Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YEREMIYA 12-16

Aisiraeli Anaiwala Yehova

Aisiraeli Anaiwala Yehova

Yeremiya anapatsidwa ntchito yovuta kwambiri imene inasonyeza zimene Yehova ankafuna kuchita powononga Aisiraeli osamva a ku Yuda ndiponso ku Yerusalemu.

Yeremiya anagula lamba wansalu

13:1, 2

  • Anamanga lambayo m’chiuno ndipo zinkaimira ubwenzi wolimba umene Aisiraeli akanakhala nawo ndi Yehova

Yeremiya anatenga lambayo n’kupita naye kumtsinje wa Firate

13:3-5

  • Iye anamubisa mumng’alu wa m’phanga n’kubwerera ku Yerusalemu

Yeremiya anabwereranso kumtsinje wa Firate kukatenga lambayo

13:6, 7

  • Anali atawonongeka

Yehova anafotokoza tanthauzo la zimenezi pambuyo poti Yeremiya wamaliza ntchitoyi

13:8-11

  • Ntchitoyi inkaoneka ngati yopanda pake, komabe Yeremiya anamvera ndi mtima wonse ndipo izi zinathandiza kuti Yehova afike anthuwo pamtima