8 DECEMBER, 2022
NKHANI ZA PADZIKO LONSE
M’bale Dubovenko ndi M’bale Litvinyuk Awagamula Kuti Akakhale Kundende Zaka 6
Pa 30 November 2022, khoti la mumzinda wa Armyanskiy m’chigawo cha Crimea linapereka chigamulo kwa M’bale Aleksandr Dubovenko ndi M’bale Aleksandr Litvinyuk. Abale awiriwa anawalamula kuti akakhale kundende zaka 6 ndipo nthawi yomweyo anawapititsa kundende.
Zokhudza Abalewa
Timalimbikitsidwa kudziwa kuti Yehova ali nafe nthawi zonse kulikonse komwe tili komanso nthawi iliyonse imene tikukumana ndi mavuto.—Salimo 139:7-12.
Nthawi Komanso Zimene Zinachitika
2 August 2021
Mlandu unayamba kuzengedwa. Abale onse awiri anaimbidwa mlandu wogwiritsa ntchito mapulogalamu a kompyuta pavidiyokomfelensi polimbikitsa kagulu kochita zinthu zoopsa
5 August 2021
Apolisi anakafufuza zinthu m’nyumba za mabanja 8 za a Mboni za Yehova kuphatikizapo nyumba ya a Dubovenko ndi a Litvinyuk. M’bale Litvinyuk anamumanga ndi kumuika m’ndende yongoyembekezera
6 August 2021
M’bale Litvinyuk anamutulutsa m’ndende yongoyembekezera ndi kumuika pa ukaidi wosachoka panyumba
9 August 2021
Apolisi anakafufuza kachiwiri zinthu m’nyumba ya a Dubovenko ndipo anawafunsa mafunso ndi kuwaika pa ukaidi wosachoka panyumba
11 August 2021
M’bale Litvinyuk anaimbidwa mlandu wotsogolera kagulu kochita zinthu zoopsa
8 February 2022
M’bale Dubovenko anaimbidwa mlandu wotsogolera kagulu kochita zinthu zoopsa
29 April 2022
Mlandu unayamba kuzengedwa. Jaji anakana pempho la a Litvinyuk lakuti akaonane ndi dokotala kuti akalandire thandizo pa nthawi yomwe anali pa ukaidi wosachoka panyumba
8 September 2022
Pa tsiku, abale onse awiri ankaloledwa kuchoka panyumba zawo pakati pa 7 koloko m’mawa ndi 7 koloko madzulo
30 November 2022
Abale onse awiri anagamulidwa kukakhala kundende za 6