Zekariya 2:1-13

2  Tsopano ndinakweza maso ndipo ndinaona munthu ali ndi chingwe choyezera m’dzanja lake.+  Ndiyeno ndinam’funsa kuti: “Ukupita kuti?” Iye anandiyankha kuti: “Ndikupita kukayeza Yerusalemu kuti ndidziwe kutalika kwa m’litali mwake ndi m’lifupi mwake.”+  Pamenepo mngelo amene anali kulankhula ndi ine uja ananyamuka n’kumapita, ndipo kunabwera mngelo wina kudzakumana naye.  Mngeloyo anauza mnzakeyo kuti: “Thamanga ukauze mnyamata uyo kuti, ‘“Mu Yerusalemu mudzakhala anthu ngati mudzi wopanda mpanda+ chifukwa cha kuchuluka kwa anthu ndi ziweto zimene zili mmenemo.+  Ine ndidzamuzungulira ngati mpanda wake wamoto+ ndipo ndidzamudzaza ndi ulemerero wanga,”’ watero Yehova.”+  “Fulumirani! Fulumirani anthu inu! Thawani m’dziko la kumpoto,”+ watero Yehova. “Anthu inu, ndinakubalalitsirani kutali kumbali zonse za dziko lapansi,”*+ watero Yehova.  “Fulumira Ziyoni!+ Thawa, iwe amene ukukhala ndi mwana wamkazi wa Babulo.+  Pambuyo popatsidwa ulemerero,+ Mulungu wandituma kwa anthu a mitundu ina amene anali kukulandani zinthu zanu,+ pakuti Yehova wa makamu wanena kuti, ‘Amene akukukhudzani,+ akukhudza mwana wa diso langa.+  Ine ndikuwaloza mowaopseza,+ ndipo adzatengedwa ndi akapolo awo kuti akhale chuma cha akapolowo.’+ Ndithu, anthu inu mudzadziwa kuti Yehova wa makamu wandituma.+ 10  “Fuula kwambiri ndi kusangalala, iwe mwana wamkazi wa Ziyoni,+ pakuti ine ndikubwera+ ndipo ndidzakhala mwa iwe,”+ watero Yehova. 11  “Mitundu yambiri ya anthu idzadziphatika kwa Yehova pa tsikulo,+ choncho adzakhala anthu anga.+ Ine ndidzakhala mwa iwe.” Ndipo udzadziwa kuti Yehova wa makamu wandituma kwa iwe.+ 12  Yehova adzatenga Yuda kukhala gawo lake m’dziko loyera,+ ndipo adzasankha Yerusalemu.+ 13  Anthu nonsenu, khalani chete pamaso pa Yehova,+ pakuti iye wanyamuka+ m’malo ake oyera okhalamo.+

Mawu a M'munsi

Mawu ake enieni, “ngati mphepo zinayi zam’mlengalenga.”