March 27– April 2
YEREMIYA 12-16
Nyimbo Na. 135 ndi Pemphero
Mawu Oyamba (Osapitirira 3 min.)
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Aisiraeli Anaiwala Yehova”: (10 min.)
Yer. 13:1-5
—Yeremiya anamvera malangizo a Mulungu oti akabise lamba ngakhale kuti zinali zovuta (jr 51 ¶17) Yer. 13:6, 7
—Yeremiya atayenda ulendo wautali kuti akatenge lamba uja, anapeza kuti anali atawonongeka (jr 52 ¶18) Yer. 13:8-11
—Yehova anasonyeza kuti ubwenzi wolimba umene anali nawo ndi Aisiraeli udzawonongeka, kapena kuti kusokonekera, chifukwa chakuti iwo anali anthu osamva (jr 52 ¶19-20; it-1-E 1121 ¶2)
Kufufuza Mfundo Zothandiza: (8 min.)
Yer. 12:1, 2, 14
—Kodi Yeremiya anafunsa funso lotani ndipo Yehova anamuyankha bwanji? (jr 118 ¶11) Yer. 15:17
—Kodi Yeremiya ankaona bwanji nkhani yosankha anthu ocheza nawo, nanga tingamutsanzire bwanji? (w04 5/1 11 ¶16) Kodi ndaphunzira zotani zokhudza Yehova pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
Kodi ndi mfundo ziti zimene ndaphunzira pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno zimene ndingazigwiritse ntchito mu utumiki?
Kuwerenga Baibulo: (Osapitirira 4 min.) Yer. 13:15-27
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Ulendo Woyamba: (Osapitirira 2 min.) Kapepala koitanira anthu ku Chikumbutso komanso vidiyo—Muuzeni zimene mudzakambirane ulendo wotsatira.
Ulendo Wobwereza: (Osapitirira 4 min.) Kapepala koitanira anthu ku Chikumbutso komanso video
—Muuzeni zimene mudzakambirane ulendo wotsatira. Nkhani: (6 min.) w16.03 29-31
—Mutu: Kodi Anthu a Mulungu Analowa Liti mu Ukapolo wa M’Babulo Wamkulu?
MOYO WATHU WACHIKHRISTU
“Muzithandiza Banja Lanu Kuti Lizikumbukira Yehova” (15 min.) Nkhani Yokambirana. Yambani ndi kuonetsa vidiyo yakuti “Mawu Awa . . . Azikhala Pamtima Pako”—Kucheza ndi Mabanja.
Phunziro la Baibulo la Mpingo: (30 min.) ia mutu 20 ¶14-26 komanso Mfundo Zofunika Kuziganizira patsamba 179
Mfundo Zimene Taphunzira Komanso za Mlungu Wamawa (3 min.)
Nyimbo Na. 48 ndi Pemphero