Pitani ku nkhani yake

M’bale Aleksandr Dubovenko ndi Aleksandr Litvinyuk

8 DECEMBER, 2022
NKHANI ZA PADZIKO LONSE

M’bale Dubovenko ndi M’bale Litvinyuk Awagamula Kuti Akakhale Kundende Zaka 6

M’bale Dubovenko ndi M’bale Litvinyuk Awagamula Kuti Akakhale Kundende Zaka 6

Pa 30 November 2022, khoti la mumzinda wa Armyanskiy m’chigawo cha Crimea linapereka chigamulo kwa M’bale Aleksandr Dubovenko ndi M’bale Aleksandr Litvinyuk. Abale awiriwa anawalamula kuti akakhale kundende zaka 6 ndipo nthawi yomweyo anawapititsa kundende.

Zokhudza Abalewa

Timalimbikitsidwa kudziwa kuti Yehova ali nafe nthawi zonse kulikonse komwe tili komanso nthawi iliyonse imene tikukumana ndi mavuto.​—Salimo 139:7-12.

Nthawi Komanso Zimene Zinachitika

 1. 2 August 2021

  Mlandu unayamba kuzengedwa. Abale onse awiri anaimbidwa mlandu wogwiritsa ntchito mapulogalamu a kompyuta pavidiyokomfelensi polimbikitsa kagulu kochita zinthu zoopsa

 2. 5 August 2021

  Apolisi anakafufuza zinthu m’nyumba za mabanja 8 za a Mboni za Yehova kuphatikizapo nyumba ya a Dubovenko ndi a Litvinyuk. M’bale  Litvinyuk anamumanga ndi kumuika m’ndende yongoyembekezera

 3. 6 August 2021

  M’bale  Litvinyuk anamutulutsa m’ndende yongoyembekezera ndi kumuika pa ukaidi wosachoka panyumba

 4. 9 August 2021

  Apolisi anakafufuza kachiwiri zinthu m’nyumba ya a Dubovenko ndipo anawafunsa mafunso ndi kuwaika pa ukaidi wosachoka panyumba

 5. 11 August 2021

  M’bale Litvinyuk anaimbidwa mlandu wotsogolera kagulu kochita zinthu zoopsa

 6. 8 February 2022

  M’bale Dubovenko anaimbidwa mlandu wotsogolera kagulu kochita zinthu zoopsa

 7. 29 April 2022

  Mlandu unayamba kuzengedwa. Jaji anakana pempho la a Litvinyuk lakuti akaonane ndi dokotala kuti akalandire thandizo pa nthawi yomwe anali pa ukaidi wosachoka panyumba

 8. 8 September 2022

  Pa tsiku, abale onse awiri ankaloledwa kuchoka panyumba zawo pakati pa 7 koloko m’mawa ndi 7 koloko madzulo

 9. 30 November 2022

  Abale onse awiri anagamulidwa kukakhala kundende za 6

Ndemanga zawo zonse zinalembedwa asanalandire chigamulo.