Pitani ku nkhani yake

Kodi Mulungu Anayamba Liti Kulenga Zinthu?

Kodi Mulungu Anayamba Liti Kulenga Zinthu?

Yankho la m’Baibulo

 Baibulo silinena nthawi imene Mulungu anayamba kulenga zinthu kapena nthawi imene anatenga kuti amalize kulenga zinthu. Limangonena kuti: “Pa chiyambi, Mulungu analenga kumwamba ndi dziko lapansi.” (Genesis 1:1) Baibulo silinena kuti pachiyambipo panali liti koma tikaona nkhani yonse ya m’buku la Genesis tikhoza kunena kuti panali isanafike nyengo 6 kapena kuti “masiku” olenga zinthu.

 Kodi anali masiku 6 enieni a maola 24?

 Ayi. M’Baibulo, mawu oti “tsiku” akhoza kutanthauza nthawi yotalika mosiyanasiyana. Mwachitsanzo, malemba ena amanena za tsiku limodzi potanthauza nthawi yonse imene Mulungu analenga zinthu zonse.—Genesis 2:4.

 Kodi chinachitika n’chiyani pa masiku 6 olenga zinthuwa?

 Mulungu anasintha dziko limene linali “lopanda maonekedwe enieni ndiponso lopanda kanthu” n’kukhala malo oti zamoyo zingakhalemo. (Genesis 1:2) Kenako analenga zamoyo padzikoli. Baibulo limatchula zinthu zokwana 6 zimene zinachitika pa nthawi imene amaitchula kuti masiku 6 olenga zinthu.

  •  Tsiku loyamba: Mulungu anachititsa kuti kuwala kufike padziko ndipo panayamba kukhala masana ndi usiku.—Genesis 1:3-5..

  •  Tsiku lachiwiri: Mulungu anapanga m’mlengalenga ndipo anasiyanitsa madzi apansi pa m’mlengalenga ndi apamwamba pake.—Genesis 1:6-8.

  •  Tsiku lachitatu: Mulungu anachititsa kuti mtunda uwonekere. Analenganso zomera.—Genesis 1:9-13.

  •  Tsiku la 4: Mulungu anachititsa kuti dzuwa, mwezi ndi nyenyezi zionekere n’kumaunikira padziko.—Genesis 1:14-19.

  •  Tsiku la 5: Mulungu analenga zamoyo zam’madzi ndi zouluka m’mlengalenga.—Genesis 1:20-23.

  •  Tsiku la 6: Mulungu analenga nyama zapamtunda ndiponso anthu.—Genesis 1:24-31.

 Litatha tsiku la 6, Mulungu anapuma pa ntchito yake kapena kuti anasiya kulenga zinthu.—Genesis 2:1, 2.

 Kodi nkhani ya m’buku la Genesis imagwirizana ndi zimene asayansi amanena?

 Baibulo silifotokoza kulengedwa kwa zinthu mwatsatanetsatane ngati kuti ndi buku la sayansi. Koma limangofotokoza nkhaniyi m’njira yoti ngakhale munthu yemwe analipo kalekale akanatha kumvetsa zimene zinachitika polenga zinthu. Ndipo zimene Baibulo limanenazi sizitsutsana ndi zimene asayansi apeza. Wasayansi wina dzina lake Robert Jastrow analemba kuti: “Tikatengera timfundo ting’onoting’ono tolembedwa mwatsatanetsatane tikhoza kuona kusiyana. Koma mfundo zikuluzikulu zimene asayansi apeza, sizisiyana ndi zimene zili m’Baibulo. Zimaoneka kuti zinthu zinachitika mwadongosolo komanso mofulumira mpaka pamene anthu anayamba kukhala padzikoli pa nthawi inayake.”

 Kodi dzuwa, mwezi ndi nyenyezi zinalengedwa pa nthawi iti?

 Dzuwa, mwezi ndi nyenyezi zinalipo kale “kumwamba” kumene kunalengedwa “pachiyambi.” (Genesis 1:1) Koma zikuoneka kuti kuwala kwake sikunkafika padziko chifukwa choti m’mlengalenga munali mdima wokhawokha. (Genesis 1:2) Choncho ngakhale kuti kuwala kunaoneka padzikoli patsiku loyamba, sizinkadziwika kuti kuwalako kukuchokera kuti. Ndiye zikuoneka kuti kumwambako kunayera patsiku la 4. Baibulo limanena kuti dzuwa, mwezi ndi nyenyezi zinayamba kuunikira padziko lapansi. Izi zikutanthauza kuti tsopano zinali zotheka kuona zinthu zonsezi munthu ali padziko lapansi.

 Kodi Baibulo limati dzikoli lakhalapo kwa nthawi yaitali bwanji?

 Baibulo silinena kuti dzikoli lakhalapo kwa nthawi yaitali bwanji. Lemba la Genesis 1:1 limangonena kuti chilengedwechi kuphatikizapo dziko lapansi zili ndi chiyambi. Mfundo imeneyi sitsutsana ndi asayansi kapena zimene asayansi amanena pa nkhani ya nthawi imene dzikoli lakhalapo.