Pitani ku nkhani yake

RUSSIA

Anamangidwa Chifukwa Chotsatira Zimene Amakhulupirira

Anamangidwa Chifukwa Chotsatira Zimene Amakhulupirira

Akuluakulu a boma ku Russia akupitirizabe kulimbana ndi a Mboni za Yehova powachitira zankhanza zofanana ndi zomwe zinkachitika m’nthawi ya ulamuliro wa Soviet Union. Kuyambira mu 2017, a Mboni za Yehova akhala akuchitidwa nkhanza zosiyanasiyana monga kumangidwa, kuchitidwa zipikisheni komanso kuikidwa m’ndende. Pofika pa 16 February 2022, a Mboni 79 anali atatsekeredwa m’ndende poyembekezera kuwazenga mlandu ndipo ena mwa iwo anali atagamulidwa kuti akakhale m’ndende, pomwe 28 anagamulidwa kukhala pa ukaidi wosachoka panyumba ndipo 222 analetsedwa kuti asachoke m’dera lomwe amakhala. Onsewa akuimbidwa mlandu wochita nawo zinthu zoopsa, wotsogolera gulu lochita zinthu “zoopsa,” kapena kupereka ndalama zothandizira gululi. Akuluakulu a boma akukayikiranso a Mboni osachepera 398 kuti ali ndi mlandu womwewu ndipo a Mboniwa ndi azaka zapakati pa 20 ndi 91.

Kodi Boma la Russia Likugwiritsa Ntchito bwanji Lamulo Lokhudza Kuchita Zinthu Zoopsa?

Akuluakulu a bomawa amati akuchita zimenezi potengera chigamulo cha mu April 2017 chakuti mabungwe a Mboni atsekedwe, koma chifukwa chinanso n’choti akuluakulu a bomawa akugwiritsa ntchito molakwika Gawo 282 la m’Buku la Malamulo a Zaupandu. Koma zoona zake n’zoti a Mboni za Yehova akuzengedwa milandu chifukwa cholambira Mulungu mwamtendere. Ngati angawapeze olakwa, ena mwa a Mboni omwe anamangidwa akhoza kugamulidwa kuti akhale m’ndende kwa zaka mpaka 10.

Patatha mwezi umodzi kuchokera pamene ntchito ya Mboni za Yehova inaletsedwa, a Dennis Christensen, azaka 48 omwe ndi nzika ya dziko la Denmark anamangidwa mumzinda wa Oryol. Pa 25 May 2017, apolisi onyamula mfuti ndiponso anthu oimira gulu lachitetezo la Federal Security Services, anakasokoneza msonkhano wachipembedzo womwe a Mboni za Yehova ankachita mwamtendere ndipo anamanga a Dennis Christensen n’kukawatsera. Iwo ankaimbidwa mlandu ‘wotsogolera zochita za gulu lochita zinthu zoopsa’ malinga ndi Gawo 282.2(1) la m’buku la malamulo a zaupandu a dziko la Russia. Kenako a Christensen anagamulidwa kuti akakhale kundende zaka 6 pambuyo poimbidwa mlanduwu kwa pafupifupi chaka chimodzi komanso kukaonekera kukhothi maulendo opitilira 50. Iwo anapatsidwa chigamulo chimenechi chifukwa chakuti ankachita zinthu mogwirizana ndi zimene amakhulupilira monga wa Mboni za Yehova. Iwo akuyembekezera kutulutsidwa m’ndende mu May 2022.

Kuyambira mu 2017, apolisi akhala akuchita zipikisheni m’nyumba zambirimbiri za a Mboni. Nthawi zonse akamachita zipikishenizi, apolisi onyamula mfuti amalowa m’nyumba za a Mboni ndipo nthawi zambiri akapezamo anthu, ana ndi achikulire omwe, amawaloza ndi mfuti m’mutu n’kuwakakamiza kuti agone pansi. Akamachita zipikisheni m’nyumbazo, amalanda zinthu komanso kutengera a Mboni ena kupolisi kuti akapitirize kuwafunsa mafunso. Kenako apolisiwo amatsegulira milandu a Mboniwo powaganizira kuti anachita zinthu zoopsa ndipo amapempha makhoti kuti awatsekere m’ndende poyembekezera kuzenga milandu yawo. Pambuyo pake amawapititsa kukhoti komwe amakawapeza kuti ndi olakwa, kuwalipiritsa chindapusa komanso kuwagamula kuti akakhale kundende.

Apolisiwa akupitirizabe kuchita zipikisheni m’nyumba za a Mboni, kuwafunsa mafunso komanso kuwamanga ngakhale kuti pa 28 October 2021, khoti lalikulu kwambiri la ku Russia linagwirizana kuti lisinthe mfundo zina zokhudza kulimbana ndi zinthu zoopsa. Malinga ndi mfundo zatsopano zomwe khotili linanena, munthu akamalambira payekha kapena anthu akamalambira limodzi asamaonedwe kuti akuchita nawo zinthu zachipembedzo choletsedwa. Komabe boma la Russia likuzunzabe a Mboni ponena kuti likuchita zinthu potsatira lamulo lothana ndi anthu ochita zinthu zoopsa. Bomali likuchita zimenezi kwa ana, achikulire komanso kwa amuna ndi akazi omwe.

Zimene Zikuchitika Pofuna Kuthetsa Zotsekera M’ndende Anthu Osalakwa

Maloya oimira a Mboni omwe ali m’ndende anakadandaula za nkhaniyi ku Komiti ya United Nations Yoona za Ufulu wa Anthu komanso ku Gulu la United Nations Loona za Anthu Omangidwa Popanda Zifukwa Zomveka (WGAD). Iwo anatumizanso madandaulo 57 ku Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Europe. Ngakhale kuti ayesetsa kuchita zimenezi, koma sizinaphule kanthu.

Mabungwe osiyanasiyana am’mayiko ena adzudzula boma la Russia chifukwa chogwiritsa ntchito molakwika lamulo lokhudza kuchita zinthu zoopsa pozunza a Mboni za Yehova. Mwachitsanzo, pa 12 March 2020, mabungwe awiri analembera limodzi chikalata chodzudzula akuluakulu a boma la Russia chifukwa chozunza a Mboni za Yehova. Iwo anati: “Bungwe la European Union ndi lodandaula kwambiri chifukwa cha a Mboni za Yehova omwe akuzunzidwabe ku Russia . . . Ndife okhudzidwa kwambiri ndi nkhani zomwe tamva posachedwapa zokhudza nkhanza ndi kuzunza a Mboni za Yehova ambiri omwe ali m’ndende poyembekezera kuwazenga milandu.” Chikalatachi chinanenanso kuti: “Kuzunza anthu ndi kuphwanya lamulo lokhudza ufulu wachibadwidwe womwe anthu padziko lonse ali nawo. (Ndipotu zimene boma la Russia likuchitazi, n’zosiyana kwambiri ndi zimene linavomereza kuti lizitsatira ndi kulemekeza m’zigamulo zotsatirazi: UN Convention against Torture and Other Cruel, Inhuman or Degrading Treatment or Punishment, the International Covenant on Civil and Political Rights and the European Convention on Human Rights).”​—OSCE Permanent Council and the European Union.

Kazembe wa dziko la United Kingdom, dzina lake Neil Bush anafotokoza nkhawa yake m’chikalata chomwe analembera bungwe la OSCE Permanent Council pa 4 March 2021. Iye anati:

Kungochokera pamene [Khoti Lalikulu Kwambiri ku Russia] linapereka chigamulo chake mu 2017, takhala tikuona kuti a Mboni za Yehova ambiri m’madera ochulua ku Russia akutsekeredwa, kufufuzidwa ndiponso kuzengedwa milandu. Ena mwa a Mboniwa ndi a Valentina Baranovskaya ndi a Roman Baranovskiy omwe anamangidwa pa 24 February, komanso a Aleksandr Ivshin omwe anamangidwa pa 10 February. Zimene boma la Russia likuchita zikuchita kusonyezeratu kuti linakonzera dala kuti lizunze a Mboni za Yehova. . . . Tikufuna kukumbutsa boma la Russia kuti monga boma lomwe linasainira kuti lizichita zinthu mogwirizana ndi malonjezo osiyanasiyana okhudza ufulu wa anthu omwe bungwe la OSCE linakhazikitsa, liyesetse kutsatira zimenezi.

Nthawi Komanso Zimene Zinachitika

 1. 16 February 2022

  A Mboni 79 anaikidwa m’ndende.

 2. 12 January 2022

  Unduna Woona Zachilungamo m’dziko la Russia unaika pulogalamu ya JW Library m’gulu la zinthu zoopsa. Pulogalamuyi ndi yoyamba komanso yokhayo imene yaletsedwa ku Russia kuti ndi yoopsa.

 3. 25 October 2021

  Khoti la m’boma la Trusovskiy ku Astrakhan linagamula kuti a Rustam Diarov, a Yevgeniy Ivanov ndi a Sergey Klikunov akakhale kundende zaka 8. Pomwe a Olga Ivanova anagamulidwa kuti akakhale kundende zaka zitatu ndi miyezi 6.

 4. 27 September 2021

  Khoti la mumzinda wa Saint Petersburg linakana pempho la apilo pa chigamulo chomwe chinaperekedwa pa 31 March 2021, chomwe chinanena kuti pulogalamu ya JW Library iletsedwe m’dziko lonse la Russia ndiponso ku Crimea chifukwa ili m’gulu la zinthu zoopsa. Choncho, chigamulo choyamba chomwe khoti linapereka chayamba kale kugwira ntchito.

 5. 23 September 2021

  Khoti la m’boma la Volgograd Traktorozavodsky linagamula kuti a Sergey Melnik ndi a Igor Yegozaryan akakhale kundende zaka 6, pomwe a Valeriy Rogozin akakhale kundende zaka 6 ndi miyezi 5.

 6. 11 August 2021

  Khoti la m’boma la Abinskiy lomwe lili m’dera la Krasnodar linagamula kuti a Vasiliy Meleshko akakhale kundende zaka zitatu litamvetsera mlandu wawo kwa masiku awiri okha.

 7. 30 June, 2021

  Khoti la mumzinda wa Blagoveshchensk lomwe lili m’chigawo cha Amur, linagamula kuti a Aleksey Berchuk akakhale m’ndende zaka 8 pomwe a Dmitriy Golik anagamulidwa kuti akakhale m’ndende zaka 7.

 8. 24 February 2021

  Khoti la mumzinda wa Abakan ku Republic of Khakassia linagamula kuti a Valentina Baranovskaya akakhale kundende zaka ziwiri ndipo mwana wawo Roman Baranovskiy, anagamulidwa kuti akakhale kundende zaka 6.

 9. 10 February 2021

  Khoti la m’boma la Abinskiy lomwe lili m’chigawo cha Krasnodar linagamula kuti a Aleksandr Ivshin akakhale kundende zaka 7 ndi miyezi 6.

 10. 2 September 2020

  Khoti la m’boma la Berezovsky lomwe lili m’chigawo cha Kemerovo linagamula kuti a Sergey Britvin ndi a Vadim Levchuk akakhale m’ndende zaka 4.

 11. 3 August 2020

  Khoti la m’chigawo cha Pskov linalamula kuti a Gennady Shpakovskiy atulutsidwe m’ndende. Khotili linagwirizana ndi zomwe a Shpakovskiy anasankha koma linasintha chigamulo choti akakhale m’ndende zaka 6 ndi hafu, m’malomwake linagamula kuti azitsatira malamulo ena ali kunyumba kwawo kwa zaka 6 ndi hafu.

 12. 13 July 2020

  Apolisi anachita zipikisheni m’nyumba pafupifupi 100 za a Mboni m’zigawo za ku Voronezh ndi ku Belgorod.

 13. 9 June 2020

  Khoti la mumzinda wa Pskov linapeza kuti a Gennady Shpakovskiy azaka 61 ndi olakwa ndipo linagamula kuti akakhale m’ndende zaka 6 ndi hafu.

 14. 6 February 2020

  Pa 19 September 2019, khoti linapeza kuti a Mboni 6 ndi olakwa ndipo 5 mwa amenewa anawasamutsira ku ndende yokhaulitsiraku akaidi (Penal Colony No1) ku Orenburg. Atangofika kundendeyi, alonda andende anawamenya kwambiri, kuwamenya ndi mateche mobwerezabwereza komanso kuwamenya ndi zibonga. A Makhammadiyev anathyoka nthiti, kuvulala mapapo ndiponso impso.

 15. 19 September 2019

  Woweruza milandu kukhoti la m’boma la Leninskiy ku Saratov dzina lake Dmitry Larin anagamula kuti a Mboni 6 akakhale kundende chifukwa chowaganizira kuti ‘amatsogolera pochita zinthu zoopsa.’ Mayina awo ndi: A Konstantin Bazhenov, a Aleksey Budenchuk, a Feliks Makhammadiyev, a Roman Gridasov, a Gennadiy German, ndiponso a Aleksey Miretskiy.

 16. 23 May 2019

  Khoti la m’chigawo cha Oryol linakana pempho la a Dennis Christensen ndipo linagwirizana ndi chigamulo chomwe chinaperekedwa poyamba chakuti akakhale kundende zaka 6.

 17. April 26, 2019

  Gulu la United Nations Loona za Anthu Omangidwa Popanda Zifukwa Zomveka linapeza kuti a Dimtriy Mikhailov anaphwanyiridwa ufulu wawo ndipo linatsutsa zimene boma la Russia likuchita pozunza a Mboni za Yehova.

 18. 6 February 2019

  Khoti la m’boma la Zheleznodorozhniy linapeza kuti a Dennis Christensen ndi olakwa ndipo linagamula kuti akakhale kundende zaka 6.

 19. 9 October 2018

  Apolisi komanso asilikali apadera anachita zipikisheni m’nyumba za a Mboni ku Kirov. Azibambo ambirimbiri a Mboni anamangidwa kuphatikizapo a Andrzej Oniszczuk, omwe ndi nzika ya dziko la Poland ndipo anawatsekera m’ndende poyembekezera kuwazenga mlandu.

 20. 15 July 2018

  Apolisi anachita zipikisheni m’nyumba zambiri za a Mboni ku Penza. A Vladimir Alushkin anamangidwa ndipo anawatsekera m’ndende poyembekezera kuwazenga mlandu.

 21. 4 July 2018

  Apolisi anachita zipikisheni m’nyumba za a Mboni ku Omsk. A Sergey ndi a Anastasiya Polyakov anamangidwa ndi kuwatsekera m’ndende poyembekezera kuwazenga mlandu. Mayi Polyakova ndi wa Mboni wamkazi woyamba kumangidwa pa mlandu wochita zinthu zoopsa ku Russia.

 22. 12 June 2018

  Apolisi anachita zipikisheni m’nyumba za a Mboni ku Saratov. A Konstantin Bazhenov, a Aleksey Budenchuk, ndi a Feliks Makhammadiyev anamangidwa ndipo anaikidwa m’ndende poyembekezera kuwazenga mlandu. A Mboni ena atatu omwe ndi a Gennadiy German, a Roman Gridasov, ndiponso a Aleksey Miretskiy analamulidwa kuti asainire chikalata chovomereza kuti satuluka mumzinda wawo.

 23. 3 June 2018

  Apolisi anachita zipikisheni m’nyumba za a Mboni ku Tomsk ndi ku Pskov. A Sergey Klimov anamangidwa ndi kuikidwa m’ndende poyembekezera kuwazenga mlandu.

 24. 19 February 2018

  Khoti la m’boma la Zheleznodorozhniy linayamba kuzenga mlandu wa a Dennis Christensen. Ndipo woweruza wake anali a Aleksey Rudnev.

 25. 20 July 2017 mpaka November 2018

  Kwa maulendo angapo a Dennis Christensen anawaonjezera nthawi yokhala m’ndende poyembekezera kuwazenga mlandu. Khoti loyamba kuwaonjezera nthawiyi linali la m’boma la Sovietskiy kenako khoti la m’boma la Zheleznodorozhniy.

 26. 26 May 2017

  Khoti la m’boma la Sovietskiy ku Oryol linagamula kuti a Dennis Christensen akakhale kundende kwa miyezi iwiri poyembekezera kuwazenga mlandu.

 27. 25 May 2017

  Apolisi anakachita chipikisheni pa nthawi ya misonkhano yachipembedzo ku Oryol ndipo anamanga a Dennis Christensen.

 28. 20 April 2017

  Khoti Lalikulu Kwambiri m’dziko la Russia linagamula kuti ofesi ya Mboni za Yehova ya m’dzikolo komanso mabungwe 395 oimira a Mboni m’dzikolo zitsekedwe.