Zekariya 10:1-12

10  “Pemphani Yehova kuti akugwetsereni mvula+ pa nthawi ya mvula yomalizira.+ Pemphani Yehova amene anapanga mitambo yamvula+ ndiponso amene amagwetsera anthu mvula yamphamvu.+ Iye amapereka mbewu m’munda mwa munthu aliyense.+  Aterafi*+ amalankhula zoipa. Ochita zamaula amaona masomphenya onama+ ndipo amafotokoza maloto opanda pake. Iwo saphula kanthu polimbikitsa anthu.+ N’chifukwa chake adzasochere ngati nkhosa.+ Iwo adzavutika chifukwa adzakhala opanda m’busa.+  “Mkwiyo wanga wayakira abusa,+ ndipo atsogoleri awo oipa ngati mbuzi+ ndiwaimba mlandu.+ Pakuti ine Yehova wa makamu ndacheukira gulu langa la nkhosa.+ Ndacheukira nyumba ya Yuda ndipo ndaisandutsa hatchi+ yanga yaulemerero, yokwera popita kunkhondo.  M’nyumba ya Yuda mudzatuluka mtsogoleri.+ Mudzatulukanso wolamulira ndi wothandiza,+ komanso mudzatuluka uta womenyera nkhondo.+ Kapitawo aliyense adzatuluka mwa iye.+ Anthu onsewa adzatuluka mwa iye.  Onsewa adzakhala ngati amuna amphamvu+ opondaponda matope a m’misewu ya kunkhondo.+ Iwo adzamenya nkhondo pakuti Yehova ali nawo.+ Adani awo oyenda pamahatchi adzachita manyazi.+  Ndidzachititsa nyumba ya Yuda kukhala yapamwamba ndipo nyumba ya Yosefe ndidzaipulumutsa.+ Ndidzawachitira chifundo ndipo ndidzawapatsa malo okhala.+ Iwo adzakhala ngati sanakanidwepo chiyambire.+ Pakuti ine ndine Yehova Mulungu wawo ndipo ndidzawayankha.+  A nyumba ya Efuraimu adzakhala ngati munthu wamphamvu+ ndipo adzasangalala mumtima mwawo ngati kuti amwa vinyo.+ Ana awo aamuna adzaona zimenezi ndipo adzakondwera.+ Mitima yawo idzakondwera chifukwa cha Yehova.+  “‘Ndidzawaitana ndi likhweru+ ndi kuwasonkhanitsa pamodzi. Ndithu ine ndidzawawombola,+ ndipo iwo adzachuluka ngati anthu amene kale anali ambiri.+  Ndidzawamwaza ngati mbewu pakati pa anthu a mitundu ina+ ndipo adzandikumbukira ali kumadera akutali.+ Iwowo ndi ana awo adzapezanso mphamvu ndipo adzabwerera.+ 10  Ndidzawabweretsa kuchokera kudziko la Iguputo.+ Ndidzawasonkhanitsa pamodzi kuchokera ku Asuri.+ Ndidzawabweretsa kudera la Giliyadi+ ndi la Lebanoni chifukwa chakuti malo okwanira anthu onsewo sadzapezeka.+ 11  Ndidzadutsa panyanja, nyanjayo nditaigwetsera tsoka.+ Ndidzamenya mafunde a nyanjayo+ ndipo madzi onse a mtsinje wa Nailo adzauma.+ Kunyada kwa Asuri kudzathetsedwa+ ndipo ndodo yachifumu+ ya Iguputo idzachoka.+ 12  Ine Yehova ndidzawachititsa kukhala amphamvu+ ndipo zochita zawo zidzalemekeza dzina langa,’+ watero Yehova.”

Mawu a M'munsi

Onani mawu a m’munsi pa Ge 31:19.