Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

A Johannes Rauthe ali pamsonkhano wokonzekera utumiki

 KALE LATHU

“Ndikugwira Ntchito Yotamanda Yehova”

“Ndikugwira Ntchito Yotamanda Yehova”

PONENA za nkhondo yoyamba ya padziko lonse, Nsanja ya Olonda ya September 1, 1915, inafotokoza kuti: “Nkhondo zonse zimene zachitika m’mbuyomu, sizingafanane ndi nkhondo imene ikuchitika ku Europe.” Nkhondoyi inafalikira m’mayiko okwana 30 ndipo Nsanja ya Olonda imeneyi inafotokozanso kuti nkhondoyi inachititsa kuti “ntchito yolalikira [za Ufumu] isokonekere, makamaka ku Germany ndi ku France.”

Ophunzira Baibulo anakumana ndi mavutowa pa nthawi imenenso sankamvetsa bwinobwino nkhani yosalowerera ndale. Koma iwo ankafunitsitsa kulalikirabe uthenga wabwino. Mwachitsanzo, M’bale Wilhelm Hildebrandt anaitanitsa timapepala tina (The Bible Students Monthly) tachifulenchi kuti azigawira anthu. Iye anapita ku France ngati msilikali wachijeremani osati kopotala. Anthu ankadabwa kwambiri kumuona atavala yunifomu ya asilikali koma n’kumagawira anthu a ku France uthenga wonena za mtendere.

Makalata amene anatuluka mu Nsanja ya Olonda anasonyeza kuti Ophunzira Baibulo ambiri ochokera ku Germany ankalalikira ali ku usilikali. Mwachitsanzo, M’bale Lemke anali msilikali wapanyanja ndipo ankalalikira kwa asilikali anzake 5. Iye analemba kuti: “Ndikugwira ntchito yotamanda Yehova m’sitima ya nkhondo.”

Nayenso M’bale Georg Kayser anapita kunkhondo ali msilikali n’kukabwerako ali mtumiki wa Mulungu. Kodi chinachitika n’chiyani? Iye anapeza buku lina la Ophunzira Baibulo, ndipo ataliwerenga anasiya usilikaliwo. Kenako anayamba ntchito yosakhudzana ndi usilikali. Nkhondoyo itatha, anachita upainiya kwa zaka zambiri.

N’zoona kuti pa nthawiyi Ophunzira Baibulo sankadziwa zambiri pa nkhani yosalowerera ndale. Koma zochita zawo zinali zosiyana kwambiri ndi anthu amene ankalimbikitsa nkhondo. Andale ndi atsogoleri azipembedzo ankalimbikitsa nkhondo koma Ophunzira Baibulo ankatsatira “Kalonga  Wamtendere.” (Yes. 9:6) Ngakhale kuti Ophunzira Baibulo ena ankalowerera ndale mosazindikira, maganizo awo ankafanana ndi a M’bale Konrad Mörtter. Iye anati: “Ndinkadziwa bwino kuti Mawu a Mulungu amanena kuti Mkhristu sayenera kupha munthu.”—Eks. 20:13. *

A Hans Hölterhoff akugwiritsa ntchito ngolo ndipo akuuza anthu za magazini yotchedwa The Golden Age

Boma la Germany silinkalola munthu kuti asapite ku nkhondo chifukwa cha zimene munthuyo amakhulupirira. Komabe Ophunzira Baibulo oposa 20 anakana kugwira ntchito zokhudza nkhondo. Chifukwa cha izi, abale ena ankaonedwa ngati mitu yawo sikugwira. Mwachitsanzo, M’bale Gustav Kujath, anamutengera kuchipatala cha amisala n’kumakamupatsa mankhwala. M’bale Hans Hölterhoff anakananso usilikali ndipo anamutsekera kundende. Kundendeko, iye ankakana ntchito iliyonse yokhudzana ndi usilikali. Izi zinachititsa kuti asilikali amumange kwambiri mpaka mikono ndi miyendo yake kuchita dzanzi. Ataona kuti sakusintha maganizo, anamuopseza kuti amupha. Koma iye sanabwerere m’mbuyo mpaka pamene nkhondoyi inatha.

Abale ena amene anakana usilikali anapempha ntchito zina. * Mwachitsanzo, M’bale Johannes Rauthe anapatsidwa ntchito yokonza njanji. M’bale Konrad Mörtter anamupatsa ntchito ya kuchipatala ndipo M’bale Reinhold Weber ankagwira ntchito ya unesi. M’bale August Krafzig anasangalala kuti ntchito imene anapatsidwa sinali yokhudzana ndi usilikali. Abale amene tawatchulawa komanso ena anatsimikiza mumtima mwawo kuti azitumikira Yehova mokhulupirika chifukwa choti amamukonda.

Zimene Ophunzira Baibulo ankachita pa nthawi ya nkhondoyi zinachititsa kuti akuluakulu a boma aziwalondalonda. Kwa zaka zambiri, abale ndi alongo ankaimbidwa milandu chifukwa cholalikira. Ndiyeno ofesi ya nthambi ya ku Germany inakhazikitsa Dipatimenti ya Zamalamulo ku Beteli ya ku Magdeburg kuti izithandiza pa nkhani ngati zimenezi.

Pang’ono ndi pang’ono, a Mboni za Yehova anayamba kumvetsa bwino zoyenera kuchita pa nkhani za ndale. Pamene nkhondo yachiwiri yapadziko lonse inayamba, iwo sanayerekeze n’komwe kulowerera. Izi zinachititsa kuti boma la Germany lizidana nawo ndipo anazunzidwa koopsa. Tidzamva zinanso m’nkhani ya mutu wakuti, “Kale Lathu” imene idzatuluke kutsogoloku.—Nkhaniyi yachokera ku Central Europe.

^ ndime 7 Kuti mudziwe zimene Ophunzira Baibulo a ku Britain anachita pa nkhondo yoyamba ya padziko lonse, werengani Nsanja ya Olonda ya May 15, 2013 pamutu wakuti, “Kale Lathu—Anakhalabe Okhulupirika pa ‘Ola la Kuyesedwa.’”

^ ndime 9 Nkhani ya nkhondoyi inafotokozedwa m’buku lina limene linatuluka mu 1904 (Millennial Dawn, Volume VI) komanso mu Nsanja ya Olonda yachijeremani ya August 1906. Nsanja ya Olonda ya September 1915 inafotokoza bwinobwino zoyenera kuchita ndipo inasonyeza kuti Ophunzira Baibulo sayenera kulowa usilikali. Koma nkhani imeneyi sinatuluke m’magazini yachijeremani.