Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

KALE LATHU

“Kodi Tichitanso Liti Msonkhano Wina?”

“Kodi Tichitanso Liti Msonkhano Wina?”

MU NOVEMBER 1932 ku Mexico City atolankhani ankayembekezera kudepoti makamera ali m’manja n’cholinga choti ajambule mlendo wapadera amene ankabwera. Apa n’kuti patangodutsa mlungu umodzi kuchokera pamene atolankhaniwo ankachita chidwi ndi nkhani yoti maloboti oyamba aikidwa mumzinda waukuluwu, womwe unali ndi anthu 1 miliyoni. Koma anasintha msanga n’kuyamba kuchita chidwi ndi mlendo wapaderayu, yemwe anali Joseph F. Rutherford. Pa nthawiyo iye anali pulezidenti wa Watch Tower Society ndipo ankabwera kudzachita nawo msonkhano wa masiku atatu. Nawonso a Mboni amumzindawu anali kudepotiko kuti amulandire M’bale Rutherford.

Magazini ya The Golden Age inati: “Zinkaonekeratu kuti msonkhanowu uthandiza kwambiri kuti Choonadi chipite patsogolo m’dziko la Mexico.” Koma n’chifukwa chiyani tinganene kuti msonkhanowu, womwe panangopezeka anthu 150 okha, unali wofunika kwambiri?

Msonkhanowu usanachitike, ku Mexico kunali a Mboni ochepa kwambiri. Kuyambira mu 1919, kunkachitika misonkhano koma chiwerengero cha mipingo chinkangotsika. Anthu ankaona kuti zinthu zingasinthe mu 1929 pamene ofesi ya nthambi inatsegulidwa mumzinda wa Mexico City. Koma kunali mavuto ena. Mwachitsanzo, pamene panatuluka malangizo oti anthu asamachite bizinezi ali mu utumiki, kopotala wina anakwiya ndipo anasiya ukopotalawu n’kuyambitsa gulu lake la ophunzira Baibulo. Komanso woyang’anira nthambi anachita zinthu zina zosemphana ndi Malemba ndipo anachotsedwa pa udindowu. Choncho a Mboni okhulupirika a ku Mexico ankafunika kulimbikitsidwa.

Ndiyeno M’bale Rutherford atabwera anawathandiza kwambiri. Anakamba nkhani ziwiri zolimbikitsa pamsonkhanowu komanso nkhani zina 5 zomwe zinaulutsidwa pa wailesi. Aka kanali koyamba kuti masiteshoni a wailesi a ku Mexico aulutse uthenga wabwino m’dziko lonse. Pambuyo pa msonkhanowu, woyang’anira nthambi watsopano anakonza zinthu zothandiza kuti ntchito yolalikira iziyenda bwino. Komanso a Mboni anayamba kugwira ntchitoyi ndi mtima wonse ndipo Yehova anawadalitsa.

Msonkhano wa mu 1941 ku Mexico City

Chaka chotsatira, kunali misonkhano yachigawo iwiri. Wina unachitika mumzinda wa Veracruz ndipo wina ku Mexico City. Chiwerengero cha ofalitsa chinayamba kukula chifukwa choti abale ndi alongo ankalalikira mwakhama. Mu 1931 kunali ofalitsa 82. Patapita zaka 10, chiwerengerochi chinawirikiza ka 10. Ndipo mu 1941, anthu pafupifupi 1,000 anabwera ku Mexico City kuti adzapezeke pa msonkhano wina waukulu.

“ANADZAZA M’MISEWU YONSE”

Mu 1943, a Mboni anavala zikwangwani n’cholinga choti aitanire anthu kumsonkhano wakuti “Mtundu Waufulu,” womwe unkachitika m’mizinda 12 ya ku Mexico. * Zikwangwanizo zinamangidwa pamodzi kuti munthu akazikoloweka pamapewa, chimodzi chikhale kutsogolo ndipo china kumbuyo. Kuyambira mu 1936, a Mboni ankagwiritsa ntchito njira imeneyi poitanira anthu ku misonkhano.

Chithunzi chimene chinapezeka m’magazini ina mu 1944 chosonyeza abale atavala zikwangwani zoitanira anthu kumsonkhano ku Mexico City

Magazini yakuti La Nación inafotokoza za ntchito yoitanira anthu kumsonkhanoyi kuti: “Pa tsiku loyamba [la msonkhanowu], [a Mboni] anauzidwa kuti ayenera kuitana anthu ambiri. Koma tsiku lotsatira, anthu anali ambiri moti sanakwane pamalo a msonkhanowo.” Atsogoleri a tchalitchi cha Katolika sanasangalale kuti anthu ambiri anapita kumsonkhanowu moti anayamba kutsutsa kwambiri a Mboni. Ngakhale zinali choncho, abale ndi alongo anali olimba mtima ndipo anapitiriza ntchito yawo yoitanira anthu kumsonkhano. Magaziniyo inati: “Anthu onse mumzindawu anaona . . . amuna ndi akazi omwe atavala zikwangwanizi.” M’magaziniyi munalinso chithunzi cha abale akuyenda m’misewu ya ku Mexico City ndipo m’munsi mwake munali mawu akuti: “Anadzaza m’misewu yonse.”

“MABEDIWO ANALI AWOFUWOFU KOMANSO OTENTHERA”

Pa nthawiyo, sizinali zophweka kuti a Mboni apite kumisonkhano yachigawo ku Mexico. Zinali choncho chifukwa misonkhanoyi inkachitika m’malo ochepa ndipo a Mboni ambiri ankakhala kumadera akumidzi kumene kunalibe misewu kapena njanji. Choncho popita kumisonkhano, anthu ankakwera abulu kapena kuyenda wapansi kwa masiku ambiri kuti akafike pamalo okwerera sitima yopita kumzinda umene msonkhano unkachitikira.

A Mboni ambiri anali osauka ndipo ankavutika kupeza ndalama zokwanira kuti akafike kumsonkhano. Akafika, ankagona kunyumba za a Mboni akumeneko omwe ankawalandira bwino. Koma ena ankagona ku Nyumba za Ufumu. Pa nthawi ina, anthu pafupifupi 90 anagona kunthambi pamabedi opangidwa ndi makatoni a mabuku. Ankapanga bedi lililonse pogwiritsa ntchito makatoni 20. Buku Lapachaka linafotokoza kuti abale ndi alongowo anayamikira kwambiri ndipo anaona kuti “mabediwo anali awofuwofu komanso otenthera kusiyana ndi kugona pasimenti.”

Abale ndi alongo ankayamikira misonkhanoyi kwambiri moti sankadandaula za mavuto amene ankakumana nawo kuti akapezekeko. Panopa chiwerengero cha ofalitsa ku Mexico chatsala pang’ono kukwana 1 miliyoni ndipo abale ndi alongowa amayamikirabe misonkhano. * Mu 1949, lipoti lina lokhudza nthambi ya ku Mexico linafotokoza za abale akumeneko kuti: “Ngakhale kuti amakumana ndi mavuto, amakonda kwambiri kutumikira Mulungu. Umboni wa zimenezi ndi wakuti pambuyo pa msonkhano waukulu uliwonse iwo amapitiriza kulankhula za msonkhanowo kwa nthawi yaitali. Ndipo nthawi zonse amakonda kufunsa kuti, Kodi tichitanso liti msonkhano wina?” Umu ndi mmene alili abale ndi alongo a ku Mexico mpaka pano.​—Nkhaniyi yachokera ku Central America.

^ ndime 9 Mogwirizana ndi Buku Lapachaka la 1944, msonkhanowu unathandiza kuti “a Mboni za Yehova adziwike kwambiri ku Mexico.”

^ ndime 14 Mu 2016, anthu okwana 2,262,646 anapezeka pa Chikumbutso ku Mexico.