Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YA PACHIKUTO | KODI PALI AMENE ANGAKHAZIKITSE BOMA LOPANDA CHINYENGO?

M’mayiko Ambiri Mukuchitika Zachinyengo

M’mayiko Ambiri Mukuchitika Zachinyengo

M’mayiko ambiri akuluakulu a boma amachita ziphuphu komanso zachinyengo zina. Ziphuphu ndi kugwiritsa ntchito mphamvu molakwika n’cholinga chofuna kupeza kenakake. Komatu zimenezi sizinayambe lero. Mwachitsanzo, m’Baibulo muli lamulo loletsa kulandira ziphuphu poweruza milandu. Izi zikusonyeza kuti ziphuphu zinkachitika, ngakhale zaka 3,500 zapitazo. (Ekisodo 23:8) Komatu ziphuphu ndi chitsanzo chimodzi chabe cha zinthu zachinyengo zomwe zimachitika m’boma. Nthawi zina akuluakulu a boma amaba katundu komanso ndalama zaboma. Amagwiritsanso ntchito udindo wawo molakwika kapenanso kukondera achibale ndi anzawo n’kupotoza dala chilungamo.

Ngakhale kuti zachinyengo zingathe kuchitika paliponse pamene pali anthu, zikuoneka kuti chinyengo chochitika m’boma ndiye chofala kwambiri. M’chaka cha 2013, bungwe lina loona za katangale, linatchula magulu 5 amene anthu amaona kuti ndi omwe amachita kwambiri zachinyengo padziko lonse. Linati magulu ake ndi azipani, apolisi, akuluakulu a boma, opanga malamulo komanso oweruza milandu. Tiyeni tione zitsanzo zingapo zomwe zikusonyeza kuti vutoli lilipodi.

  • AFRICA: M’chaka cha 2013, akuluakulu a boma okwana 22,000 ku South Africa anaimbidwa mlandu chifukwa chochita zachinyengo.

  • SOUTH AMERICA: Mu 2012, ku Brazil, andale 25 anaimbidwa mlandu chifukwa chogwiritsa ntchito ndalama za boma pokopa anthu kuti awavotere. Mmodzi mwa anthuwa ndi yemwe anali wachiwiri kwa pulezidenti wa dzikolo.

  • ASIA: Mu 1995 anthu 502 anafa mumzinda wa Seoul ku South Korea, nyumba ina itagwa. Kafukufuku anasonyeza kuti akuluakulu a boma analandira ziphuphu kuchokera ku kampani yomwe inamanga nyumbayi. Kampaniyo inagwiritsa ntchito zipangizo zosalimba komanso inamanga nyumbayo mosatsatira malamulo opewera ngozi.

  • EUROPE: Mayi wina wogwira ntchito m’bungwe lina loona za mayiko a ku Europe, dzina lake Cecilia Malmström, anati: “Chinyengo chafika poipa kwambiri. Koma zikuoneka kuti palibe chomwe andale akuchita poonetsetsa kuti chitheretu.”

Anthu sangathe kuthetsa zachinyengo zomwe zimachitika m’boma. Pulofesa Susan Rose-Ackerman, yemwe ndi katswiri woona za katangale, anati: “Chinyengo sichingathe pokhapokha ngati boma litasintha mmene limachitira zinthu.” Ngakhale kuti ambiri angaone kuti n’zosatheka kuti chinyengo chithe m’dzikoli, Baibulo limanena kuti chinyengo chidzatha.