Pitani ku nkhani yake

Nyumba Yosonyeza Mbiri ya Mboni za Yehova

Nyumba Yosonyeza Mbiri ya Mboni za Yehova

Mu October 2012, a Mboni za Yehova anatsegulira nyumba yawo yosungiramo zinthu zakale yomwe ili kulikulu lawo ku Brooklyn m’dera la New York. * M’nyumbayi aikamo zinthu zosonyeza mavuto osiyanasiyana amene anakumana nawo komanso mmene anapambanira pamene anthu ena ankalimbana nawo chifukwa chachikhulupiriro chawo. M’nyumbayi anaikamo zinthu zothandiza munthu kudziwa yekha mbiri ya Mboni za Yehova mosachita kumufotokozera.

M’nyumbayi anaikamo zinthu zosonyeza mbiri yathu mogwirizana ndi nthawi, kuyambira Chikhristu chitangoyamba kumene mu 33 C.E. mpaka kudzafika m’nthawi yathu ino. Nyumbayi ili ndi zigawo 4 ndipo chigawo chilichonse chikusonyeza nthawi imene zinthu zimene zili m’chigawocho zinkachitika. Komanso chigawo chilichonse chili ndi mutu wochokera m’Baibulo. Munthu akafika m’chigawocho amayamba n’kuonera kavidiyo ka m’Chingelezi kosonyeza zimene zili m’chigawocho. Munthu angasankhe kuti aziona mawu a m’kavidiyoko m’zinenero zina 6, zomwe ndi Chifulenchi, Chitaliyana, Chijapanizi, Chikoreya, Chipwitikizi ndi Chisipanishi.

Zigawo Zikuluzikulu Zimene Zili M’nyumbayi

Chigawo choyamba chili ndi mutu wakuti “Anthu Akonda Mdima,” wochokera pa mawu a Yesu opezeka palemba la Yohane 3:19. Baibulo linalosera kuti anthu oipa “adzayamba kulankhula zinthu zopotoka.” (Machitidwe 20:30) Zimene anthu oipawo anachita zasonyezedwa bwino motsatira nthawi.

Chigawo chachiwiri chili ndi mutu wakuti “Kuwala Kuunike,” wochokera palemba la 2 Akorinto 4:⁠6. M’chigawo chimenechi muli zimene zinachitika kuyambira chakumapeto kwa zaka za m’ma 1800 mpaka kumayambiriro kwa zaka za m’ma 1900. Chigawochi chinayamba ndi kufotokoza nkhani ya kagulu ka amuna angapo amene anayamba kuphunzira Baibulo mwakhama n’kumatsatira zimene likunena osati kuikapo maganizo awo. Nkhaniyi imafotokozanso mmene kaguluko kanakulira komanso kanadziwira zinthu zambiri nkhondo yoyamba ya padziko lonse isanayambe.

Mbali yachiwiri ya chigawochi ikusonyeza sewero lotchuka lapakanema lotchedwa “Sewero la Chilengedwe.” Mu 1941, Ophunzira Baibulo (dzina limene a Mboni za Yehova ankadziwika nalo) anayamba kuonetsa sewero lapakanemali, lomwe linali ndi zithunzi zosayenda komanso zinthunzi zina zoyenda zokhalanso ndi mawu. M’zaka zotsatira, anthu mamiliyoni ambirimbiri ankakhamukira kumalo amene ankaonetsa seweroli. M’chigawochi mulinso zithunzi zenizeni zingapo zimene zinali m’seweroli. Kuwonjezera pamenepa, muli kavidiyo kamene kanatengedwa m’gawo loyambirira la sewerolo komanso zithunzi zakalala zoposa 500.

Chigawo chachitatu cha nyumba yosungiramo zinthu zakaleyi chili ndi mutu wakuti “Chinjokacho Chinakwiya,” wochokera pa Chivumbulutso 12:17. Chigawochi chikusonyeza kuzunzidwa kwa otsatira a Khristu chakumayambiriro kwa zaka za m’ma 1900 komanso muli nkhani zolimbikitsa za Akhristu amene anakhalabe olimba pokana kulowerera ndale ndiponso nkhondo. Mulinso kavidiyo kosonyeza nkhani ya munthu wina wa Mboni wotchedwa Remigio Cuminetti, amene anakana kuvala yunifolomu ya asilikali a nkhondo a dziko la Italy ndipo anakana kumenya nawo nkhondo yoyamba ya padziko lonse. Kavidiyo kenanso kakufotokoza za m’bale wina wotchedwa Alois Moser wa ku Austria. Iye anakana kunena mawu akuti “Hitler Mpulumutsi Wathu!” Chifukwa cha zimenezi, iye anachotsedwa ntchito ndipo kenako anaikidwa kundende yozunzirako anthu ya Dachau.

M’chigawochi mulinso malo ena a mdima oyerekezera ndende. M’malo amenewa muli zithunzi za anthu a Mboni za Yehova a m’mayiko ngati Greece, Japan, Poland ndi Serbia, omwe anamangidwa chifukwa cha zimene amakhulupirira.

Chigawo chomaliza cha nyumbayi chili ndi mutu wakuti “Uthenga Wabwino wa Anthu a Mitundu Yonse,” wochokera palemba la Mateyu 24:14. Chigawochi chikusonyeza zochita za Mboni za Yehova kuyambira mu 1950 mpaka kudzafika masiku ano. Zithunzi zambirimbiri zimene zili m’chigawochi zikusonyeza mmene gulu lathu lakulira mofulumira kwambiri, mmene timalalikirira mwakhama ndiponso mmene timakondanirana. Ndipotu ife a Mboni za Yehova timadziwika bwino chifukwa cha zinthu zitatu zimenezi.

Munthu akamaliza kuona zinthu zochititsa chidwi zimene zili m’nyumbayi, angapite pamalo enaake amene ali m’nyumba yomweyi pamene pali makompyuta ndipo angathe kuwerenga nkhani komanso kuona zithunzi za nyumba zotchedwa “Nyumba ya Baibulo” komanso “Chihema cha Brooklyn,” zomwe a Mboni za Yehova ankazigwiritsa ntchito zaka zoposa 100 zapitazo.

N’chifukwa Chiyani Anamanga Nyumbayi?

Ntchito yokonzekera kumanga nyumbayi inatenga chaka chathunthu ndipo ntchito yomanga inatenga miyezi yambiri ndithu. Anthu a Mboni za Yehova padziko lonse anapereka zinthu zosiyanasiyana zakale kwambiri komanso zamtengo wapatali zokhudza gulu lathu n’cholinga choti ziikidwe m’nyumbayi.

N’chifukwa chiyani a Mboni analolera kugwira ntchito yonseyi? Atafunsidwa kuti a Mboni za Yehova azipindula chiyani akabwera kudzaona zimene zili m’nyumba yosungiramo zinthu zakaleyi, m’modzi mwa anthu amene ali m’Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova anabwereza kunena mawu odziwika bwino, akuti: “Kuti tidziwe kumene tikupita, tiyenera kudziwa kumene tikuchokera.”

^ ndime 2 Nyumbayi ili ku 25 Columbia Heights ku Brooklyn m’dera la New York, ndipo imatsegulidwa kuyambira Lolemba mpaka Lachisanu nthawi ya 8 koloko m’mawa mpaka 5 koloko madzulo. Kulowa pakhoma ndi ulele.