NSANJA YA OLONDA July 2015 | N’chiyani Chingatithandize Tikakhala Ndi Nkhawa

Anthu ambiri amakumana ndi mavuto komanso zinthu zodetsa nkhawa, koma ena sakhala ndi nkhawa kwambiri. N’chiyani chimawathandiza?

NKHANI YAPACHIKUTO

Zinthu Zodetsa Nkhawa Zimachitika Kulikonse

Anthu atulukira kuti ngakhale kuda nkhawa pang’ono kumachititsa kuti munthu afe msanga. N’chiyani chingakuthandizeni kuti musamade nkhawa kwambiri?

NKHANI YAPACHIKUTO

Kuda Nkhawa Chifukwa cha Kusowa kwa Ndalama

Bambo wina anakwanitsa kusamalira banja lake ngakhale pamene mitengo ya zinthu inali itakwera kwambiri.

NKHANI YAPACHIKUTO

Kuda Nkhawa Chifukwa cha Mavuto a M’banja

Nkhani ya mkazi amene mwamuna wake anamusiya ukwati, zimene zinamuthandiza, komanso zimene kukhala ndi chikhulupiriro kumatanthauza.

NKHANI YAPACHIKUTO

Kuda Nkhawa Chifukwa cha Zinthu Zoopsa

N’chiyani chingatithandize ngati tili ndi nkhawa chifukwa cha nkhondo, kusamvera malamulo kwa anthu, kuwonongeka kwa chilengedwe, kusintha kwa nyengo komanso matenda?

BAIBULO LIMASINTHA ANTHU

Moyo Wanga Unkangoipiraipirabe

Stephen McDowell anali wachiwawa, koma anthu ena atapha munthu, zinapangitsa kuti asinthe moyo wake.

Kodi Anthufe Tingasangalatsedi Mulungu?

Tingapeze yankho tikaganizira zimene zinachitikira Yobu, Loti, ndi Davide, omwe analakwitsapo zinthu zazikulu.

Kodi Mukudziwa?

Kodi mphero ankazigwiritsa ntchito bwanji kale? Kodi mawu akuti “pachifuwa” amatanthauza chiyani?

Kuyankha Mafunso a M’Baibulo

Kodi anthu adzasiya kuchita zoipa?

Zina zimene zili pawebusaiti

Kodi Mulungu Angandithandize Ndikapemphera?

Kodi Mulungu zimam’khudza tikamavutika?