Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mmene Moyo Unalili Zinthu Zitasintha Kwambiri ku Korea

Mmene Moyo Unalili Zinthu Zitasintha Kwambiri ku Korea

Mmene Moyo Unalili Zinthu Zitasintha Kwambiri ku Korea

Yosimbidwa ndi Chong-il Park

“Ndiwe wa mantha eti! Ukuopa kufera kunkhondo? Ukungonamizira chipembedzo pofuna kukana usilikali.” Izi ndi zimene mkulu wa asilikali wa gulu lachitetezo ananena mu June 1953, zaka zoposa 55 zapitazo.

ZIMENEZI zinachitika ku Korea nthawi imene kunali nkhondo. Ndiyeno mkuluyo anatulutsa mfuti n’kuiika pa tebulo. Kenako anati: “Ufera muno m’malo mokafera kunkhondo. Kapena kodi wasintha maganizo?”

Ndinayankha molimba mtima kuti: “Ayi sindinasinthe.” Ndiyeno mkuluyo anauza msilikali wina kuti akonze zokandinyonga.

Zinthu zinafika pamenepa chifukwa ndinakana atandilamula kuti ndilowe usilikali. Ndikuyembekezera kunyongedwa, ndinauza mkuluyo kuti ndinadzipereka kale kwa Mulungu. Choncho, ndinkaona kuti sindikufunikira kutumikira anthu ena koma Mulungu yekha. Tinakhala kanthawi osalankhulana, ndipo kenako msilikali uja anabweranso ndi kunena kuti wakonza zonse zofunikira kuti ndiphedwe.

Panthawiyi, anthu ambiri a ku South Korea samazidziwa bwino Mboni za Yehova. Iwo makamaka sankamvetsa chifukwa chake chikumbumtima chathu sichimatilola kulowa usilikali. Ndisanafotokoze zimene zinachititsa kuti zinthu zifike pamenepa, ndiloleni ndinene zomwe zinandichititsa kukana zimene mkulu wa asilikali uja anandiuza kuchita.

Mmene Ndinaphunzirira Choonadi

Ndinabadwa mu October 1930, ndipo ndinali woyamba kubadwa m’banja lathu. Ndinabadwira m’tauni ina pafupi ndi mzinda wa Seoul womwe panthawiyo unali likulu la dziko la Korea. Agogo anga anali odzipereka kwambiri m’chipembedzo cha Confucius ndipo ankandiphunzitsa kuti nanenso ndikhale wachipembedzo chomwechi. Iwo sankafuna kuti ndizipita ku sukulu moti ndinayamba sukulu iwo atamwalira. Ndipo panthawiyi ndinali ndi zaka 10. Ndiyeno mu 1941, mayiko a Japan ndi United States anathandizira mayiko osiyana pankhondo yachiwiri yapadziko lonse.

Popeza dziko la Korea linkalamulidwa ndi dziko la Japan, m’mawa uliwonse kusukulu tinkachita mwambo wolemekeza mfumu ya ku Japan. Azakhali anga ndi amuna awo anali a Mboni za Yehova ndipo panthawi ya nkhondo yachiwiri yapadziko lonse anali kundende m’dziko la Korea chifukwa chikhulupiriro chawo sichinawalole kuthandiza pankhondoyo. Boma la Japan linkachitira nkhanza anthu a Mboni za Yehova moti ambiri kuphatikizapo amuna awo a azakhali anafa. Kenako azakhali anadzakhala kwathu.

Dziko la Japan linasiya kulamulira dziko la Korea mu 1945. Azakhali aja pamodzi ndi a Mboni ena amene anatuluka ku ndende, anandithandiza kuphunzira Baibulo ndipo mu 1947 ndinabatizidwa kukhala wa Mboni za Yehova. Mu August 1949, Don ndi Earlene Steele anafika ku Seoul. Iwo anaphunzira ku Sukulu ya Gileadi Yophunzitsa Baibulo, ndipo anali amishonale oyamba kudzatumikira m’dziko la Korea. Patangotha miyezi yochepa chabe kunabweranso amishonale ena.

Pa January 1, 1950, ineyo ndi ofalitsa ena atatu achikoreya tinayamba upainiya, dzina la atumiki anthawi zonse a Mboni za Yehova. Nkhondo yachiwiri yapadziko lonse itatha, tinali oyamba kuchita upainiya ku Korea.

Mmene Moyo Unalili Panthawi ya Nkhondo ku Korea

Pasanapite nthawi, Lamlungu pa June 25, 1950, dziko la North Korea linayamba kumenyana ndi la South Korea. Panthawiyi, m’dziko lonse la Korea munali mpingo umodzi wokha wa Mboni za Yehova, womwe unali ku Seoul ndipo unali ndi ofalitsa 61. Ndipo ofesi ya kazembe wa dziko la America inauza amishonale onse kuchoka m’dzikoli kuti apulumutse moyo wawo. Nazonso Mboni zambiri za m’dzikoli zinachoka ku Seoul ndipo zinapita ku madera a kum’mwera kwa dzikoli.

Koma boma la South Korea linkaletsa achinyamata a msinkhu wanga, omwe anali oyenera kulowa usilikali, kuti asachoke m’mzindawu. Kenako asilikali achikomyunizimu analowa m’mzinda wa Seoul ndipo anayamba kulamulira mzindawu. Ngakhale kuti panthawiyi ndinabisala m’kachipinda kakang’ono kwa miyezi itatu, ndinkalalikirabe za Ufumu wa Mulungu. Mwachitsanzo, ndinakumana ndi mphunzitsi wina amene ankathawanso asilikali achikomyunizimu. Tinayamba kukhalira limodzi ndipo ndinkaphunzira naye Baibulo tsiku lililonse. Patapita nthawi anabatizidwa n’kukhala wa Mboni za Yehova.

Ndiyeno asilikali a ku North Korea anadziwa malo amene tinkabisala. Tinawauza kuti ndife ophunzira Baibulo ndipo tinawafotokozera ziphunzitso za m’Baibulo za Ufumu wa Mulungu. Tinadabwa kwambiri kuona kuti sanatigwire koma anachita chidwi ndi uthenga wa m’Baibulo. Zinali zodabwitsa kuti ena mwa iwo anabweranso maulendo angapo kuti adzamve zambiri za Ufumu wa Mulungu. Zimenezi zinalimbitsa kwambiri chikhulupiriro chathu chakuti Yehova amatiteteza.

Asilikali a United Nations atayambanso kulamulira mzinda wa Seoul, mu March 1951 ndinapatsidwa chilolezo chapadera choti ndipite ku mzinda wa Taegu. Ndinalalikira ndi Mboni zinzanga kwa miyezi ingapo mu mzinda umenewu. Ndiyeno, mu November 1951, nkhondo isanathe, Don Steele anabweranso ku Korea.

Ndinam’thandiza kulinganizanso ntchito yathu yolalikira. Panafunika kumasulira mu Chikoreya mabuku omwe amathandiza Mboni pantchito yawo yolalikira monga Nsanja ya Olonda ndi Informant, umene masiku ano timati Utumiki Wathu wa Ufumu. Zinthu zimenezi ankazitumiza ku mipingo imene panthawiyo inali m’mizinda yosiyanasiyana. Nthawi zina tinkayendera limodzi ndi Don pokalimbikitsa mipingo.

Mu January 1953, ndinasangalala kwambiri kulandira kalata yondiitana ku maphunziro aumishonale ku Sukulu ya Gileadi imene imachitikira ku New York. Koma atandidulira tikiti yandege ndinalandira uthenga kuchokera ku ofesi ya boma ya Korea yoti ndikayambe usilikali.

Nkhani ya Moyo Kapena Imfa

Ndili polembetsera usilikali, ndinafotokozera msilikali wina kuti sindimachita nawo za ndale kapena usilikali. Nditamuuza zimenezi ananditumiza kwa anthu oona zachitetezo kuti akandifufuze ngati ndinali wa chikomyunizimu. Apa m’pamene ndinafunikira kusankha moyo kapena imfa monga ndafotokozera kumayambiriro kuja. Koma m’malo mondiwombera, mkulu wa asilikali uja mwadzidzidzi anapatsa ndodo msilikali wina kuti andikwapule nayo. Ngakhale kuti ndinkamva kupweteka kwambiri, ndinasangalala kuti ndinapirira.

Anthu oona zachitetezo aja ananditumizanso kolembetsera usilikali konkuja. Asilikali a kumeneku sanasamale za chikhulupiriro changa moti anandipatsa nambala ya usilikali n’kunditumiza ku malo ophunzitsira usilikali pachilumba cha Cheju pafupi ndi dziko la Korea. Tsiku lotsatira onse omwe analembedwa kumene usilikali, kuphatikizapo ineyo, anatiuza kuti tilumbire kuti ndife asilikali. Ndinakana kulumbira ndipo anandiimba mlandu ku khoti la asilikali. Choncho anandigamula kuti ndikhale m’ndende zaka zitatu.

Anthu Ambiri Anakhalabe Okhulupirika

Tsiku limene ndimayenera kupita ku sukulu ya Gileadi, ndinaona ndege imene ndimafunika kukwera popita ku Gileadi ikuuluka. Sindinakhumudwe chifukwa cholephera kupita ku Gileadi koma ndinasangalala kwambiri chifukwa chokhala wokhulupirika kwa Yehova. Ndipo pa Mboni zachikoreya, si ine ndekha amene ndinakana usilikali. M’zaka zimenezi, Mboni zoposa 13,000 zinakana kulowa usilikali. Tikaphatikiza zaka zonse zimene Mboni zimenezi zakhala ku ndende ku Korea n’zoposa 26,000.

Ananditulutsa mu 1955, nditakhala ku ndende zaka ziwiri, chifukwa ndinali mkaidi wakhalidwe labwino. Ndinayambiranso utumiki wanga wa nthawi zonse ndipo mu October 1956, anandiitana kukatumikira ku ofesi ya Mboni za Yehova ku South Korea. Mu 1958, anandiitananso ku sukulu ya Gileadi. Nditamaliza maphunziro amenewa ananditumiza kukatumikiranso ku Korea.

Patapita nthawi pang’ono nditabwerera ku Korea, ndinadziwana ndi Mboni ina yokhulupirika dzina lake In-hyun Sung, ndipo tinakwatirana mu May 1962. Iye anakulira m’banja la Chibuda ndipo anaphunzira choonadi kwa mnzake wa ku sukulu. Zaka zitatu zoyambirira titangokwatirana, mlungu uliwonse tinkayendera mipingo ku Korea ndi cholinga cholimbikitsa mwauzimu abale ndi alongo. Kuyambira mu 1965 takhala tikugwira ntchito pa ofesi yanthambi ya Mboni ya ku Korea, yomwe ili pamtunda wa makilomita 60 kuchokera ku Seoul.

Ndikaganizira Mmene Zinthu Zasinthira

Ndikaganizira zomwe zachitika m’mbuyomu ndimadabwa kwambiri ndi mmene zinthu zasinthira m’dziko lathu. Nkhondo yachiwiri yapadziko lonse ndiponso ya North Korea ndi South Korea itatha, dziko la South Korea linali litawonongedwa kwambiri. Mizinda inali mabwinja okhaokha. Magetsi ankathimathima ndipo chuma cha dzikoli chinalowa pansi kwambiri. Koma pambuyo pa zaka 50, dziko la South Korea lasintha kwambiri.

Masiku ano, dziko la South Korea lili pa nambala 11 pa mayiko olemera kwambiri. Dzikoli ndi lotchuka chifukwa cha mizinda yake yamakono, sitima zamakono zothamanga kwambiri, komanso lili ndi akatswiri opanga zinthu zamagetsi ndi magalimoto. Panopo dziko la South Korea lili pa nambala 5 pa mayiko amene amapanga magalimoto ambiri. Koma chosangalatsa kwambiri n’chakuti, dzikoli layamba kulemekeza ufulu wa chibadwidwe wa nzika zake.

Mu 1953 pamene ankandiimba mlandu ku khoti la asilikali, boma la Korea silinkadziwa chifukwa chake anthu ena amakana kulowa usilikali. Ena mwa ife anali kutiganizira kuti tinali achikomyunizimu ndipo Mboni zina zinamenyedwa mpaka kufa. Ambiri amene anamangidwa ali achinyamata chifukwa chokana kulowa usilikali, aona ana awo ngakhale zidzukulu zawo zomwe, zikumangidwanso pa chifukwa chomwechi.

Zaka zingapo zapitazo, atolankhani alemba nkhani zabwino zofotokoza chifukwa chake Mboni za Yehova sizilowa usilikali m’dziko lililonse. Katswiri wina wodziwa malamulo amene anazunza kwambiri Mboni ina analemba kalata yopepesa imene inafalitsidwa m’magazini ina yotchuka.

Ndikukhulupirira kuti boma la South Korea lidzalemekeza ufulu wathu wosatenga mbali m’nkhondo monga amachitira mayiko ena ambiri. Ndimapemphera kuti boma la South Korea lidzapatse ufulu anthu achikhulupiriro ngati changa ndi kusiya zomanga achinyamata amene chikumbumtima chawo chimawaletsa kulowa usilikali “kuti tikhale ndi moyo wabata ndi wamtendere.”—1 Timoteyo 2:1, 2.

Monga atumiki a Mulungu wathu, Yehova, timaona kuti n’kofunika kukhala kumbali yosonyeza kuti iye ndiye woyenera kutilamulira. (Machitidwe 5:29) Timafuna ndi mtima wonse kukhala wokhulupirika kuti tikondweretse mtima wake. (Miyambo 27:11) Ndine wosangalala kuti ndili m’gulu la anthu amene asankha ‘kukhulupirira Yehova ndi mtima wawo wonse, osachirikizika pa luntha lawo.’—Miyambo 3:5, 6.

[Mawu Otsindika patsamba 13]

“Tinadabwa kwambiri kuona kuti sanatigwire koma anachita chidwi ndi uthenga wa m’Baibulo”

[Mawu Otsindika patsamba 14]

Mboni za ku Korea zakhala ku ndende zaka zoposa 26,000 chifukwa chokana kulowa usilikali

[Chithunzi patsamba 12]

Tili ku ndende ya asilikali, mu 1953

[Chithunzi patsamba 15]

Tikuyendera mipingo ndi Don Steele panthawi ya nkhondo mu 1952

[Chithunzi patsamba 15]

Mu 1961, tisanakwatirane

[Chithunzi patsamba 15]

Ndikuthandiza woyang’anira woyendayenda kumasulira nkhani mu 1956

[Chithunzi patsamba 15]

Ndili ndi In-hyun Sung masiku ano