Pitani ku nkhani yake

N’chifukwa Chiyani Pali Zipembedzo Zambiri Zimene Zimati N’zachikhristu?

N’chifukwa Chiyani Pali Zipembedzo Zambiri Zimene Zimati N’zachikhristu?

Yankho la m’Baibulo

 Anthu akhazikitsa zipembedzo zambiri zimene amati n’zachikhristu pogwiritsa ntchito zimene Yesu ankaphunzitsa. Komabe Baibulo limasonyeza kuti pali chipembedzo chimodzi chokha chachikhristu chimene n’cholondola. Tiyeni tione zifukwa zitatu zimene zikutipangitsa kunena zimenezi.

  1.   Yesu ananena kuti ankaphunzitsa “choonadi,” ndipo AKhristu oyambirira ankatchula chipembedzo chawo kuti “choonadi.” (Yohane 8:32; 2 Petulo 2:2; 2 Yohane 4; 3 Yohane 3) Zimene mavesiwa anena zikusonyeza kuti zipembedzo zimene zimachita zinthu zosemphana ndi zimene Yesu ankaphunzitsa si zipembedzo zoona zachikhristu.

  2.   Baibulo limanena kuti Akhristu onse ‘azilankhula mogwirizana.’ (1 Akorinto 1:10) Komabe zipembedzo zambiri zimene zimati n’zachikhristu zimaphunzitsa mfundo zosiyana zokhudza zimene Akhristu ayenera kutsatira. Kunena zoona zipembedzo zimenezi sizingakhale zolondola.​—1 Petulo 2:21.

  3.   Yesu ananeneratu kuti anthu ambiri azidzanena kuti ndi Akhristu koma adzalephera kumvera malamulo choncho iye adzawakana. (Mateyu 7:21-23; Luka 6:46) Anthu ena adzasokonezedwa ndi atsogoleri azipembedzo amene azidzaphunzitsa zinthu zonama pofuna kukwaniritsa zofuna zawo. (Mateyu. 7:15) Komabe anthu ena adzasankha kukhala kumbali ya zipembedzo zimene zimati n’zachikhristuzi chifukwa zimaphunzitsa zimene iwowo amafuna osati zimene Baibulo limanena.​—2 Timoteyo 4:3, 4.

 M’fanizo lake la tirigu ndi namsongole, Yesu ananeneratu kuti mumpingo wa Chikhristu mudzalowa anthu ampatuko. (Mateyu 13:24-30, 36-43) Yesu anasonyeza kuti kwa nthawi yaitali kudzakhala kovuta kuzindikira Akhristu enieni ndi Akhristu abodza. Choncho atumwi atafa anthu ena anayamba mpatuko monga mmene Yesu ananenera. (Machitidwe 20:29, 30) Ngakhale kuti zipembedzo zimene zimati n’zachikhristu zimaphunzitsa zosiyana, zipembedzo zonsezo ‘zapatuka pa choonadi.’​—2 Timoteyo 2:18.

 Yesu ananenanso kuti n’kupita kwa nthawi kusiyana pakati pa chipembedzo choona ndi zipembedzo zimene zimati n’zachikhristu kudzaonekera. Zimenezi zikuchitika masiku athu ano omwe amatchedwa “mapeto a nthawi ino.”​—Mateyu 13:30, 39.