Zekariya 6:1-15

6  Ndinakwezanso maso ndipo ndinaona magaleta anayi akubwera kuchokera pakati pa mapiri awiri. Mapiriwo anali amkuwa.  Galeta loyamba linali kukokedwa ndi mahatchi ofiira,+ ndipo galeta lachiwiri linali kukokedwa ndi mahatchi akuda.+  Galeta lachitatu linali kukokedwa ndi mahatchi oyera,+ ndipo galeta lachinayi linali kukokedwa ndi mahatchi amawangamawanga.+  Ndiyeno ndinafunsa mngelo amene anali kulankhula ndi ine uja kuti: “Kodi magaleta amenewa akuimira chiyani mbuyanga?”+  Mngeloyo anandiyankha kuti: “Magaletawa akuimira zolengedwa zauzimu zinayi+ zakumwamba zimene zikubwera+ pambuyo poimirira pamaso pa Ambuye+ wa dziko lonse lapansi.+  Mahatchi akuda amene akukoka galeta akupita kudziko la kumpoto.+ Mahatchi oyera akupita kutsidya la nyanja. Mahatchi amawangamawanga akupita kudziko la kum’mwera.+  Mahatchi amawangamawanga+ apitanso kukafufuza koti alowere kuti azikayendayenda mbali ina ya dziko lapansi.”+ Kenako iye anauza mahatchiwo kuti: “Pitani, mukayendeyende padziko lapansi.” Mahatchiwo anapita n’kumakayendayenda padziko lapansi.  Mngelo uja anandiitana mofuula n’kundiuza kuti: “Taona, mkwiyo+ umene Yehova anali nawo padziko la kumpoto watha chifukwa cha mahatchi amene apita kumeneko.”+  Yehova anapitiriza kulankhula nane kuti: 10  “Ukalandire chopereka kuchokera kwa anthu amene anatengedwa kupita kudziko lina.+ Ukalandire choperekacho kwa Heledai, Tobiya ndi Yedaya. Iweyo upite pa tsiku loikidwiratu, ndipo ukalowe m’nyumba ya Yosiya mwana wa Zefaniya,+ kumene kuli anthu ochokera ku Babulowo. 11  Pa choperekacho ukatengepo siliva ndi golide n’kupangira chisoti chachifumu chaulemerero.+ Chisoticho udzaveke Yoswa+ mkulu wa ansembe, mwana wa Yehozadaki. 12  Ndiyeno udzamuuze kuti,“‘Yehova wa makamu wanena kuti: “Munthu uyu+ dzina lake ndi Mphukira.+ Adzaphuka pamalo ake ndipo adzamanga kachisi wa Yehova.+ 13  Munthu ameneyu adzamanga kachisi wa Yehova ndipo adzalandira ulemerero.+ Iye azidzalamulira atakhala pampando wake wachifumu ndipo adzakhalanso wansembe ali pampando womwewo.+ Maudindo awiri onsewo adzakhala ogwirizana.+ 14  Chisoti chachifumu chaulemererocho chizidzakhala m’kachisi wa Yehova kuti anthu azidzakumbukira+ Helemu, Tobiya, Yedaya+ ndi Heni mwana wa Zefaniya. 15  Anthu amene ali kutali, ndithu adzabwera kudzamanga nawo kachisi wa Yehova.”+ Anthu inu mukadzamvera mawu a Yehova Mulungu wanu,+ mudzadziwa kuti Yehova wa makamu wandituma kwa inu.’”+

Mawu a M'munsi