu akachita zinthu mosiyana ndi mfundo za m’Baibulo, amakhala pa “tsoka,” kaya munthuyo akudziwa kapena sakudziwa. N’zoona kuti n’kulakwa kukhala ‘wolungama mopambanitsa’ mwa kukulitsa nkhani zing’onozing’ono, komabe bwenzi lenileni silimalekerera khalidwe loipa. (Mlaliki 7:16) Choncho, sikoyenera kungonyalanyaza nkhaniyo.—Levitiko 5:1.

Dziyerekezereni kuti ndinu kholo. Dzifunseni kuti: ‘Ndikanakhala kuti ndine kholo ndipo mwana wanga amaonera zinthu zolaula pa Intaneti, kodi ndingasangalale wina atandiuza? Kodi ndingamve bwanji ngati mnzake wa mwana wanga akudziwa zimenezi koma osanena chilichonse?’

Nanga bwanji malamulo a Mulungu? Apa sipofunika kungokhala chete. M’malo mwake, muyenera kutsatira malamulo a Mulungu a m’Baibulo. Dziwani kuti mukaimira choonadi, mumasangalatsa mtima wa Mlengi wanu. (Miyambo 27:11) Komanso, mumamva bwino podziwa kuti mwamuthandiza kwambiri mnzanuyo.—Ezekieli 33:8.

“Mphindi Yakulankhula”

Baibulo limanena kuti pali “mphindi yakutonthola [kapena kuti yokhala chete] ndi mphindi yakulankhula.” (Mlaliki 3:7) Nthawi zambiri achinyamata sadziwa zoyenera kuchita pankhani zina. Mwachitsanzo, mnzawo akachita tchimo, iwo angaganize kuti: ‘Sindikufuna kumuika mnzangayu m’mavuto’ kapena kuti ‘sindikufuna kudana naye.’ Ngati maganizo anu atakhala amenewa, kusankha chochita kungaoneke ngati kosavuta. Mungasankhe kungokhala chete.

Komabe mukamakula, mumayamba kuona zinthu mwauchikulire. Mumazindikira kuti mnzanuyo ali ndi vuto limene akufunika thandizo ndipo mwina inuyo ndi amene mungam’thandize. Koma kodi mungatani ngati mwamva kuti mnzanu wachita zosiyana ndi malamulo kapena mfundo za m’Baibulo?

Choyamba, tsimikizirani ngati zimene mwamvazo zili zoona. N’kutheka kuti ndi mphekesera chabe. (Miyambo 14:15) Mtsikana wina dzina lake Katie anati: “Mnzanga wina ankafalitsa nkhani zabodza zokhudza ineyo, ndipo anzanga ena ankakhulupirira zimenezo. Ndinkaona kuti palibe amene angakhulupirire zonena zanga.” Komatu Baibulo linalosera kuti Yesu “sadzadzudzula mwamphekesera.” (Yesaya 11:3) Kodi tikuphunzirapo chiyani pamenepa? Musafulumire kukhulupirira kuti zonse zimene mwamva n’zoona. Yesani kupeza zoona zake za nkhaniyo. Taonaninso chitsanzo ichi chimene chinachitikadi.

James, amene tamutchula koyamba kwa nkhani ino uja, anamva kuti mnzake wina anamwa mankhwala osokoneza bongo atapita ku phwando.

Taganizirani izi: Kodi mukanatani mukanakhala James? Kodi mukanatsimikiza bwanji kuti zimene mwamvazo ndi zoona?

․․․․․

Zimene James anachita. Poyamba James anachita ngati sanamve chilichonse. Koma iye anati: “Chikumbumtima changa chinayamba kundivutitsa. Ndinkadziwa kuti ndiyenera kukalankhula ndi mnzangayo za nkhaniyi.”

Kodi mukuganiza bwanji? Kodi kuyamba mwalankhula ndi munthu amene mwamva kuti wachita tchimo kuli ndi ubwino wotani?

․․․․․

Ngati simungathe kulankhula ndi munthuyo, kodi mungatani?

․․․․․

Mnzake wa James anavomera kuti anamwadi mankhwala osokoneza bongo atapita ku phwandoko. Komabe, anam’pempha James kuti asakauze aliyense. Koma James ankafuna kuchita zimene zinali zoyenera. Ndipo ankafunanso kuti mnzakeyo achite zinthu zoyenera. Choncho, anamuuza mnzakeyo kuti am’patsa mlungu umodzi kuti akaulule nkhaniyo kwa akulu mu mpingo wake. Ngati sakaulula, ndiye kuti James akawauza akulu nkhaniyo.

Kodi mukuganiza kuti James anachita bwino? N’chifukwa chiyani mukuti anachita bwino kapena sanachite bwino?

․․․․․

Mnzake wa James atalephera kuwauza akulu, James anakawauza. Ndipo, patapita nthawi, mnzakeyo anazindikira kulakwa kwake. Akulu anamuthandiza kuzindikira kuti m’pofunika kulapa kuti akhalenso ndi ubwenzi wabwino ndi Yehova.

Kodi Ndiye Kuti Ndinu Wapakamwa?

Mwina mungafunse kuti: ‘Kodi ndikamunenera mnzangayu, sindikhala wapakamwa? Kodi sizingakhale bwino kungokhala ngati sindikudziwa chilichonse?’ Ngati mukuona choncho, kodi mungatani?

Choyamba, dziwani kuti chinthu chosavuta kuchita chimakhala choipa koma chinthu chabwino chimavuta kuchita. Zimafunika kulimba mtima kuti muulule tchimo limene mnzanu wachita. Bwanji osauza Mulungu nkhaniyi m’pemphero? M’pempheni Mulungu kuti akupatseni nzeru komanso akulimbitseni mtima. Ndipo iye adzakuthandizani.—Afilipi 4:6.

Chachiwiri, ganizirani mmene mnzanuyo angapindulire ngati mutaulula tchimo lake. Mwachitsanzo, yerekezerani kuti muli ndi mnzanu ndipo mukukwera phiri, ndiyeno mnzanuyo wapunthwa n’kugwa. Mwachiwonekere mungafunike kumuthandiza. Nanga bwanji ngati chifukwa cha manyazi akukana kuti mum’thandize? Kodi mungangomusiya moyo wake uli pachiswe?

N’zofanana ndi mnzanu amene wapunthwa mwauzimu. Iye angaganize kuti angachire yekha mwauzimu popanda kumuthandiza. Komabe si nzeru kuganiza choncho. N’zoona kuti mnzanuyo angachite manyazi ndi zimene wachitazo. Koma ngati ‘muitana thandizo,’ mungapulumutse mnzanuyo.—Yakobe 5:15.

Choncho, musaope kuulula ngati mnzanu wachita tchimo. Mukamuitanira thandizo, mumasonyeza kuti ndinu wokhulupirika kwa Yehova Mulungu ndi kwa mnzanuyo, amene tsiku lina adzakuthokozani kuti munamuthandiza.

Nkhani zina zakuti “Zimene Achinyamata Amafunsa,“ mungazipeze pa adiresi yathu ya pa Intaneti ya www.jw.org.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Tasintha maina m’nkhani ino.

^ ndime 6 Akulu mu mpingo wa Mboni za Yehova amathandiza mwauzimu munthu aliyense amene wachita tchimo lalikulu.—Yakobe 5:14-16.

ZOTI MUGANIZIRE

▪ Kodi n’chifukwa chiyani kuulula tchimo limene mnzanu wachita ndi umboni woti ndinu wokhulupirika kwa mnzanuyo?

▪ Ndi anthu a m’Baibulo ati amene mungawatchule amene anayesedwa pankhani yokhala okhulupirika kwa mnzawo? Nanga mungaphunzire chiyani pa zimene anachita?

[Chithunzi patsamba 20]

Ngati mnzanu wachita tchimo, onetsetsani kuti wathandizidwa