Akuitanira anthu ku Chikumbutso ku Albania

NDANDANDA YA UTUMIKI KOMANSO MOYO WATHU WACHIKHRISTU March 2017

Zitsanzo za Ulaliki

Zitsanzo za ulaliki wa Nsanja ya Olonda ndiponso zomwe tingachite pophunzitsa anthu za Ufumu wa Mulungu. Gwiritsani ntchito zitsanzozi kuti mupange ulaliki wanuwanu.

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

“Ine Ndili ndi Iwe Kuti Ndikulanditse”

Nthawi imene Yehova Mulungu anasankha Yeremiya kuti akhale mneneri, Yeremiyayo ankaona kuti sangakwanitse. Kodi Yehova anamutsimikizira bwanji kuti angakwanitse?

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

Anasiya Kuchita Zimene Mulungu Ankafuna

Aisiraeli ankaganiza kuti machimo awo angachotsedwe chifukwa cha nsembe zimene ankapereka mwamwambo. Yeremiya anaulula molimba mtima machimo ndiponso chinyengo chawo.

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Kodi Tingagwiritse Ntchito Bwanji Kabuku Kakuti Kodi Ndani Akuchita Chifuniro cha Yehova Masiku Ano?

Muzigwiritsa ntchito kabukuka pothandiza ophunzira Baibulo kuti adziwe za a Mboni za Yehovafe, gulu lathu komanso zimene timachita.

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

Anthu Akamatsogoleredwa ndi Yehova Zinthu Zimawayendera Bwino

Ku Isiraeli, anthu amene ankatsatira malangizo a Yehova Mulungu ankakhala mwamtendere, osangalala komanso zinthu zinkawayendera bwino.

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Kodi Tingagwiritse Ntchito Bwanji Kabuku Kakuti Mverani Mulungu?

Muzigwiritsa ntchito zithunzi ndiponso malemba pophunzitsa mfundo zikuluzikulu za m’Baibulo anthu amene amavutika kuwerenga.

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

Aisiraeli Anaiwala Yehova

Kodi Yehova ankafuna kusonyeza chiyani pamene anauza Yeremiya kuti ayende mtunda wa makilomita pafupifupi 500 kupita kumtsinje wa Firate kukabisa lamba?

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Muzithandiza Banja Lanu Kuti Lizikumbukira Yehova

Kuchita Kulambira kwa Pabanja nthawi zonse komanso m’njira yabwino kungathandize banja lanu kuti lizikumbukira Yehova. Kodi mungathetse bwanji mavuto amene anthu ambiri amakumana nawo okhudza Kulambira kwa Pabanja?