Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 KALE LATHU

“Tinalimbikitsidwa Kukonda Kwambiri Yehova Ndiponso Kulalikira Mwakhama”

“Tinalimbikitsidwa Kukonda Kwambiri Yehova Ndiponso Kulalikira Mwakhama”

LACHISANU m’mawa, pa 8 September 1922, anthu 8,000 anasonkhana muholo inayake ndipo munkatentha kwambiri. Tcheyamani analengeza kuti nkhani imene ikambidwe ndi yofunika kwambiri moti munthu amene angatuluke muholoyo sadzaloledwa kulowanso.

Anthu ataimba nyimbo, Joseph F. Rutherford anapita pamalo okambira nkhani. Aliyense ankayembekezera mwachidwi nkhani yake. Koma panali anthu ochepa amene ankalephera kukhala pansi chifukwa cha kutentha. M’bale Rutherford anawapempha kuti akhale pansi n’kumamvetsera. Pamene ankayamba kukamba nkhani, anthu ambiri sanaone kuti panali nsalu yopinda imene inapachikidwa m’mwamba.

Mutu wa nkhani ya M’bale Rutherford unali wakuti “Ufumu Wakumwamba Wayandikira.” Iye analankhula mwamphamvu kwa ola ndi hafu ndipo anafotokoza mmene aneneri akale ankalengezera mopanda mantha kubwera kwa Ufumu. Nkhaniyi itafika pachimake, anafunsa anthu kuti: “Kodi mukukhulupirira kuti Mfumu yaulemerero yayamba kulamulira?” Anthu onse anayankha mokweza kuti: “Inde.”

Kenako M’bale Rutherford ananena mofuula kuti: “Choncho bwererani kumunda, inu ana nonse a Mulungu wam’mwambamwamba. Onani, Mfumu yayamba kulamulira ndipo inu ndinu atumiki ake olengeza za Ufumuwo. Choncho lengezani, lengezani, lengezani.”

Pa nthawiyi, nsalu ija inatambasulidwa ndipo panaoneka mawu oti, “Lengezani za Mfumu ndi Ufumu Wake.”

M’bale Ray Bopp anati: “Anthufe tinadabwa kwambiri.” Mlongo wina dzina lake Anna Gardner ananena kuti: “Anthu ankaomba m’manja kwambiri moti matabwa a denga anagwedezeka.” M’bale Fred Twarosh ananenanso kuti: “Anthu onse anaimirira.” Ndipo M’bale Evangelos Scouffas anati: “Zinali ngati tinadzutsidwa ndi mphamvu inayake ndipo tinaima m’maso mukulengeza misozi.”

Anthu ambiri pamsonkhanowo anali atayamba kale kulalikira za Ufumu. Koma atamva nkhaniyo analimbikitsidwa kuti ayambe kugwira ntchitoyi mwakhama kwambiri. Mlongo Ethel Bennecoff ananena kuti Ophunzira Baibulofe “tinalimbikitsidwa kukonda kwambiri Yehova ndiponso kulalikira mwakhama.” Mlongo Odessa Tuck, yemwe pa nthawiyo anali ndi zaka 18, anachoka pamsonkhanowo ali wofunitsitsa kudzipereka. Iye ankafuna kuchita mofanana ndi Yesaya pamene Mulungu anafunsa kuti, “Ndani apite m’malo mwa ife?” Mlongoyu anati: “Sindinadziwe kumene ndipite, mmene ndipitire kapena zimene ndikachite. Koma chomwe ndinkafuna ndi kunena kuti, ‘Ine ndilipo! Nditumizeni.’” (Yes. 6:8) M’bale Ralph Leffler ananena kuti: “Tinganene kuti pa tsiku losaiwalikali m’pamene panayambira ntchito yolengeza Ufumu padziko lonse.”

Zimene zinachitikazi n’zimene zinachititsa kuti msonkhano wa mu 1922 umene unachitika ku Cedar  Point ku Ohio ukhale wosaiwalika m’mbiri ya Mboni za Yehova. M’bale George Gangas anati: “Msonkhanowu unandithandiza kuona kufunika kopezeka pamisonkhano yonse ikuluikulu.” Ndipo n’kutheka kuti kuyambira nthawi imeneyo sanajombenso msonkhano uliwonse. Mlongo Julia Wilcox analemba kuti: “N’zovuta kufotokoza mmene ndimamvera nthawi iliyonse imene mabuku athu amatchula za msonkhano wa mu 1922 wa ku Cedar Point. Nthawi zonse ndimafuna kunena kuti, ‘Zikomo kwambiri Yehova chifukwa chondilola kupezeka pamsonkhanowu.’”

Mwina nafenso timakumbukira msonkhano wina umene unatilimbikitsa kwambiri. N’kutheka kuti unatithandiza kuyamba kulalikira mwakhama komanso kukonda kwambiri Mulungu ndiponso Mfumu yake. Tikaganizira msonkhano ngati umenewu, nafenso timafuna kunena kuti, “Zikomo kwambiri Yehova chifukwa chondilola kupezeka pamsonkhanowu.”