Pitani ku nkhani yake

Kale Lathu

Werengani nkhani zokhudza anthu komanso zinthu zosiyanasiyana zimene zakhala zikuchitika m’mbiri ya Mboni za Yehova.

Historical Overview

Kuulutsa Mawu a Uthenga Wabwino

Kodi a Mboni za Yehova ankachita zotani poulutsa Uthenga wa Ufumu kudzera pa wailesi ya WBBR?

“Nyengo Yofunika Kwambiri”

Nsanja ya Olonda inanena kuti nthawi ya Chikumbutso inali “nyengo yofunika kwambiri” ndipo inalimbikitsa anthu kuti azipezeka pa mwambowu. Kodi kalelo anthu ankachita bwanji mwambo wa Chikumbutso?

“Ntchito Yokolola Idakalipo Yambiri”

Ku Brazil kuli a Mboni za Yehova oposa 760,000 amene amaphunzitsa mfundo zoona za m’Baibulo. Kodi ntchito yolalikira inayamba bwanji ku South America?

Zinthu Zinkayenda Bwino Chifukwa cha Chikondi

Ngati munayamba posachedwa kufika pa misonkhano ya Mboni za Yehova, mwina mungadabwe kudziwa zimene tinkachita kale.

Anayamba Kufesa Mbewu za Ufumu ku Portugal

Kodi anthu anakumana ndi mavuto ati pamene anayamba kulalikira ku Portugal, nanga anathana nawo bwanji?

1870 to 1918

Nkhani za Onse Zinathandiza Kufalitsa Uthenga Wabwino ku Ireland

N’chiyani chinathandiza C. T. Russell kuona kuti “m’munda mwayera kale ndipo m’mofunika kukolola”?

Padutsa Zaka 100 Tsopano

Padutsa zaka 100 tsopano kuchokera pamene filimu ya chilengedwe inayamba kuonetsedwa pofuna kuthandiza anthu kukhulupirira kuti Baibulo ndi Mawu a Mulungu.

Sewero Limene Linathandiza Ambiri Kuphunzira Baibulo

Anthu ankatha kuonetsa chidule cha “Sewero la Pakanema la Chilengedwe” kumadera akutali ngakhale kumene kunalibe magetsi.

“Ndikugwira Ntchito Yotamanda Yehova”

Ophunzira Baibulo sankadziwa zambiri pa nkhani yosalowerera ndale koma ankachitabe zinthu moona mtima ndipo zotsatira zake zinali zabwino.

Anakhalabe Okhulupirika pa “Ola la Kuyesedwa”

Werengani kuti mudziwe mmene anthu anachitira chidwi ndi Ophunzira Baibulo chifukwa chosalowerera nkhondo pa nthawi ya nkhondo yoyamba ya padziko lonse mu 1914.

1919 to 1930

“Kwa Amene Apatsidwa Ntchitoyi”

Msonkhano womwe unachitika mu 1919 unali chiyambi cha ntchito yolalikira imene zotsatira zake zinafalikira padziko lonse.

“Tinalimbikitsidwa Kukonda Kwambiri Yehova Ndiponso Kulalikira Mwakhama”

Msonkhano wachigawo wa mu 1922 utachitika, kodi anthu anatsatira bwanji malangizo oti ‘alengeze za Mfumu ndi Ufumu wake’?

Uthenga Wabwino Unayamba Kuwala ku Japan

Makalavani otchedwa Yehu ankathandiza kwambiri polalikira uthenga wa Ufumu ku Japan.

Sewero la Chilengedwe Linali la pa Nthawi Yake

Werengani kuti mudziwe mmene ”Sewero la Chilengedwe” linathandizira a Mboni za Yehova ku Germany pa nthawi imene ankazunzidwa pa nkhondo yachiwiri yapadziko lonse.

“Yehova Anakubweretsani ku France Kuti Muphunzire Baibulo”

Mu 1919 dziko la France linalola kuti anthu a ku Poland asamukire m’dzikolo ndipo izi zinathandiza kuti ena aphunzire Baibulo.

“Ndinali Ngati Kamba Woyenda Ndi Chigoba Chake”

Chakumapeto kwa chaka cha 1929, kunali mavuto aakulu a zachuma. Kodi akopotala kapena kuti apainiya ankapeza bwanji zinthu zofunika pamoyo wawo?

1931 to Present

Ankakondabe Yehova pa Nthawi Zovuta

Pambuyo pa Nkhondo Yachiwiri Yapadziko Lonse, abale omwe ankakhala m’madera a ku Europe ankakumana ndi mavuto ambiri. Kodi tingaphunzire chiyani kwa abale ndi alongo omwe ankakhala pa nthawi yovutayi?

“Musalole Kuti Chilichonse Chikulepheretseni”

Atumiki a nthawi zonse a ku France a zaka za m’ma 1930 anali zitsanzo pa nkhani ya kudzipereka komanso kupirira.

‘Kungatalike Bwanji Ndipo Msewu Ungaipe Bwanji Ankafikako’

Chakumapeto kwa zaka za m’ma 1920 ndi kumayambiriro kwa zaka za m’ma 1930, apainiya akhama anayesetsa kulalikira kumadera akumidzi a ku Australia.

“Kodi Tichitanso Liti Msonkhano Wina?”

N’chifukwa chiyani msonkhano wa mu 1932 wa ku Mexico City umene anthu 150 okha anapezeka ndi wosaiwalika?

Mfumu Inasangalala Kwambiri

Werengani kuti mumve mmene mfumu ya ku Swaziland inkakondera kuphunzira Baibulo.

Boti la Lightbearer Linabweretsa Kuwala kwa Choonadi Kum’mwera Chakum’mawa kwa Asia

Ngakhale kuti ankatsutsidwa, amuna ochepa a m’boti la Lightbearer anafalitsa molimba mtima kuwala kwa choonadi cha m’Baibulo m’dera lalikulu kwambiri lokhala anthu ambiri.

Galimoto Yodziwika Kwambiri Yokhala ndi Zokuzira Mawu

Kuchokera mu 1936 mpaka 1941, galimoto ya zokuzira mawu inathandiza a Mboni za Yehova ochepa a ku Brazil kuti athe kulalikira uthenga wa Ufumu kwa anthu ambiri m’dzikoli.

“Ofalitsa a ku Britain Galamukani!”

Kwa zaka 10, utumiki sunkayenda bwino ku Britain. Kodi n’chiyani chinathandiza kuti ziyambenso kuyenda bwino?

Anapereka Zinthu Zawo Zabwino Kwambiri

Kodi a Mboni za Yehova anathandiza bwanji abale awo a ku Germany nkhondo yachiwiri yapadziko lonse itangotha?

Anapereka Zinthu Zawo Zabwino Kwambiri

Kodi a Mboni za Yehova anathandiza bwanji abale awo a ku Germany nkhondo yachiwiri yapadziko lonse itatangotha?

Anthu Akuphunzitsidwa Kulemba Ndi Kuwerenga Padziko Lonse

Akuluakulu a boma m’mayiko osiyanasiyana akhala akuthokoza a Mboni za Yehova chifukwa cha ntchito yophunzitsa anthu kuwerenga ndi kulemba.