Zekariya 13:1-9

13  “Pa tsiku limenelo,+ kudzakumbidwa chitsime+ kuti a m’nyumba ya Davide ndi anthu okhala mu Yerusalemu adzayeretsedwe ku machimo+ ndi ku zinthu zawo zonyansa.+  Yehova wa makamu wanena kuti, “Pa tsiku limenelo, ndidzathetsa mayina a mafano m’dziko lonseli+ ndipo mafanowo sadzakumbukiridwanso. M’dzikoli ndidzachotsamo aneneri+ komanso mzimu wonyansa.+  Pakadzapezeka munthu aliyense wolosera, bambo ake ndi mayi ake amene anamubereka, adzamuuze kuti, ‘Iwe ufa ndithu, chifukwa walankhula zonama m’dzina la Yehova.’ Ndiyeno bambo ndi mayi akewo adzamulase chifukwa chakuti anali kulosera.+  “Zikadzatero, aneneri azidzachita manyazi pa tsiku limenelo.+ Azidzachita manyazi ndi masomphenya awo pamene akulosera. Sadzavalanso chovala chapadera chaubweya+ kuti anamize anthu.  Mneneri aliyense azidzanena kuti, ‘Ine si mneneri. Ndine mlimi, chifukwa munthu wina anandigula kuti ndikhale kapolo wake kuyambira ndili mnyamata.’  Akadzafunsidwa kuti, ‘Kodi zilonda zimene zili pathupi pakozi watani?’ Iye azidzayankha kuti, ‘Zilonda zimenezi zinabwera chifukwa chomenyedwa m’nyumba ya anthu amene anali kundikonda kwambiri.’”  “Iwe lupanga, nyamuka ukanthe m’busa wanga.+ Ukanthe mwamuna wamphamvu yemwe ndi mnzanga,”+ watero Yehova wa makamu. “Ipha m’busa+ ndipo nkhosa zake zibalalike.+ Ine ndidzakomera mtima nkhosa zonyozeka.”+  “Ndiyeno magawo awiri mwa magawo atatu a anthu a m’dziko lonseli adzaphedwa.+ Koma gawo lachitatu la anthuwo lidzatsalamo,”+ watero Yehova.  “Ine ndidzatenga gawo lachitatulo n’kuliika pamoto+ kuti liyengeke. Ndidzawayenga ngati mmene amayengera siliva+ ndi kuwayeza ngati mmene amayezera golide.+ Gawo limeneli la anthu lidzaitana dzina langa, ndipo ine ndidzawayankha.+ Ndidzanena kuti, ‘Awa ndi anthu anga,’+ ndipo iwo adzanena kuti, ‘Yehova ndi Mulungu wathu.’”+

Mawu a M'munsi