Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YA PACHIKUTO | N’CHIYANI CHINGATITHANDIZE TIKAKHALA NDI NKHAWA?

Zinthu Zodetsa Nkhawa Zimachitika Kulikonse

Zinthu Zodetsa Nkhawa Zimachitika Kulikonse

“Nditapita kukagula zakudya, ndinangopeza mabisiketi okhaokha ndipo mtengo wake unali utawonjezereka maulendo 10,000. Nditapitanso tsiku lotsatira, ndinapeza kuti m’masitolo onse munalibiretu zakudya.”—Paul, Zimbabwe.

“Tsiku lina amuna anga anangondiuza kuti akufuna kundisiya. Zimenezi zinandidetsa nkhawa kwambiri ndipo ndinadzifunsa kuti, Ndingapirire bwanji nkhanza zimenezi? Nanga ana angawa ziwathera bwanji?”—Janet, United States.

“Nditangomva kulira kwa masayilini, ndinathawa n’kugona pansi msangamsanga. Apa n’kuti ndege zikuphulitsa mabomba. Panapita maola angapo, koma ndinkanjenjemerabe ndi mantha.”—Alona, Israel.

Masiku ano zinthu zodetsa nkhawa ndi zambiri chifukwa tikukhala mu “nthawi yapadera komanso yovuta.” (2 Timoteyo 3:1) Anthu ambiri akuvutika chifukwa chosowa ndalama, kutha kwa banja, nkhondo, matenda oopsa ndiponso ngozi zoyambitsidwa ndi anthu kapenanso zochitika mwadzidzidzi. Komatu si zokhazi, ena akatuluka chotupa amakhala ndi nkhawa chifukwa amaganiza kuti ndi khansa. Anthu enanso amakhala ndi nkhawa kuti zidzukulu zawo zikamadzakula, dzikoli lidzakhala litaipa kwambiri.

Nthawi zina kuda nkhawa sikumakhala kolakwika. Mwachibadwa munthu amada nkhawa akamakonzekera kulemba mayeso, kuchita zinazake, ndiponso kufunsidwa mafunso pofuna kulowa ntchito. Nkhawa imatithandizanso kuti tisachite zinthu zoipa. Koma si bwino kumangokhala ndi nkhawa nthawi zonse ndiponso mopitirira malire. Zotsatira za kafukufuku wokhudza anthu opitirira 68,000 yemwe anachitika posachedwapa zinasonyeza kuti kuda nkhawa ngakhale pang’ono pokha kumachititsa kuti munthu afe msanga. Mpake kuti Yesu anafunsa kuti: “Ndani wa inu amene angatalikitse moyo wake pang’ono pokha mwa kuda nkhawa?” Uwu ndi umboni wakuti nkhawa sitalikitsa moyo wa munthu. N’chifukwa chake Yesu ananena kuti: “Lekani kudera nkhawa.” (Mateyu 6:25, 27) Koma kodi n’chiyani chingathandize munthu kuti asamade nkhawa kwambiri?

Chofunika ndi kugwiritsa ntchito malangizo anzeru, kukhala ndi chikhulupiriro cholimba mwa Mulungu ndiponso kukhulupirira ndi mtima wonse kuti m’tsogolo zinthu zidzakhala bwino. Tizikumbukira kuti ngakhale kuti panopa sitikukumana ndi zinthu zodetsa nkhawa kwambiri, tingadzakumane nazo m’tsogolo. Ndiye tiyeni tione mmene mfundozi zinathandizira Paul, Janet, ndi Alona pa nthawi imene anakumana ndi mavuto odetsa nkhawa.