Zekariya 5:1-11

5  Kenako ndinakweza maso anga ndipo ndinaona mpukutu ukuuluka.+  Iye anandifunsa kuti: “Ukuona chiyani?”+ Ine ndinayankha kuti: “Ndikuona mpukutu ukuuluka. Mpukutuwo ndi wautali mikono* 20 ndipo m’lifupi mwake ndi wautali mikono 10.”  Ndiyeno anandiuza kuti: “Ili ndi temberero limene likubwera padziko lonse lapansi,+ chifukwa aliyense amene akuba+ sakulandira chilango, monga mmene temberero limene lalembedwa kumbali imodzi ya mpukutuwo likunenera. Komanso aliyense amene akulumbira mwachinyengo+ sakulandira chilango, monga mmene temberero limene lalembedwa kumbali inayo ya mpukutuwo likunenera.+  Yehova wa makamu wanena kuti, ‘Ine ndatumiza mpukutuwo kuti ukalowe m’nyumba ya munthu wakuba ndi m’nyumba ya munthu wolumbira mwachinyengo m’dzina langa.+ Mpukutuwo upita kukakhala m’nyumba mwake n’kuwonongeratu nyumbayo, matabwa ake ndi miyala yake.’”+  Kenako mngelo amene anali kulankhula ndi ine uja anandiyandikira n’kundiuza kuti: “Kweza maso ako uone chimene chikubwera.”  Choncho ndinafunsa kuti: “N’chiyani chimenechi?” Iye anandiyankha kuti: “Chimenechi ndi chiwiya choyezera chokwana muyezo wa efa.”* Ndiyeno anapitiriza kunena kuti: “Umu ndi mmene amaonekera anthu oipa a padziko lonse lapansi.”  Tsopano chivundikiro chamtovu cha chiwiya choyezeracho chinavundukulidwa, ndipo mkati mwa chiwiyacho, ndinaonamo mkazi atakhala pansi.  Mngelo uja anandiuza kuti: “Mkazi ameneyu dzina lake ndi Kuipa.” Kenako anamukankha n’kumubwezera m’chiwiya choyezera chokwana muyezo wa efacho,+ ndipo anavundikira chiwiyacho ndi chivundikiro chake chamtovu chija.  Ndiyeno ndinakweza maso ndipo ndinaona akazi awiri akubwera. Akaziwo anali kuuluka ndi mapiko ooneka ngati a dokowe ndipo mphepo inali kuwomba mapikowo. Iwo ananyamula chiwiya choyezera chija n’kupita nacho m’mwamba, pakati pa dziko lapansi ndi kumwamba. 10  Choncho ndinafunsa mngelo amene anali kulankhula ndi ine uja kuti: “Chiwiya choyezeracho akupita nacho kuti?” 11  Iye anandiyankha kuti: “Akupita nacho kudziko la Sinara+ kuti akamangire+ mkaziyo nyumba kumeneko. Akamumangira nyumba yolimba ndipo akamukhazika kumeneko pamalo ake oyenera.”

Mawu a M'munsi

Mkono umodzi ndi wofanana ndi masentimita 44 ndi hafu.
“Muyezo wa efa” ndi wofanana ndi chitini cha malita 22.