Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YA PACHIKUTO | N’CHIYANI CHINGATITHANDIZE TIKAKHALA NDI NKHAWA?

Kuda Nkhawa Chifukwa cha Kusowa kwa Ndalama

Kuda Nkhawa Chifukwa cha Kusowa kwa Ndalama

Paul, yemwe ali ndi ana awiri ananena kuti: “Mavuto a zachuma atakula m’dziko lathu, zakudya zinayamba kudula komanso zinkasowa. Tinkadikirira pamzere kwa maola ambiri koma nthawi zambiri chakudyacho chinkatha tisanagule n’komwe. Anthu anaonda kwambiri moti ena ankakomoka ndi njala. Mitengo ya zinthu inakwera kufika mamiliyoni kenako mabiliyoni ndipo pamapeto pake ndalama ya dziko lathu inatheratu mphamvu. Ndalama zanga zonse zakubanki, za inshuwalansi komanso za penshoni zinalibenso ntchito.”

Paul

Paul ankadziwa kuti kugwiritsa ntchito “nzeru zopindulitsa” ndi kumene kungamuthandize kuti akwanitse kusamalira banja lake. (Miyambo 3:21) Iye ananena kuti: “Ndinkagwira ntchito ya zamagetsi, koma zinthu zitavuta ndinkalolera kugwira ntchito iliyonse ngakhale yamalipiro ochepa. Anthu ena ankandipatsa zakudya kapena katundu monga malipiro anga. Akandipatsa sopo 4, ndinkagwiritsa ntchito muwiri winayo n’kugulitsa. Patapita nthawi, ndinagula tianapiye 40. Nkhukuzi zitakula, ndinagulitsa n’kugula anapiye ena 300. Kenako ndinasinthanitsa nkhuku 50 ndi matumba a ufa awiri olemera 50kg. Ufawu unali wokwanira kudyetsa banja langa ndi mabanja enanso kwa nthawi yaitali ndithu.”

Paul ankadziwanso kuti kudalira Mulungu ndi kothandiza kwambiri. Tikamamvera Mulungu, iye amatithandiza. Pa nkhani yokhudza kupeza zinthu zofunika pamoyo, Yesu anati: “Siyani kuvutika mumtima . . . Atate wanu amadziwa kuti zinthu zonsezi n’zofunika kwa inu.”—Luka 12:29-31.

N’zomvetsa chisoni kuti Satana, yemwe ndi mdani wamkulu wa Mulungu, amapusitsa anthu kuti aziika maganizo awo onse pa zofuna za moyo. Anthu amada nkhawa kwambiri ndi zinthu zimene zikuwachitikira ndiponso zimene sizingachitike n’komwe. Ndipo amavutika kufunafuna zinthu zomwe ndi zosafunika pamoyo wawo. Izi zimachititsa kuti anthu ambiri azingotenga ngongole ndipo pamapeto pake amakhala ndi nkhawa, chifukwa Baibulo limati: “Wobwereka amakhala kapolo wa wobwereketsayo.”—Miyambo 22:7.

Anthu ena amachita zinthu asanaganize bwino ndipo pamapeto pake amanong’oneza bondo. Paul anafotokoza kuti: “Anthu ambiri amene tinayandikana nawo anasiya mabanja ndi anzawo kuti akasakesake chuma kumaiko akunja. Ena anapita opanda mapepala owavomereza kukhala m’dziko lina ndipo izi zinachititsa kuti asalembedwe ntchito. Nthawi zambiri ankangokhalira kuthawa apolisi komanso ankagona m’misewu. Zonsezi zinawachitikira chifukwa chosakhulupirira kuti Mulungu awathandiza. Koma ine ndi banja langa tinaona kuti ndi bwino kukhalabe limodzi ndi kudalira Mulungu kuti atithandize pa nthawi ya mavuto a zachumayi.”

MUZITSATIRA MALANGIZO A YESU

Paul anapitiriza kuti: “Yesu ananena kuti: ‘Musamade nkhawa za tsiku lotsatira, chifukwa tsiku lotsatira lidzakhala ndi zodetsa nkhawa zakenso. Zoipa za tsiku lililonse n’zokwanira pa tsikulo.’ Potsatira malangizo amenewa, ndinkangopempha Mulungu kuti, ‘mutipatse ife lero chakudya chathu chalero’ kuti tikhale ndi moyo. Mulungu ankatithandizadi kupeza chakudya monga mmene Yesu analonjezera. Nthawi zambiri sitinkapeza zakudya za kumtima kwathu. Ndikukumbukira kuti tsiku lina nditapita kokagula chakudya, ndinakhala pamzere ndisakudziwa n’komwe kuti akugulitsa chakudya chanji. Nditafika kutsogolo, ndinangoona kuti akugulitsa yogati yekhayekha. Sindikonda yogati koma ndinagulabe popeza chinali chakudya, moti tsiku limenelo tinagonera yogatiyo. Ndikuthokoza Mulungu kuti kwa nthawi yonseyi, ine ndi banja langa sitinagonepo ndi njala.” *

Mulungu walonjeza kuti: “Sindidzakusiyani kapena kukutayani ngakhale pang’ono.”—Aheberi 13:5

“Panopa zinthu zayamba kutiyendera bwino. Koma pa nthawi yonse imene tinali ndi vuto la ndalama, taphunzira kuti kudalira Mulungu ndi kofunika kuti munthu usamade nkhawa kwambiri. Tikamachita zimene Yehova * amafuna, iye nthawi zonse amatithandiza. Taona kuti lemba la Salimo 34:8 limanenadi zoona. Lembali limati: ‘Talawani ndipo muona kuti Yehova ndi wabwino. Wodala ndi munthu wamphamvu amene amathawira kwa iye.’ Sitida nkhawa kuti tidzatani tikadzakumananso ndi vuto la kusowa kwa ndalama.

Mulungu amathandiza atumiki ake okhulupirika kupeza chakudya cha tsiku lililonse

“Tazindikira kuti anthufe timafunikira chakudya kuti tikhale ndi moyo osati ntchito kapena ndalama. Mulungu analonjeza kuti: ‘Padziko lapansi padzakhala tirigu wambiri.’ Tidzasangalala kwambiri lonjezo limeneli likadzakwaniritsidwa. Koma panopa tikakhala ‘ndi chakudya, zovala ndi pogona, timakhala okhutira ndi zinthu zimenezi.’ Timalimbikitsidwanso ndi mawu a m’Baibulo akuti: ‘Moyo wanu ukhale wosakonda ndalama, koma mukhale okhutira ndi zimene muli nazo pa nthawiyo. Pakuti Mulungu anati: “Sindidzakusiyani kapena kukutayani ngakhale pang’ono.” Moti tikhale olimba mtima ndithu ndipo tinene kuti: “Yehova ndiye mthandizi wanga. Sindidzaopa.”’” *

Kuti ‘tiyende ndi Mulungu’ ngati mmene Paul ndi banja lake anachitira, tifunika kukhala ndi chikhulupiriro cholimba. (Genesis 6:9) Kaya panopa tikuda nkhawa chifukwa cha vuto la kusowa kwa ndalama, kapena ngati m’tsogolo titadzakumana ndi vutoli, chikhulupiriro komanso nzeru zimene Paul anasonyeza, zingatiphunzitse zinthu zofunika kwambiri.

Kodi tingatani ngati tikuda nkhawa chifukwa cha mavuto a m’banja?

^ ndime 10 Baibulo limati dzina la Mulungu ndi Yehova.