Zekariya 14:1-21

14  “Tamverani! Tsiku la Yehova likubwera.+ Adani anu adzakulandani zinthu zanu n’kuzigawana ali mumzinda wanu womwewo.  Ndidzasonkhanitsa mitundu yonse ya anthu kuti imenyane ndi Yerusalemu.+ Mzindawu udzalandidwa,+ katundu wa m’nyumba adzatengedwa ndipo akazi adzagwiriridwa.+ Hafu ya anthu a mumzindawu idzatengedwa kupita kudziko lina,+ koma anthu otsala+ sadzachotsedwa mumzindawu.+  “Yehova adzapita kukamenyana ndi anthu a mitundu inawo+ ngati mmene anachitira pomenyana ndi adani ake m’mbuyomu.+  Pa tsiku limenelo mapazi ake adzaponda paphiri la mitengo ya maolivi. Phiri limeneli lili moyang’anizana ndi Yerusalemu kumbali ya kum’mawa.+ Phiri la mitengo ya maolivi+ limeneli lidzagawanika pakati+ kuyambira kum’mawa mpaka kumadzulo. Zikadzatero, pakati pa mapiriwo padzakhala chigwa chachikulu kwambiri. Hafu imodzi ya phirilo idzasunthira kumpoto ndipo hafu inayo idzasunthira kum’mwera.  Anthu inu mudzathawira kuchigwa chimene chidzakhale pakati pa mapiri anga,+ chifukwa chakuti chigwacho chidzafika mpaka ku Azeli. Mudzathawa ngati mmene munachitira pothawa chivomezi chimene chinachitika m’masiku a Uziya, mfumu ya Yuda.+ Ndithu, Yehova Mulungu wanga adzabwera+ limodzi ndi oyera onse.+  “Pa tsiku limenelo, sipadzakhala kuwala kwapadera.+ Zinthu zidzaundana chifukwa cha kuzizira kwambiri.+  Tsiku limenelo lidzatchedwa tsiku la Yehova.+ Sikudzakhala masana kapena usiku,+ chifukwa ngakhale usiku kudzakhala kukuwalabe.+  Pa tsiku limenelo madzi amoyo+ adzatuluka mu Yerusalemu.+ Hafu ya madziwo idzapita kunyanja ya kum’mawa+ ndipo hafu inayo idzapita kunyanja ya kumadzulo.+ Zimenezi zidzachitika m’chilimwe ndiponso m’nyengo yozizira.+  Yehova adzakhala mfumu ya dziko lonse lapansi.+ Pa tsiku limenelo, Yehova adzakhala mmodzi+ ndipo dzina lake lidzakhala limodzi.+ 10  “Dziko lonse lidzasintha ndi kukhala ngati chigwa cha Araba+ kuyambira ku Geba+ kukafika ku Rimoni+ kum’mwera kwa Yerusalemu. Mzindawu udzakwezedwa pamalo ake ndipo anthu adzakhalamo.+ Anthuwo adzakhalamo kuyambira ku Chipata cha Benjamini+ mpaka ku Chipata Choyamba, kukafika ku Chipata cha Pakona. Komanso adzakhala kuyambira ku Nsanja ya Hananeli+ mpaka kukafika kumalo a mfumu oponderamo mphesa. 11  Anthu adzakhala mumzindawo ndipo simudzakhalanso zinthu zoyenera kuwonongedwa.+ Anthu okhala mu Yerusalemu, adzakhala mmenemo ali otetezeka.+ 12  “Mliri umene Yehova adzagwetsere anthu onse a mitundu ina amene adzamenyane ndi Yerusalemu ndi uwu:+ Munthu aliyense mnofu wake udzawola ali chiimire,+ maso ake adzawola ali m’malo mwake ndiponso lilime lake lidzawola m’kamwa mwake. 13  “Pa tsiku limenelo Yehova adzawasokoneza kwambiri.+ Aliyense adzagwira dzanja la mnzake, ndipo aliyense adzamenya mnzake ndi dzanja lake. 14  Yuda nayenso adzamenya nkhondo mothandizana ndi Yerusalemu, ndipo adzasonkhanitsa chuma cha anthu a mitundu yonse yowazungulira. Adzasonkhanitsa golide, siliva ndi zovala zambirimbiri.+ 15  “Mliri wofanana ndi umenewu udzagweranso mahatchi, nyulu,* ngamila, abulu amphongo ndi chiweto cha mtundu uliwonse chimene chidzapezeke m’misasa ya adaniwo. 16  “Aliyense wotsala mwa anthu a mitundu yonse amene akubwera kudzamenyana ndi Yerusalemu,+ azidzapita kukagwadira Mfumu,+ Yehova wa makamu,+ chaka ndi chaka,+ ndi kukachita nawo chikondwerero cha misasa.+ 17  Aliyense wochokera m’mabanja+ a padziko lapansi, amene sadzapita+ ku Yerusalemu kukagwadira Mfumu, Yehova wa makamu, mvula sidzagwa m’dziko lake.+ 18  Ngati banja la Iguputo silidzabwera mumzindawu, m’dziko lawonso simudzagwa mvula. Mliri umene Yehova adzagwetsere mitundu ina ya anthu amene sazidzabwera kudzachita chikondwerero cha misasa, udzawagwera. 19  Chimenechi chidzakhala chilango cha Iguputo chifukwa cha tchimo lake komanso chifukwa cha tchimo la anthu onse a mitundu ina amene sazidzabwera kudzachita nawo chikondwerero cha misasa.+ 20  “Pa tsiku limenelo, pamabelu a mahatchi padzalembedwa mawu+ akuti ‘Chiyero n’cha Yehova!’+ Ndipo miphika yakukamwa kwakukulu+ ya m’nyumba ya Yehova adzaigwiritsa ntchito ngati mbale zolowa+ za paguwa lansembe.+ 21  Mphika uliwonse wakukamwa kwakukulu mu Yerusalemu ndi mu Yuda udzakhala woyera ndipo udzakhala wa Yehova wa makamu. Anthu onse amene azidzapereka nsembe azidzabwera n’kutengako ina mwa miphikayo ndi kuphikiramo.+ Pa tsiku limenelo, m’nyumba ya Yehova wa makamu+ simudzapezeka Mkanani.”+

Mawu a M'munsi

“Nyulu” ndi nyama yooneka ngati hatchi.